Kodi Ndinu Wokonzeka ‘Kudzalandila Dziko Lapansi’?
TONSEFE timayembekezela mwacidwi kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.” (Mat. 5:5) Odzozedwa adzalandila dziko lapansi mwa kulamulila monga mafumu kumwamba pamodzi na Yesu. (Chiv. 5:10; 20:6) Koma Akhristu ambili oona akuyembekezela kudzakhala kwamuyaya padziko lapansi. Iwo adzakhala angwilo, acimwemwe, komanso adzakhala mwamtendele. Kuti izi zikatheke, pali nchito zina zimene adzafunika kudzagwila. Mwacitsanzo, ganizilani nchito zitatu izi: nchito yodzakonza dziko lapansi kukhala paradaiso, kulandila m’nyumba zawo amene adzaukitsidwe, komanso kuwaphunzitsa. Tsopano, ganizilani zimene mungacite palipano poonetsa kuti ndinu wofunitsitsa kukagwilako nchitozo.
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZAKONZA NAWO DZIKO LAPANSI KUKHALA PARADAISO?
Pamene Yehova analamula anthu kuti ‘mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile,’ iye anaonetsa kuti pothela pake dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. (Gen. 1:28) Anthu amene adzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi adzafunika kumvela lamulo limeneli. Sikuti iwo adzangofikila kufutukula paradaiso ayi, cifukwa tsopano munda wa Edeni kulibe. Aramagedo ikadzangotha, tidzakhala na nchito yambili yokonza malo owonongeka. Imeneyi idzakhaladi nchito yaikulu!
Izi zitikumbutsa nchito imene Aisiraeli anagwila atabwelako ku Babulo. Dziko lawo linakhala matongwe kwa zaka 70. Koma Yesaya anali atalosela kuti na thandizo la Yehova, iwo adzalikonzanso dzikolo. Ulosiwo unati: “Adzacititsa cipululu cake kukhala ngati Edeni ndi dela lake lacipululu kukhala ngati munda wa Yehova.” (Yes. 51:3) Aisiraeli analikonzadi dziko lawo. Mofananamo, na thandizo la Yehova, aja amene adzalandila dziko lapansi adzakwanitsa kulikonza kuti likhale paradaiso wokongola. Ndipo mungaonetse palipano kuti mukufunitsitsa kudzagwila nawo nchitoyi.
Njila imodzi mungacitile izi ni kuonetsetsa kuti pakhomo panu ni paukhondo, komanso zinthu zimaikidwa mwadongosolo. Mungacite zimenezi ngakhale kuti anthu oyandikana nawo nyumba si aukhondo. Cina, mungamadzipeleke kuti muziyeletsa nawo Nyumba ya Ufumu kapena Bwalo la Misonkhano. Ngati mikhalidwe yanu ilola, mungasaine fomu yofunsila kuti muzithandiza pa nchito yopeleka thandizo pakacitika tsoka. Mwa kutelo, mudzaonetsa kuti ndinu wokonzeka kudzathandiza ngati tsoka lingacitike. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ningaphunzileko maluso ati amene ningakawagwilitse nchito m’dziko latsopano ngati naloledwa kukapezekamo?’
KODI NDINU WOKONZEKA KUKAWALANDILA M’NYUMBA ZANU OUKITSIDWA?
Yesu atangoukitsa mwana wa Yairo, ananena kuti mwanayo anafunikila kupatsidwa cakudya. (Maliko 5:42, 43) Cioneka siinali nchito yovuta kupezela cakudya kamtsikana ka zaka 12 kameneko. Koma ganizilani kukula kwa nchito idzakhalapo Yesu akadzakwanilitsa lonjezo lake lakuti “onse ali m’manda acikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Ngakhale kuti Baibo siifotokoza zambili, n’kutheka kuti amene adzaukitsidwa adzafunika kuwathandiza kupeza cadya, pogona, komanso zovala. Kodi mungaonetse bwanji palipano kuti ndinu wokonzeka kudzawathandiza? Ganizilani mafunso awa:
Mungacite ciyani palipano poonetsa kuti ndinu wokonzeka kudzalandila dziko lapansi?
Akalengeza kuti woyang’anila dela adzacezela mpingo wanu, kodi mumadzipeleka kuti adzadye cakudya ku nyumba kwanu? Atumiki a nthawi zonse apadela akatumizidwa m’munda kucoka pa Beteli, kapena woyang’anila dela utumiki wake ukatha, kodi mungawathandize kupeza malo okhala? Ngati m’dela lanu mudzacitika msonkhano wacigawo kapena wapadela, kodi mungadzipeleke kukagwilako nchito msonkhanowo usanayambe kapena pambuyo pake, kapena kudzipeleka kuti mukalandile alendo ocokela kwina?
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZAPHUNZITSA OMWE ADZAUKITSIDWE?
Malinga na Machitidwe 24:15, timayembekezela kuti mabiliyoni a anthu adzaukitsidwa. Ambili adzakhala aja oti asanamwalile analibe mwayi wom’dziŵa Yehova. Koma akadzaukitsidwa, iwo adzakhala na mwayi umenewo. a Atumiki a Mulungu okhulupilika komanso aluso adzatengako mbali pa nchitoyo. (Yes. 11:9) Mlongo Charlotte, amene analalikilapo ku Europe, South America, komanso ku Africa, akuyembekezela nchitoyo mwacidwi. Mwacimwemwe iye anati: “Niyembekezela kukaphunzitsa anthu amene adzaukitsidwa. Nthawi zambili nikamaŵelenga za anthu amene anakhalako kumbuyoku, mumtima nimati, ‘Munthuyu akanakhala kuti anali kum’dziŵa Yehova, umoyo wake ukanakhala wabwino kwambili.’ Nifunitsitsa kukawafotokozela za umoyo wabwino umene anauphonya.”
Ngakhale atumiki a Yehova okhulupilika amene anakhalako Yesu asanabwele padziko lapansi, adzafunika kuphunzila zambili. Ganizilani cimwemwe komanso mwayi wapadela umene tidzakhala nawo, kufotokozela Danieli kukwanilitsika kwa maulosi amene analemba koma amene iye sanawamvetse. (Dan. 12:8) Kapena kuthandiza Rute na Naomi kudziŵa kuti banja lawo linali mu mzele wobadwila Mesiya. Ha! Zidzakhala zosangalatsa cotani nanga kugwilako nchito ya padziko lonse yophunzitsa anthu imeneyo. Panthawiyo sikudzakhala zovuta kapena zosokoneza zilizonse zimene zili m’dziko loipali masiku ano.
Kodi mungaonetse bwanji palipano kuti ndinu wokonzeka kukagwilako nchito imeneyo? Njila imodzi ni kuyesetsa kunola maluso athu a kuphunzitsa, na kutengako mbali nthawi zonse pa nchito ya padziko lonse yolalikila. (Mat. 24:14) Ngakhale kuti palipano simungacite zambili cifukwa ca msinkhu wanu kapena pa zifukwa zina, kuyesetsa kwanu kudzaonetsa kuti ndinu wokonzeka kukaphunzitsa anthu amene adzaukitsidwa.
Koma mafunso ofunika kwambili ni akuti, Kodi mukufunitsitsadi kudzalandila dziko lapansi? Kodi mukuyembekezela mwacidwi kudzakonza dzikolo, kudzalandila odzaukitsidwa, na kuwaphunzitsa? Mungaonetse kuti ndinu wokonzeka, mwa kuseŵenzetsa mipata imene mungakhale nayo palipano, kuti muzigwilako nchito zofanana ndi zimene mudzagwila mukadzalandila dziko lapansi!
a Onani nkhani yakuti ‘Kuthandiza Anthu Ambili Kukhala Olungama,’ mu Nsanja ya Mlonda ya September 2022.