Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 32

Inu Acicepele—Pitanibe Patsogolo Pambuyo pa Ubatizo

Inu Acicepele—Pitanibe Patsogolo Pambuyo pa Ubatizo

“Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzela m’cikondi.”—AEF. 4:15.

NYIMBO 56 Khulupilila Coonadi Iwe Mwini

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Ni zinthu zabwino ziti zimene acicepele ambili akwanitsa kucita?

 CAKA ciliconse, acicepele masauzande amabatizika. Kodi munatenga sitepe limeneli? Ngati n’telo, abale na alongo anu auzimu ni okondwela, ndipo Yehova nayenso akukondwela nanu. (Miy. 27:11) Tangoganizani zimene mwakwanitsa kale kucita. Mwakhala mukuphunzila Baibo mwina kwa zaka zingapo. Ndipo kuphunzilako kwakuthandizani kukhulupilila kuti Baibo ni Mawu a Mulungu. Kuposa pamenepo, mwadziŵanso Mwiniwake wa Mawu a m’buku lopatulika, na kuyamba kum’konda. Cikondi canu pa Yehova cinakula moti munafika pokhala mtumiki wodzipatulila wobatizika. Munapanga cisankho cabwino kwambili.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

 2 Mosakayikila, cikhulupililo canu cinayesedwa m’njila zambili musanabatizike. Ndipo mudzakumanabe na mayeso ena pamene mukukula. Satana adzafuna kufooketsa cikondi canu pa Yehova, kuti muleke kum’tumikila. (Aef. 4:14) Koma conde, musalole zimenezo kukucitikilani. Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova na kusungabe lonjezo limene munapeleka podzipatulila? Muyenela kupitabe patsogolo, kapena kuti ‘kuyesetsa mwakhama’ kuti mukhale Mkhristu wokhwima. (Aheb. 6:1) Koma kodi mungacite bwanji zimenezo?

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUPITEBE PATSOGOLO

3. Kodi Akhristu onse ayenela kucita ciyani akabatizika?

3 Tikabatizika, tonsefe tiyenela kutsatila ulangizi umene mtumwi Paulo anapatsa okhulupilila anzake ku Efeso. Iye anawalimbikitsa kuti akhale Akhristu ‘acikulile.’ (Aef. 4:13) Imeneyo ni njila ina yokambila kuti, ‘Pitanibe patsogolo.’ Conco, tingamvetse zimene Paulo anatanthauza pamene anayelekezela makulidwe auzimu na mmene mwana amakulila kuthupi. Mwana akabadwa, makolo amakondwela kwambili ndipo amamunyadila. Koma sikuti mwanayo adzakhalabe khanda mpaka kale-kale. M’kupita kwa nthawi, iye amaleka kucita “zacibwana.” (1 Akor. 13:11) N’zimenenso ife Akhristu tiyenela kucita. Tikabatizika, tiyenela kupitabe patsogolo kuuzimu. Tiyeni tikambilane njila zina zimene zingatithandize kucita zimenezi.

4. Ni khalidwe liti limene lingakuthandizeni kupita patsogolo kuuzimu? Fotokozani. (Afilipi 1:9)

4 Kulani m’cikondi canu pa Yehova. Yehova mum’konda kale kwambili. Koma cikondi canu pa iye cingakule kuposa pamenepo. Motani? Mtumwi Paulo anaonetsa njila imodzi ya mmene tingacitile zimenezi pa Afilipi 1:9. (Ŵelengani.) Paulo anali kupemphelela kuti cikondi ca Afilipi “cipitilile kukula.” Conco, tingakule m’cikondi cathu pa Yehova mwa “kudziŵa zinthu molondola, komanso kuzindikila zinthu bwino kwambili.” Tikam’dziŵa bwino Yehova, timafika pom’konda kwambili, komanso timayamikila makhalidwe ake na mmene amacitila zinthu. Cilakolako cathu cofuna kum’kondweletsa cimakula, ndipo timapewa kucita ciliconse cimene cingamukhumudwitse. Timayesetsa kudziŵa cimene cili cifunilo cake, na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco.

5-6. Kodi tingakule bwanji m’cikondi cathu pa Yehova? Fotokozani.

5 Tingakule m’cikondi cathu pa Yehova mwa kum’dziŵa bwino Mwana wake, amene anaonetsa bwino kwambili makhalidwe a Atate wake. (Aheb. 1:3) Njila yabwino yomudziŵila Yesu, ni kuphunzila mabuku anayi a Uthenga Wabwino. Ngati mulibe cizoloŵezi coŵelenga Baibo tsiku lililonse, bwanji osayamba palipano? Mukamaŵelenga nkhani za Yesu, muziganizila kwambili makhalidwe ake. Iye anali wofikilika, ndipo anali kunyamula ana aang’ono mwacikondi n’kuwafukatila. (Maliko 10:13-16) Yesu anali wokoma mtima komanso waubwenzi, moti ophunzila ake anali kumasuka kumuuza mmene anali kumvela mumtima. (Mat. 16:22) Mwakutelo, Yesu anatengela citsanzo ca Atate wake wakumwamba. Nayenso Yehova ni wofikilika kwambili. Tingamufikile m’pemphelo. Popemphela, tingam’khuthulile za mumtima mwathu, tili na cidalilo cakuti sadzatidzudzula. Iye amatikonda, komanso amatisamalila.—1 Pet. 5:7.

6 Yesu anali kucitila anthu cifundo. Mtumwi Mateyu anati: “Poona cikhamu ca anthu, iye anawamvela cisoni, cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Kodi nayenso Yehova amawamvela cifundo anthu? Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.” (Mat. 18:14) Izi n’zolimbikitsa kwambili! Tikayamba kum’dziŵa bwino Yesu, cikondi cathu pa Yehova cimakula.

7. Kodi kumacezako na Akhristu okhwima kungakuthandizeni bwanji?

7 Cina, mungakulitse cikondi canu na kupita patsogolo kuti mukhale Mkhristu wofikapo, mwa kupatula nthawi yoceza na abale na alongo okhwima mu mpingo mwanu. Onani cimwemwe cimene iwo apeza. Saona kuti analakwitsa kusankha kutumikila Yehova. Conco, apempheni kuti akusimbilen’koni zocitika zolimbikitsa zimene akhala nazo potumikila Yehova. Ndipo mukakhala na zisankho zikulu-zikulu zoti mupange, mungawapemphe nzelu. Kumbukilani kuti “pakakhala aphungu oculuka anthu amapulumuka.”—Miy. 11:14.

Mungadzikonzekeletse bwanji kudzayang’anizana na nkhani ya cisanduliko kusukulu? (Onani ndime 8-9)

8. Mungacite ciyani ngati mumakayikila zimene Baibo imakamba?

8 Thetsani zikayiko zanu. Monga taonela  m’ndime 2, Satana adzayesetsa kukulepheletsani kupita patsogolo kuuzimu. Njila imodzi imene angacitile zimenezi, ni kuyambitsa zikayiko m’maganizo mwanu pa ziphunzitso zina za m’Baibo. Mwacitsanzo, mwina anthu ena adzayesa kukupangitsani kukhulupilila cisanduliko—ciphunzitso cosalemekeza Mulungu. N’kutheka kuti pamene munali wocepelapo, simunaiganizilepo nkhani imeneyi. Koma popeza kuti lomba mwakula, mwina mumaphunzitsidwa zimenezi kusukulu. Zimene aphunzitsi anu angakambe pa za cisanduliko zingaoneke kuti n’zoona komanso zomveka. Koma n’kutheka kuti iwo sanafufuze mozama maumboni oonetsa kuti Mlengi alikodi. Kumbukilani mfundo ya pa Miyambo 18:17. Imati: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwela n’kumufufuzafufuza.” Conco, m’malo mongovomeleza m’cimbulimbuli zimene amakuphunzitsani kusukulu, fufuzani mosamala mfundo za coonadi za m’Mawu a Mulungu, Baibo. Fufuzaninso m’zofalitsa zathu. Ndipo kambani na abale na alongo amene kale anali kukhulupilila za cisanduliko. Afunseni cimene cinawapangitsa kuyamba kukhulupilila kuti kuli Mlengi amene amatikonda. Makambilano otelo angakuthandizeni kukhala na maumboni akuti Mlengi alikodi.

9. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Melissa?

9 Mlongo wina dzina lake Melissa anapindula kwambili cifukwa cofufuza nkhani ya zacilengedwe. b Iye anati: “Kusukulu, matica amafotokoza cisanduliko m’njila yakuti apangitse munthu kukhulupilila kuti n’cazoona. Poyamba, sin’nafune kufufuza cifukwa coopa kuti ningapeze kuti ciphunzitsoco n’cazoona. Koma n’nadziŵa kuti Yehova safuna kuti tizim’tumikila mwacimbuli-mbuli. Conco, n’nayamba kufufuza. N’naŵelenga buku la m’cizungu lakuti Is There a Creator Who Cares About You? na bulosha lakuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? komanso lakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri. Mfundo zimene n’napeza zinali zothandiza kwambili. Nimangoona kuti n’nacedwa kuyamba kufufuza mfundozo.

10-11. N’ciyani cingakuthandizeni kusungabe makhalidwe oyela? (1 Atesalonika 4:3, 4)

10 Pewani makhalidwe oipa. Pa nthawi ya unyamata, cilakolako ca kugonana cingakhale camphamvu kwambili, moti mungamalakelake kucita ciwelewele. Satana amafuna kuti mugonje ku zilakolako zanu. Ndiye n’ciyani cingakuthandizeni kusungabe khalidwe loyela? (Ŵelengani 1 Atesalonika 4:3, 4.) Mukamapemphela kwa Yehova panokha, muuzeni mmene mukumvela, ndipo m’pempheni kuti akulimbitseni. (Mat. 6:13) Kumbukilani kuti iye amafuna kukuthandizani, osati kukupezani zifukwa. (Sal. 103:13, 14) Mawu a Mulungu nawonso angakuthandizeni. Mlongo Melissa amene tam’chula kale, anamenya nkhondo kuti athetse maganizo osayenela. Anati: “Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kunanithandiza kuti nisagonje. Inali kunikumbutsa kuti ndine wake-wake wa Yehova, komanso kuti nifunika citsogozo cake pa umoyo wanga.”—Sal. 119:9.

11 Musamayese kuthetsa nokha mavuto amene mumakumana nawo. Auzenkoni makolo anu. N’zoona kuti simungamasuke kukambilana nkhani zacinsinsi na makolo anu. Koma mufunikabe kutelo. Mlongo Melissa anati: “N’tapemphela kuti nilimbe mtima, n’nauza atate za vuto langa. N’tawafotokozela, n’namva bwino kwambili. Ndipo n’nadziŵa kuti Yehova waninyadila.”

12. N’ciyani cingakuthandizeni kupanga zisankho zabwino?

12 Lolani mfundo za m’Baibo kukutsogolelani. Pamene mukukula, makolo anu adzayamba kukupatsani ufulu woculukilapo wopanga nokha zisankho. Ngakhale n’telo, mufunikabe thandizo cifukwa mukalibe kudziŵa zambili pa umoyo. Kodi mungapewe bwanji kupanga zisankho zolakwika zimene zingawononge ubwenzi wanu na Yehova? (Miy. 22:3) Mlongo wina dzina lake Kari, anafotokoza cimene cinam’thandiza kupanga zisankho zanzelu. Anazindikila kuti si pa ciliconse pamene Akhristu okhwima amafunika malamulo. Iye anati: “N’nafunika kumvetsetsa mfundo za m’Baibo m’malo mongotsatila cabe malamulo.” Mukamaŵelenga Baibo, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene naŵelengazi ziniuza ciyani za mmene Yehova amaonela zinthu? Kodi pali mfundo zilizonse zimene ningaseŵenzetse kuti nicite zoyenela? Ngati zilipo, kodi ningapindule motani nikaseŵenzetsa mfundozo?’ (Sal. 19:7; Yes. 48:17, 18) Mwa kuŵelenga Baibo na kusinkhasinkha mfundo zake, simudzavutika kupanga zisankho zokondweletsa Yehova. Pamene mupitabe patsogolo, mudzaona kuti simucita kufunika lamulo pa ciliconse, cifukwa mudzakhala mutadziŵa mmene Yehova amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana.

Ni mabwenzi otani amene mlongo wacitsikana uyu anasankha? (Onani ndime 13,)

13. Kodi mabwenzi abwino angakuthandizeni bwanji? (Miyambo 13:20)

13 Sankhani mabwenzi okonda Yehova. Monga takambila kale, mabwenzi amene mungasankhe angakuthandizeni kukula kuuzimu. (Ŵelengani Miyambo 13:20.) Mlongo wina dzina lake Sara, cimwemwe cinali kumuthela. Koma pali cina cinam’thandiza kuti apezenso cimwemwe. Mlongo Sara anati: “N’napeza mabwenzi abwino panthawi yake. Ine na mlongo wina wacicepele tinali kukonzekela pamodzi Nsanja ya Mlonda mlungu uliwonse. Mnzanga wina ananithandiza kuyamba kupelekako ndemanga pa misonkhano. Cifukwa ca thandizo la mabwenzi abwino, n’nayamba kuona kuti phunzilo la panekha na pemphelo n’lofunika kwambili. N’nayamba kulimbitsa ubale wanga na Yehova, ndipo n’napezanso cimwemwe.”

14. Kodi m’bale Julien anawapeza bwanji mabwenzi abwino?

14 Mungacite ciyani kuti mupange ubwenzi na anthu amene angakuthandizeni kukula kuuzimu? M’bale Julien, amene tsopano ni mkulu anati: “Pamene n’nali wacinyamata, kulalikila na ena kunanithandiza kupeza mabwenzi abwino. Mabwenzi amenewo anali okangalika, cakuti ananithandiza kuona kuti ulaliki ni wosangalatsa kwambili. N’nadziikila colinga coyamba utumiki wanthawi zonse. N’nazindikilanso kuti n’nalibe mabwenzi ambili abwino cifukwa n’nali kungofuna kukhala na mabwenzi a msinkhu wanga okha. Pambuyo pake, n’napezanso mabwenzi ena abwino pa Beteli. Citsanzo cawo cinanithandiza kusankha bwino zosangalatsa, ndipo izi zinathandiza kuti nimuyandikile kwambili Yehova.”

15. Kodi Paulo anam’cenjeza ciyani Timoteyo za mabwenzi? (2 Timoteyo 2:20-22)

15 Nanga bwanji mukazindikila kuti winawake mu mpingo sangakhale bwenzi lanu labwino? Paulo anaona kuti anthu ena mu mpingo wacikhristu wa m’zaka za zana loyamba sanali kulemekeza zinthu zauzimu. Motelo, anacenjeza Timoteyo kuti awapewe. (2 Timoteyo 2:20-22.) Ubwenzi wathu na Yehova ni wamtengo wapatali. Conco, tisalole aliyense kutiwonongela ubwenzi wathithithi umene tinapanga na Atate wathu wakumwamba.—Sal. 26:4.

KODI KUDZIIKILA ZOLINGA KUNGAKUTHANDIZENI BWANJI KUPITA PATSOGOLO KUUZIMU?

16. Kodi mungadziikile zolinga zotani?

16 Dziikileni zolinga zokupindulilani. Sankhani zolinga zimene zingalimbitse cikhulupililo canu, na kukuthandizani kuti mukhale Mkhristu wokhwima. (Aef. 3:16) Mwacitsanzo, mungadziikile colinga cocita phunzilo la inu mwini na kuŵelenga Baibo mokhazikika. (Sal. 1:2, 3) Kapena mungadziikile colinga comapemphela kaŵili-kaŵili komanso mocokela pansi pa mtima. Mwinanso mungaone kuti muyenela kusamala kwambili posankha zosangalatsa, ndiponso mmene mumagwilitsila nchito nthawi yanu. (Aef. 5:15, 16) Yehova adzakondwela kwambili poona kuti mukuyesetsa kuti mupite patsogolo.

Nanga anadziikila colinga cotani? (Onani ndime 17)

17. Kodi kuthandiza ena kungakupindulileni bwanji?

17 Mudzakhala Mkhristu wokhwima ngati muthandiza anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Mudzapeza cimwemwe cacikulu ngati mugwilitsa nchito bwino nthawi na mphamvu zanu za pa unyamata kuti muthandize ena. Mwacitsanzo, mungadziikile colinga cakuti muzithandiza okalamba komanso odwala mu mpingo mwanu. Mwina mungadzipeleke kupita kukawagulilako zinthu, kapena kuwathandiza mmene angaseŵenzetsele zipangizo zamakono. Ngati ndinu m’bale, mungadziikile colinga codzakhala mtumiki wothandiza, muli na maganizo akuti mukatumikile abale na alongo anu. (Afil. 2:4) Mumaonetsanso kuti mumakonda anthu mwa kuwauzako uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 9:36, 37) Ngati n’kotheka, mungadziikile colinga cokacitako utumiki wanthawi zonse.

18. Kodi kucita utumiki wa nthawi zonse kungakuthandizeni bwanji kuti mukule kuuzimu?

18 Kucita utumiki wanthawi zonse kungakupatseni mipata yambili kuti mupite patsogolo kuuzimu. Kutumikila monga mpainiya kungakutsegulileni khomo loloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, kutumikila pa Beteli, kapena kugwilako nchito zamamangidwe za gulu. Mlongo wina wacicepele dzina lake Kaitlyn, amene ni mpainiya anati: “Kulalikila na abale komanso alongo aluso kunanithandiza kuti nikule kuuzimu pambuyo pa ubatizo wanga. Citsanzo cawo cinanithandiza kuzamitsa cidziŵitso canga pa Baibo, na kunola luso langa lakuphunzitsa.”

19. Kodi mudzalandila madalitso otani pamene mukupitabe patsogolo kuuzimu?

19 Pamene mukupita patsogolo kuuzimu, mudzalandila madalitso ambili. Mudzapewa kudziikila zolinga zosapindulila zimene zingakuwonongeleni cabe mphamvu zanu za pa unyamata. (1 Yoh. 2:17) Mudzapewanso kupwetekedwa mtima kumene kumabwela ngati munthu wapanga zisankho zolalikwika. M’malo mwake, zinthu zidzakuyendelani bwino ndipo mudzapeza cimwemwe. (Miy. 16:3) Citsanzo canu cabwino cingalimbikitse Akhristu anzanu, acicepele ngakhale acikulile omwe. (1 Tim. 4:12) Ndipo coposa zonse, mudzakhala na mtendele komanso okhutila cifukwa cokondweletsa Yehova na kukhala pa ubwenzi wolimba na iye.—Miy. 23:15, 16.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

a Atumiki onse a Yehova amakondwela acicepele akabatizika. Ndipo ophunzila atsopano amenewa akabatizika, ayenela kupitabe patsogolo kuuzimu. Kuti onse apindule mu mpingo, nkhani ino ikambe maka-maka pa njila zimene acicepele amene angobatizika kumene angatsatile kuti apitilize kukula kuuzimu na kukhala Akhristu ofikapo.

b Maina ena asinthidwa.