Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Kuika Maganizo Athu pa Zinthu za Mzimu Kumabweletsa Moyo na Mtendele’

‘Kuika Maganizo Athu pa Zinthu za Mzimu Kumabweletsa Moyo na Mtendele’

“Otsatila za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.”—AROMA 8:5.

NYIMBO: 45, 36

1, 2. N’cifukwa ciani Aroma caputa 8 ni yofunika ngako kwa Akhiristu odzozedwa?

PONENA za Cikumbutso ca imfa ya Yesu cimene timacita caka ciliconse, kodi munaŵelengako Aroma 8:15-17? N’kutheka kuti munaŵelengako. Lemba limeneli lifotokoza mmene Akhiristu amadziŵila kuti ni odzozedwa. Limati mzimu woyela umacitila umboni pamodzi na mzimu wawo. Ndipo vesi yoyamba m’caputa imeneyo imakamba za “amene ali ogwilizana ndi Khiristu Yesu.” Koma kodi Aroma caputa 8 imakamba cabe za odzozedwa, kapena imakhudzanso Akhiristu oyembekezela kudzakhala padziko lapansi?

2 Kweni-kweni, caputa imeneyo imakamba za odzozedwa. Iwo amalandila “mzimu” monga amene ‘akudikila . . . kuti atengedwe kukhala ana a Mulungu, . . . kuti atuluke m’matupi [awo a nyama].’ (Aroma 8:23) Zoona, ciyembekezo cawo n’cokakhala ana a Mulungu kumwamba. Izi zinatheka cifukwa anakhala Akhiristu obatizika, ndipo Mulungu anawakhululukila macimo kupitila mwa dipo, ndi kuwayesa olungama monga ana auzimu.—Aroma 3:23-26; 4:25; 8:30.

3. N’cifukwa ciani tingati Aroma caputa 8 ni yofunikanso kwa aja odzakhala padziko lapansi?

3 Komabe, Aroma caputa 8 ni yofunikanso kwa aja odzakhala padziko lapansi, ndaŵa nawonso Mulungu amawaona kukhala olungama. Timaona zimenezi mwa mau a Paulo m’kalata yake asanalembe mau a m’caputa 8. M’caputa 4 anakamba za Abulahamu wokhulupilika. Iye anakhalako Yehova akalibe kupatsa Aisiraeli Cilamulo, ndipo kukali zaka zambili Yesu akalibe kutifela. Komabe, Yehova anaona cikhulupililo ca Abulahamu, moti anamuyesa wolungama. (Ŵelengani Aroma 4:20-22.) Masiku anonso, Yehova akhoza kuwayesa olungama Akhiristu okhulupilika amene ali na ciyembekezo ca m’Baibo codzakhala na moyo wamuyaya padziko lapansi. Iwonso angapindule na malangizo a pa Aroma caputa 8 opita kwa anthu olungama.

4. Kodi Aroma 8:21 iyenela kutithandiza kufunsa kuti ciani?

4 Aroma 8:21 imatitsimikizila kuti dziko latsopano lidzabwela ndithu. Vesiyi imalonjeza kuti “cilengedweco cidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” Koma funso n’lakuti, Kodi tidzakhalako, kodi mudzalandilako mphoto imeneyo? Aroma caputa 8 ili na malangizo amene angakuthandizeni kuti mukapezekemo.

“KUIKA MAGANIZO PA ZINTHU ZA THUPI”

5. Ni nkhani yaikulu iti imene Paulo anakamba pa Aroma 8:4-13?

5 Ŵelengani Aroma 8:4-13. Aroma caputa 8 imasiyanitsa anthu amene amayenda “motsatila zofuna za thupi” ndi amene amayenda “motsatila za mzimu.” Ena angaganize kuti kumeneku n’kusiyana pakati pa anthu ali m’coonadi ndi amene salimo, komanso pakati pa Akhiristu ndi anthu akunja. Komabe, Paulo anali kulembela amene anali “ku Roma monga okondedwa a Mulungu, oitanidwa kukhala oyela.” (Aroma 1:7) Conco, Paulo anali kusiyanitsa Akhiristu oyenda motsatila za thupi ndi Akhiristu amene anali kuyenda motsatila mzimu. Kodi anali osiyana bwanji?

6, 7. (a) Kodi Baibo imaseŵenzetsa liu lakuti “thupi” m’njila zina ziti? (b) Kodi Paulo analiseŵenzetsa bwanji liu lakuti “thupi” pa Aroma 8:4-13?

6 Ganizilani coyamba liu lakuti “thupi.” Kodi apa Paulo anali kutanthauza ciani? Baibo ili na matanthauzo osiyana-siyana pa liu lakuti “thupi.” Nthawi zina limatanthauza thupi lathu leni-leni. (Aroma 2:28; 1 Akor. 15:39, 50) Lingatanthauzenso cibale, kapena kuti cibululu. Mwacitsanzo, Yesu “anatuluka m’mbeu ya Davide monga munthu [“mwa thupi,” Buku Lopatulika].” Nayenso Paulo anaona Ayuda monga ‘anthu a mtundu wake [“monga mwa thupi,” Buku Lopatulika].’—Aroma 1:3; 9:3.

7 Komabe, zimene Paulo analemba m’caputa 7 zimatithandiza kumvetsa zimene “thupi” lochulidwa pa Aroma 8:4-13 limatanthauza. Iye anagwilizanitsa “kukhala mogwilizana ndi thupi” na “zilakolako za ucimo” zimene “zinali kugwila nchito m’ziwalo [zawo.]” (Aroma 7:5) Izi zitithandiza kumvetsa mau a Paulo akuti anthu “otsatila zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi.” Iye analukamba za anthu osumika maganizo na mtima wawo wonse pa zolakalaka ndi zofuna za thupi lopanda ungwilo. Kweni-kweni, amenewo ni anthu otsatila zokhumba ndi zilakolako zawo, kaya ni zaciwelewele kapena zina.

8. N’cifukwa ciani ngakhale Akhiristu odzozedwa anafunikila kucenjezedwa kuti asakhale na umoyo wotsatila za thupi?

8 Mwina mungadabwe na mmene Paulo anacenjezela Akhiristu odzozedwa za kuyofya kokhala “mogwilizana ndi thupi.” Kodi Akhiristu amene ni mabwenzi a Mulungu, amenenso Iye waayesa olungama, nawonso angakhale pa ciopsezo cimeneco? Mkhiristu aliyense angayambe kulabadila thupi lake locimwa. Mwacitsanzo, Paulo analemba kuti abale ena ku Roma anali akapolo a “mimba zawo [kapena zilakolako zawo].” Izi zitanthauza kuti iwo anaika patsogolo zakugonana, kudya, ndi zinthu zina. Ena anali ‘kunyenga anthu oona mtima.’ (Aroma 16:17, 18; Afil. 3:18, 19; Yuda 4, 8, 12) Kumbukilaninso m’bale wa ku Korinto uja amene ‘anatengana ndi mkazi wa bambo ake.’ (1 Akor. 5:1) Conco, mpomveka kuti Mulungu anauzila Paulo kuti acenjeze Akhiristuwo pa nkhani yokhudza “kuika maganizo pa zinthu za thupi.”—Aroma 8:5, 6.

9. Kodi cenjezo la Paulo pa Aroma 8:6 sililetsa ciani?

9 Cenjezo limenelo n’lofunikila ngakhale lelolino. Pambuyo potumikila Mulungu kwa zaka zambili, Mkhiristu angayambe kusumika maganizo ake pa zinthu za thupi. Apa sitikamba za Mkhiristu amene nthawi zina amaganizilako za zakudya, nchito, zosangulutsa, ngakhale zacikondi. Cimeneci n’cibadwa kwa mtumiki aliyense wa Mulungu. Ngakhale Yesu anakondwela na zakudya, ndipo anadyetsanso ena. Analudziŵa kuti zakudya n’zofunika. Nayenso Paulo analembapo za kufunika ndi ulemu wake wa zacikondi m’cikwati.

Kodi zokamba zanu zimaonetsa kuti mumaika maganizo anu pa za mzimu kapena za thupi? (Onani palagilafu 10 na 11)

10. Kodi mau a pa Aroma 8:5, 6 akuti kuika “maganizo pa zinthu” atanthauza ciani?

10 Nanga kodi Paulo anatanthauzanji pokamba za “kuika maganizo pa zinthu za thupi”? Liu la Cigiriki limene Paulo anaseŵenzetsa litanthauza “kusumika maganizo na mtima wonse pa cinthu cinacake, ndi kuyesa kucipangila mapulani a mmene ungacicitile ngati zingatheke.” Anthu amene amakhala mwa thupi amalola kuti umoyo wawo uzitsogoleledwa na maganizo awo opanda ungwilo. Ponena za mauwo a pa Aroma 8:5, katswili wina anati: “Anthu a conco amasumika maganizo awo pa zinthu za thupi, kumacita nazo cidwi kwambili, kuzikambapo-kambapo nthawi zonse, ndi kuzikhumbila.”

11. Kodi tingaphatikizepo zinthu ziti podzifunsa kuti, ‘Kodi ine nimakonda ciani maka-maka mu umoyo wanga?’

11 Conco, kunali koyenela kuti Akhiristu a ku Roma adzifufuze kuti aone zinthu zimene anali kuika patsogolo. Kodi zinali “zinthu za thupi”? Ifenso tifunika kudzifufuza mofananamo. Nanganso zokamba zathu, kodi zimalemelela ku ciani? Timakonda kucita zinthu zanji tsiku na tsiku? Ena angapeze basi maganizo awo ali pa kukonda kumwako mitundu yosiyana-siyana ya moŵa kapena waini, kaya kutengeka kwambili na kukongoletsa pa nyumba, kugula zovala zili m’fashoni, kupeza njila zopezela ndalama, kukonza zokayenda pa maholide, na zina zaconco. Zinthu izi zilibe vuto pa izo zokha, ni mbali ya umoyo wa munthu. Kodi si paja Yesu anasandutsapo madzi kukhala vinyo! Ndipo kodi si Paulo anauza Timoteyo kuti azimwako “vinyo pang’ono”? (1 Tim. 5:23; Yoh. 2:3-11) Koma kodi Yesu na Paulo basi nthawi zonse anali kumangokamba za vinyo na kumautamanda? Iyayi. Nanga ise bwanji? Kodi ife timakonda ciani maka-maka mu umoyo wathu?

12, 13. N’cifukwa ciani zimene timaikapo maganizo ni nkhani yaikulu?

12 Kudzifufuza n’kofunika. Cifukwa? Paulo analemba kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa.” (Aroma 8:6) Imeneyi ni nkhani yoopsa—imfa ya kuuzimu tsopano, ndi imfa yeni-yeni m’tsogolo. Komabe, Paulo sanatanthauze kuti munthu ‘akaika maganizo pa zinthu za thupi,’ ndiye kuti basi mapeto ake ni imfa. Munthu akhoza kusintha. Kumbukilani za mwamuna uja wa ciwelewele ku Korinto. Iye anakonda zinthu za “thupi” cakuti anafika pocotsedwa mumpingo. Koma anasintha. Analeka kuyenda motsatila za thupi ndi kubwelela m’njila yolongosoka.—2 Akor. 2:6-8.

13 Ngati zinatheka mwamuna uja kusintha, n’zothekanso kwa Mkhiristu aliyense masiku ano, maka-maka amene sanacite kufika pa saizi ya munthu wa ku Korinto uja. Ndithudi, zimene Paulo anacenjeza zokhudza zotulukapo zake ngati munthu ‘aika maganizo pa zinthu za thupi,’ ziyenela kulimbikitsa Akhiristu kupanga masinthidwe ofunikila.

“KUIKA MAGANIZO PA ZINTHU ZA MZIMU”

14, 15. (a) Kodi Paulo anatilimbikitsa kuika maganizo athu pa ciani?’ (b) Koma kodi “kuika maganizo pa zinthu za mzimu” sikutanthauza ciani?

14 Mtumwiyo ataticenjeza za “kuika maganizo pa zinthu za thupi,” anatilimbikitsanso kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.” Ha! ikomelenji mphoto yake—moyo na mtendele! Tingacite ciani kuti tikailandile mphoto imeneyo?

15 “Kuika maganizo pa zinthu za mzimu” sikutanthauza kuti basi munthu lomba waleka na kuganiza koma kumangolota zinthu zauzimu paliponse yayi. Sikutinso basi nkhani izingokhala Baibo, cikondi cake pa Mulungu, na ciyembekezo cake ca mtsogolo, ayinso. Tiyeni tikumbukile kuti Paulo ndi ena a m’zaka 100 zoyambilila amene anakondweletsa Mulungu, anali kukhala na umoyo monga munthu aliyense. Anali kudya na kumwa. Ambili anali kukwatila ndi kusangalala na umoyo wa banja. Analinso kuseŵenza kuti azipeza zofunikila.—Maliko 6:3; 1 Ates. 2:9.

16. Ngakhale kuti Paulo anali na umoyo mofanana ndi anthu onse, kodi n’ciani cimene anaika patsogolo maka-maka?

16 Komabe, zinthu zabwino-bwino zimenezi si zimene atumiki a Mulungu anaziika patsogolo kwambili mu umoyo wawo. Pambuyo pochula kuti Paulo anali kugwila nchito yopanga matenti, Baibo imafotokoza kuti iye anaika patsogolo maka-maka nchito yolalikila ndi kuphunzitsa anthu. (Ŵelengani Machitidwe 18:2-4; 20:20, 21, 34, 35.) N’zimenenso iye analimbikitsa abale ndi alongo ku Roma kucita. Inde, umoyo wa Paulo unasumika pa zinthu za kuuzimu. Akhiristu a ku Roma anafunika kutengela citsanzo cake. Nafenso tiyenela kutelo.—Aroma 15:15, 16.

17. Kodi tingakhale na umoyo wotani ‘tikaika maganizo athu pa zinthu za mzimu?’

17 Kodi pali phindu lanji ngati tiika patsogolo zinthu za kuuzimu? Yankho yomveka bwino-bwino ili pa Aroma 8:6, yakuti: “Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.” Izi zitanthauza kulola maganizo athu kutsogoleledwa na mzimu woyela, kuti agwilizane ndi maganizo a Mulungu. Tikaika maganizo athu pa zinthu za “mzimu,” tidzakhaladi na umoyo wokhutilitsa ndi watanthauzo ngakhale pali pano. Koma m’tsogolo moyo wamuyaya, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.

18. Kodi “kuika maganizo pa zinthu za mzimu” kumabweletsa bwanji mtendele?

18 Tsopano, tiyeni tikambilane za mau olimbikitsa akuti, “kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa . . . mtendele.” Anthu ambili saupeza mtendele wa maganizo. Amayesa njila izi na izi kuti apeze mtendele, pamene ise tili nawo kale. Cina cimene cimatithandiza kukhala na mtendele n’cakuti timayesetsa kukhala pamtendele ndi a m’banja lathu, komanso ndi Akhiristu anzathu mu mpingo. Timazindikila ise, abale athu ndi alongo athu, tonse ndise opanda ungwilo. Mwa ici, nthawi zina pangabuke mavuto. Zimenezo zikacitika, tinaphunzitsidwa kutsatila malangizo a Yesu akuti: ‘Yanjana ndi m’bale wako.’ (Mat. 5:24) Zimenezi si zovuka kweni-kweni. Timakumbukila kuti m’bale kapena mlongo ameneyo nayenso amatumikila “Mulungu amene amapatsa mtendele.”—Aroma 15:33; 16:20.

19. Ni mtendele wapadela uti umene tingakhale nawo ngati tiika maganizo pa zinthu zoyenela?

19 Palinso mtendele wina wamtengo wapatali. Ngati ‘tiika maganizo pa zinthu za mzimu,’ timakhala pamtendele na Mlengi wathu. Yesaya analemba ulosi umene unakwanilitsika m’nthawi yake, koma kukwanilitsika kwake kwakukulu kukucitika masiku ano. Ulosiwo unati: “Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendele wosatha, cifukwa amadalila inu [Yehova].”—Yes. 26:3; ŵelengani Aroma 5:1.

20. N’cifukwa ciani muli oyamikila malangizo a pa Aroma caputa 8?

20 Conco, kaya ndife odzozedwa na mzimu kapena tili na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha m’paradaiso, tifunika kuyamikila malangizo ouzilidwa a pa Aroma caputa 8. Inde, tiyamikila ngako malangizo akuti tisaike kwambili patsogolo zinthu za “thupi.” Tikutelo cifukwa taona ubwino wotsatila mau olimbikitsa akuti: “Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.” Mphoto imene tidzalandila pocita zimenezi idzakhala yamuyaya, ndaŵa Paulo anati: “Cifukwa malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khiristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23.