Kodi Ndinu Wanchito Mnzake Wabwino?
“INE ndinali pambali pake monga mmisili waluso. . . . Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miy. 8:30) Umu ni mmene Baibo imafotokozela Mwana wa Mulungu, pamene anali kugwila nchito na Atate wake zaka zosaŵelengeka asanabwele padziko lapansi. Onani kuti vesili limatiuzanso mmene Yesu anamvelela monga wanchito mnzake wa Mulungu. Iye anali “wosangalala” pamaso pake.
Pamene Yesu anali kumwamba, anaphunzila makhalidwe abwino amene anamuthandiza kukhala wanchito mnzake wabwino. Atabwela padziko lapansi, iye anakhala citsanzo cabwino koposa poseŵenza na ena. Kodi tingapindule bwanji na citsanzo cake? Tikapenda citsanzo cake, tipeza mfundo zitatu zimene zingatithandize kuseŵenza bwino na ŵena. Mfundozo zidzatithandiza kulimbitsa mgwilizano pakati pathu.
MFUNDO YOYAMBA: MUZIONETSA ULEMU KWA ENA
Wanchito wabwino amaona anchito anzake kukhala ofunika, ndipo amapewa kudzionetsela. Yesu anaphunzila kudzicepetsa kotelo kwa Atate wake. Olo kuti ni Yehova yekha woyenelela kuchedwa Mlengi, iye anafuna kuti ena adziŵe udindo umene Mwana wake anali nawo monga wanchito mnzake. Timadziŵa zimenezi pa mawu amene Mulungu anakamba akuti: “Tiyeni tipange munthu m’cifanizilo cathu.” (Gen. 1:26) Yesu anayamikila kudzicepetsa kwa Yehova kumeneku.—Sal. 18:35.
Yesu ali padziko lapansi anaonetsa khalidwe la kudzicepetsa. Pamene anthu anali kum’tamanda pa zinchito zake, iye anapeleka citamandoco kwa Mulungu. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 7:15, 16) Yesu anali kukhala mwamtendele na ophunzila ake, ndipo anawacha mabwenzi osati akapolo. (Yoh. 15:15) Iye anafika ngakhale posambitsa mapazi awo kuti awaphunzitse khalidwe la kudzicepetsa. (Yoh. 13:5, 12-14) Mofananamo, ifenso tiyenela kulemekeza anchito anzathu na kuika zofuna zawo patsogolo pa zofuna zathu. Tikamaonetsana ulemu wina na mnzake, na kupewa kudzifunila ulemelelo, tingacite zambili potumikila Mulungu.—Aroma 12:10.
Cina, munthu wodzicepetsa amazindikila kuti “aphungu akaculuka [zolingalila] zimakwanilitsidwa.” (Miy. 15:22) Kaya tikhale na cidziŵitso coculuka bwanji, kapena maluso oculuka motani, tizikumbukila kuti palibe munthu adziŵa zonse. Ngakhale Yesu anavomeleza kuti panali zina zimene sanali kuzidziŵa. (Mat. 24:36) Cidwi cake cinali pa kufuna kudziŵa maganizo a ophunzila ake opanda ungwilo. (Mat. 16:13-16) Ndiye cifukwa cake, anchito anzake anali kumasuka kukhala naye. Mofananamo, tikakhala odzicepetsa na kukumbukila kuti sitidziŵa zonse, komanso kumvetsela maganizo a ŵena, tidzalimbikitsa mgwilizano pakati pathu, ndipo capamodzi tidzakwanilitsa colinga cathu.
N’kofunika kwambili maka-maka kwa akulu kutengela citsanzo ca Yesu akamaseŵenzela pamodzi. Iwo ayenela kukumbukila kuti mzimu woyela, ungapangitse mkulu aliyense pa bungwe lawo kutulutsa mfundo yothandiza. Akamacita mamiting’i yawo, mkulu aliyense ayenela kupangitsa mkulu mnzake kukhala womasuka kupelekapo ndemanga. Akatelo, adzapanga zigamulo zopindulila mpingo wonse.
MFUNDO YACIŴILI: “ANTHU ONSE ADZIŴE KUTI NDINU OLOLELA”
Wanchito wabwino amakhala wololela pocita zinthu na anchito anzake. Iye amakhala wokonzeka kusintha. Yesu anali na mipata yambili yoona Atate wake akuonetsa khalidwe la kulolela. Mwacitsanzo, Yehova anamutuma kukawombola mtundu wa anthu ku cilango ca imfa cimene analandila.—Yoh. 3:16.
Yesu anali kulolela pakafunika kutelo. Kumbukilani mmene anathandizila mayi wa ku Foinike, ngakhale kuti iye anatumidwa kwa a nyumba ya Isiraeli. (Mat. 15:22-28) Iye analinso wololela kwa ophunzila ake. Mwacitsanzo, bwenzi lake lapamtima Petulo atamukana pamaso pa anthu, Yesu anamukhululukila. Pambuyo pake, iye anapatsa Petulo maudindo aakulu. (Luka 22:32; Yoh. 21:17; Mac. 2:14; 8:14-17; 10:44, 45) Citsanzo ca Yesu citiphunzitsa kuti tiyenela kukhala ololela kwa anthu onse.—Afil. 4:5.
Kukhala ololela kudzatithandizanso kukhala okonzeka kusintha, kuti tizigwila nchito mwamtendele na anthu osiyana-siyana. Yesu anali kukhala bwino na anthu moti adani ake ansanje anamuimba mlandu wakuti ni “bwenzi la okhometsa msonkho ndi ocimwa,” anthu amene anamvetsela uthenga wake. (Mat. 11:19) Mofanana na Yesu, nafenso tiyenela kugwila nchito mwamtendele na anthu osiyana-siyana. M’bale Louis, amene anatumikilako m’dela kwa nthawi yaitali komanso pa Beteli, pamodzi na anthu azikhalidwe zosiyana-siyana, anati: “Kuseŵenza pamodzi na ŵanthu azikhalidwe zosiyana-siyana kuli ngati kumanga mpanda pogwilitsa nchito miyala, imene imakhala ya masaizi osiyana-siyana. Mwa ici, womangayo amafunikila khama lokwanitsa kuyala bwino miyalayo kuti mpandawo ukatuluke woongoka bwino-bwino. Inenso nayesetsa kupanga masinthidwe pofuna kuthandizila kuti ‘mpandawo’ uwongoke bwino-bwino, titelo kunena kwake.” Umenewu ni mzimu wabwino ngako!
Wanchito mnzake wabwino sabisila anzake mfundo zothandiza, pofuna kukhalabe na ulamulilo pa iwo
Kodi tingaonetse bwanji khalidwe la kulolela mu mpingo mwathu? Tili na mwayi woonetsa kulolela m’kagulu kathu ka ulaliki. Mwina angatigaŵe na wofalitsa amene ali na maudindo ambili m’banja kuposa ife, kapena wosiyana nafe msinkhu. Tingaonetse kulolela mwa kusinthako mmene timacitila ulaliki wathu kuti tiwathandize kusangalala kwambili na ulaliki.
MFUNDO YACITATU: KHALANI “OKONZEKA KUGAŴILA ENA”
Wanchito mnzake wabwino amakhala ‘wokonzeka kugaŵila ena.’ (1 Tim. 6:18) Pogwila nchito na Atate wake, Yesu ayenela kuti anaona kuti Yehova sanam’bise kalikonse. Pamene Yehova anali “kukonza kumwamba,” Yesu anali “pomwepo,” ndipo anaphunzila kwa iye. (Miy. 8:27) Patapita nthawi, Yesu anagaŵila ophunzila ake “zimene [anamva]” kwa Atate wake. (Yoh. 15:15) Nafenso tiyenela kutengela citsanzo ca Yehova, mwa kugaŵilako anchito anzathu maluso na cidziŵitso cimene tili naco. Zoonadi, wanchito mnzake wabwino sabisila anzake mfundo zothandiza zimene ena afunika kudziŵa, pofuna kukhalabe na ulamulilo pa iwo. Iye amasangalala kuuzako ena zinthu zabwino zimene amaphunzila.
Cina, tingauzeko anchito anzathu mawu a cilimbikitso. Kodi sitimakondwela wina akaona zabwino zimene tam’citila kapena akatiyamikila? Yesu anali kuuza anchito anzake zabwino zimene anaona mwa iwo. (Yelekezelani na Mateyu 25:19-23; Luka 10:17-20) Iye anafika powauza kuti iwo adzacita “nchito zazikulu kuposa” iye. (Yoh. 14:12) Usiku wakuti maŵa aphedwa, iye analamula atumwi ake okhulupilika kuti: “Inu mwakhalabe ndi ine m’mayeselo anga.” (Luka 22:28) Tangoganizilani mmene mawu amenewa anawalimbikitsila kucita zambili! Ngati nafenso timayamikila anchito anzathu, iwo adzakondwela kwambili, komanso adzalimbikitsidwa kucita zambili.
MUNGAKHALE WANCHITO MNZAKE WABWINO
M’bale wina dzina lake Kayode anati: “Wanchito mnzake wabwino safunika kucita kukhala wangwilo, koma amapangitsa ena kukhala osangalala kuti nchito ikhale yosavuta kuigwila.” Kodi ndinu wanchito wotelo? Bwanji osafunsa anchito anzanu kuti akuuzeni mtundu wa munthu amene muli. Ngati iwo amasangalala kutumikila nanu, monga zinali kwa ophunzila a Yesu, mungakambe monga mtumwi Paulo kuti: “Ndife anchito anzanu kuti mukhale ndi cimwemwe.”—2 Akor. 1:24.