Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 17

NYIMBO 99 Abale Miyanda Miyanda

Sitinakhalepo Tokha Ngakhale Pang’ono

Sitinakhalepo Tokha Ngakhale Pang’ono

“Ndikuthandiza.”​—Yes. 41:10.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Njila zinayi zimene Yehova amatisamalilila.

1-2. (a) N’cifukwa ciyani tingakambe kuti sitikhala tokha tikakumana ndi mavuto? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

 TIKAYANG’ANIZANA ndi mavuto aakulu, tingamve monga tili tokhatokha m’nkhalango ndipo tasocela. Komabe sitimakhala tokha tikakumana ndi mayeso. Atate wathu wacikondi wakumwamba sikuti amangoona mavuto athu, koma amatilonjezanso kuti adzatithandiza kupilila mavutowo. Yehova amatsimikizila atumiki ake okhulupilika kuti: “Ndikuthandiza.”​—Yes. 41:10.

2 M’nkhani ino, tikambilane mmene Yehova amatithandizila mwa (1) kutitsogolela, (2) kutisamalila, (3) kutiteteza, komanso (4) kutitonthoza. Yehova amatitsimikizila kuti ngakhale titakumana ndi mavuto otani mu umoyo, sadzatitaya konse kapena kutisiya. Conco sitili tokha ayi!

YEHOVA AMATITSOGOLELA

3-4. Kodi Yehova amatitsogolela motani? (Salimo 48:14)

3 Welengani Salimo 48:14. Yehova amadziwa kuti sitingadzitsogolele tokha. Ndi motani mmene iye amatsogolela alambili ake okhulupilika masiku ano? Njila imodzi imene amacitila zimenezi ndi kugwilitsa nchito Baibulo. (Sal. 119:105) Kudzela m’Mawu ake Baibulo, Yehova amatithandiza kupanga zisankho ndi kukhala ndi makhalidwe omwe amatithandiza kukhala ndi cimwemwe cacikulu palipano ndi kukapeza moyo wosatha m’tsogolo. a Mwacitsanzo, amatiphunzitsa kuti tisamasunge cakukhosi, tizikhala oona mtima m’zocita zathu zonse, komanso kuti tizikonda kwambili ena kucokela mumtima. (Sal. 37:8; Aheb. 13:18; 1 Pet. 1:22) Tikamaonetsa makhalidwe aumulungu amenewa, tidzakhala makolo abwino, mutu wa banja wabwino kapena mkazi wabwino, komanso mabwenzi abwino.

4 Kuwonjezela apo, Yehova m’Mawu ake anaikamo zitsanzo za anthu amene anakumana ndi mavuto ngati amene tikukumana nawo. (1 Akor. 10:13; Yak. 5:17) Tikamawelenga zocitika zenizeni zimenezi ndi kuzigwilitsa nchito pa umoyo wathu, timapindula m’njila zosacepela ziwili. Coyamba, timazindikila kuti sitili tokha. Ena akumanapo ndi mavuto amene tikukumana nawo, ndipo akwanitsa kuwapilila. (1 Pet. 5:9) Caciwili, timaphunzila zimene tingacite kuti tithe kupilila mavuto athu.​—Aroma 15:4.

5. Kodi Yehova amagwilitsa nchito ndani potitsogolela pa njila ya kumoyo?

5 Yehova amagwilitsanso nchito alambili anzathu potitsogolela. b Mwacitsanzo, oyang’anila madela amayendela mipingo kawilikawili kuti atilimbikitse. Nkhani zawo zimalimbikitsa cikhulupililo cathu. Ndipo zimatithandiza kukhalabe ogwilizana. (Mac. 15:40–16:5) Akulu naonso amayesetsa kuonetsa cidwi wofalitsa aliyense. (1 Pet. 5:​2, 3) Makolo amaphunzitsa ana awo kukonda Yehova, mmene angapangile zisankho zanzelu, komanso mmene angakhalile ndi makhalidwe abwino. (Miy. 22:6) Ndipo akazi okhwima kuuzimu amathandiza alongo acicepele mwa kukhala zitsanzo zabwino, kuwapatsa malangizo othandiza, komanso kuwalimbikitsa mwacikondi.​—Tito 2:​3-5.

6. Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule ndi citsogozo ca Yehova?

6 Yehova wacita mbali yake potipatsa citsogozo cimene tikufunikila. Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene waticitila? Miyambo 3:​5, 6 imatiuza kuti: “Uzikhulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalile luso lako lomvetsa zinthu.” Tikatelo, “iye adzawongola njila [zathu],” kutanthauza kuti adzatithandiza kupewa mavuto ambili, ndipo tidzakhala ndi umoyo wosangalatsa. Ndife oyamikila cotani nanga kuti Yehova amatipatsa malangizo acikondi!​—Sal. 32:8.

YEHOVA AMATISAMALILA

7. Kodi Yehova amatisamalila m’njila ziti? (Afilipi 4:19)

7 Welengani Afilipi 4:19. Kuwonjezela pa kutitsogolela kuuzimu, Yehova amadalitsa khama lathu kuti tipeze zofunikila zapaumoyo monga cakudya, zovala, ndi pogona. (Mat. 6:33; 2 Ates. 3:12) N’cibadwa kukhala ndi nkhawa ya mmene tingapezele zofunikila zapaumoyo, koma Yehova amatilimbikitsa kuti tisamade nkhawa kwambili. (Mat. 6:25) Cifukwa ciyani? Cifukwa Atate wathu sangawataye konse alambili ake okhulupilika pamene akufunikila thandizo. (Mat. 6:8; Aheb. 13:5) Timakhulupilila ndi mtima wonse mawu amene anakamba akuti adzatisamalila.

8. Kodi Yehova anamuthandiza motani Davide?

8 Ganizilani mmene Yehova anathandizila Davide. Pa nthawi imene Davide anali kukhala umoyo wothawathawa, Yehova anapatsa Davide ndi amuna omwe anali naye zinthu zofunikila kuti akhale ndi moyo. Pokumbukila mmene Yehova anamusamalila pa nthawi yonseyo, Davide analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.” (Sal. 37:25) N’kutheka kuti nanunso pa umoyo wanu mwaona Yehova akusamalila mwacikondi atumiki ake odzipeleka.

9. Masiku ano, kodi Yehova amawasamalila bwanji atumiki ake pa nthawi ya matsoka? (Onaninso zithunzi.)

9 Yehova amasamalilanso anthu ake pa nthawi ya matsoka. Mwacitsanzo, m’nthawi ya atumwi pomwe kunagwa njala, Akhristu a m’madela osiyanasiyana anatumiza thandizo la mciza njala kwa abale ndi alongo awo. (Mac. 11:​27-30; Aroma 15:​25, 26) Masiku anonso, anthu a Mulungu amaonetsa mzimu umodzimodzi wa kuwolowa manja. Tsoka likagwa, Yehova mwacikondi amasonkhezela anthu ake kupeleka zofunikila monga cakudya, madzi, zovala, komanso mankhwala kwa amene akhudzidwa ndi tsokalo. Anchito azamamangidwe amakonzanso nyumba za abale komanso Nyumba za Ufumu. Ndipo atumiki a Yehova mwacangu amapeleka citonthozo komanso cilimbikitso cocokela m’Baibulo kwa amene ataikilidwa katundu kapena okondedwa awo. c

Kodi Yehova amatitonthoza motani tikagweledwa tsoka? (Onani ndime 9) e


10-11. Kodi mwaphunzila ciyani pa zimene zinacitikila Borys?

10 Yehova mowolowa manja amasamalilanso awo amene akalibe kuyamba kumutumikila. Nafenso timafunafuna mipata yoonetsela kukoma mtima kwa awo amene si okhulupilila anzathu. (Agal. 6:10) Tikatelo, tidzawathandiza kudziwa zambili zokhudza Mboni komanso Yehova. Ganizilani zinacitikila Borys, mphunzitsi wamkulu pa sukulu inayake amene akhala ku Ukraine. Ngakhale kuti iye si wa Mboni za Yehova, nthawi zonse amacita mokoma mtima ndi ana a sukulu ake amene ndi Mboni, ndipo amalemekeza zimene amakhulupilila. Pamene Borys anasankha kuthawa kumene anali kukhala cifukwa ca nkhondo ndi kupita kumalo otetezeka m’dzikolo, abale athu anam’thandiza. Kenako Borys anapezekapo pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Pokumbukila zimene zinam’citikila, iye anati: “Mboni za Yehova zinandionetsa kukoma mtima, ndipo zinandisamalila. Ndiwayamikila kwambili a Mboni za Yehova.”

11 Ifenso tingatengele Atate wathu wakumwamba wacifundo mwa kuwaonetsa cikondi anthu amene akufunikila thandizo, kaya ndi okhulupilila anzathu kapena ayi. (Luka 6:​31, 36) Tili ndi cidalilo cakuti tikayesetsa kuwaonetsa cikondi anthu, tidzawathandiza kuti akhale ophunzila a Khristu. (1 Pet. 2:12) Koma kaya adzasankha kutumikila Yehova kapena ayi, tidzakhala ndi cimwemwe coculuka cimene cimabwela kaamba kopatsa.​—Mac. 20:35.

YEHOVA AMATITETEZA

12. Kodi Yehova analonjeza kuti adzapeleka citetezo cotani kwa anthu ake monga gulu? (Sal. 91:​1, 2, 14)

12 Welengani Salimo 91:​1, 2, 14. Yehova analonjeza kuti adzatisamalila masiku ano popeleka citetezo cauzimu. Sadzamulola konse Satana kuti adetse kulambila koona. (Yoh. 17:15) Ndipo timakhulupilila ndi mtima wonse kuti ‘cisautso cacikulu’ cikadzayamba, Yehova adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti adzatisamalila, osati kuuzimu kokha, koma ngakhalenso kuthupi.​—Chiv. 7:​9, 14.

13. Kodi Yehova amatiteteza motani payekhapayekha?

13 Kodi Yehova amapeleka citetezo cotani kwa aliyense payekhapayekha? Kudzela m’Malemba, Yehova amatithandiza kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela. (Aheb. 5:14) Tikamagwilitsa nchito mfundo za m’Mawu a Mulungu pa umoyo wathu, timadziteteza ku mavuto akuuzimu komanso akuthupi. (Sal. 91:4) Kuwonjezela apo, Yehova amapeleka citetezo kudzela mu mpingo. (Yes. 32:​1, 2) Tikamakhala pakati pa anthu amene amakonda Yehova, amenenso amagwilitsila nchito mfundo zake, timalimbikitsidwa ndipo zimatithandiza kupewa zisonkhezelo zoipa.​—Miy. 13:20.

14. (a) N’cifukwa ciyani Mulungu samaticinjiliza ku mavuto onse? (b) Kodi Salimo 9:10 limatitsimikizila ciyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

14 Kale, Yehova anali kuteteza alambili ake kuthupi. Komabe sanali kucita izi nthawi zonse. Nthawi zina “zinthu zosayembekezeleka” zimatigwela. (Mlal. 9:11) Kuyambila kale, Yehova wakhala akulola atumiki ake kuzunzidwa ngakhale kufa kumene pofuna kuonetsa kuti Satana ndi wabodza. (Yobu 2:​4-6; Mat. 23:34) N’cimodzimodzinso masiku ano. Ngakhale kuti Yehova sangawacotse mavuto athu, ndife otsimikiza kuti sangataye anthu amene amamukonda. d​—Sal. 9:10.

YEHOVA AMATITONTHOZA

15. Kodi pemphelo, Mawu a Mulungu, komanso Akhristu anzathu amatitonthoza motani? (2 Akorinto 1:​3, 4)

15 Welengani 2 Akorinto 1:​3, 4. Nthawi zina timakhala ndi cisoni cacikulu, nkhawa, kapena kuvutika maganizo. Mwina palipano mukukumana ndi zosautsa zimene zikukupangitsani kumva kuti muli nokhanokha. Kodi pali aliyense amene amamvetsa mmene mukumvela? Inde alipo, ameneyo ndi Yehova. Sikuti iye amangoona ululu wathu, koma ‘amatitonthozanso pa mayeselo athu onse.’ Kodi amatitonthoza motani? Tikamucondelela m’pemphelo, amatipatsa “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:​6, 7) Timapezanso citonthozo tikamawelenga mawu amene Yehova anatilembela m’Baibulo. M’Mawu ake amenewo, Yehova amatiuza za kuzama kwa cikondi cake pa ife, mmene tingakhalile anzelu, ndipo amatipatsa ciyembekezo. Pa misonkhano yathu ya Cikhristu, timapeza citonthozo tikakhala pamodzi ndi abale ndi alongo, komanso tikamaphunzila mfundo za m’Baibulo.

16. Kodi tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitila Nathan ndi Priscilla?

16 Kuti timvetse mmene Yehova amapelekela citonthozo ndi cilimbikitso kudzela m’Mawu ake, tiyeni tiganizile zimene zinacitikila Nathan ndi Priscilla amene akhala ku America. Zaka zingapo zapitazo, iwo anasankha kupita kudela kumene kunali kufunikila ofalitsa Ufumu ambili. Nathan anati, “Tinali ndi cidalilo cakuti Yehova adzadalitsa khama lathu.” Koma atafika kumaloko, anayang’anizana ndi mavuto athanzi komanso azacuma amene sanayembekezele. Patapita nthawi, iwo anabwelela kwawo, ndipo anapitiliza kukumana ndi mavuto azacuma. Nathan anakamba kuti: “Tinadabwa kuti n’cifukwa ciyani Yehova sanatidalitse monga tinali kuganizila. Ndinafika poganiza kuti mwina ndinalakwitsa cinacake.” M’kupita kwa nthawi, Nathan ndi Priscila anadzazindikila kuti Mulungu sanawasiye pa nthawi imene anafunikila thandizo. Nathan anakambanso kuti, “Pa nthawi zovuta zimenezo, Baibulo linakhala ngati bwenzi lanzelu limene linali kutipatsa cilimbikitso ndi citsogozo. Kuganizila mmene Yehova anatithandizila kupilila mavutowo m’malo moganizila kwambili mavuto amenewo, kunatikonzekeletsa kudzayang’anizana ndi mavuto am’tsogolo mwacikhulupililo.”

17. Kodi mlongo Helga anatonthozedwa motani? (Onaninso cithunzi.)

17 Abale ndi alongo athu angatitonthozenso m’njila zina. Motani? Onani citsanzo ca Helga wa ku Hungary. Kwa zaka, iye anali kugwebana ndi zovuta zosiyanasiyana zimene zinamupangitsa kukhala ndi nkhawa komanso kumva kuti ndi wosafunika. Koma akakumbukila zocitikazo, iye amazindikila kuti Yehova anali kumutonthoza kudzela mu mpingo. Iye anakamba kuti: “Yehova nthawi zonse anali kundithandiza akaona kuti mphamvu zanga zikucepa cifukwa ca nchito yakuthupi, kusamalila mwana wanga wodwala, komanso cifukwa ca zovuta zina. Kwa zaka 30, tsiku lililonse Yehova wakhala akusunga lonjezo lake mwa kunditonthoza. Nthawi zambili, iye amandilimbitsa kudzela m’mawu okoma, ondiganizila, komanso ondiyamikila ocokela kwa ena. Nthawi zambili, anthu amandilembela mameseji, kunditumizila makhadi, kapena kundiuza mawu ondiyamikila pa nthawi yomwe ndikufunikila kwambili cilimbikitso.”

Kodi Yehova angakugwilitseni nchito motani potonthoza ena? (Onani ndime 17)


18. Kodi tingawatonthoze motani ena?

18 Tingatengele citsanzo ca Mulungu wathu mwa kutonthoza ena. Tingacite motani zimenezi? Tingatelo mwa kukamba nawo moleza mtima, kuwauzako mawu otonthoza, komanso kuwathandiza pa zimene akusowa. (Miy. 3:27) Timayesetsa kutonthoza onse amene akuvutika, kuphatikizapo awo asanayambe kutumikila Mulungu. Maneba athu akagweledwa malilo, akadwala, kapena akakhala ndi nkhawa, timawayendela, kuwamvetsela, komanso kuwagawilako uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo. Tikamatengela citsanzo ca Yehova yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” tidzathandiza okhulupilila anzathu kupilila mavuto awo, ndipo tidzafewetsanso mitima ya anthu osakhulupilila kuti ayambe kulambila koyela.​—Mat. 5:16.

NTHAWI ZONSE YEHOVA AMAKHALA NAFE

19. Kodi Yehova amaticitila ciyani? Nanga tingatengele motani citsanzo cake?

19 Yehova amadela nkhawa kwambili onse amene amamukonda. Iye satitaya tikamakumana ndi mavuto. Monga mmene kholo lacikondi limasamalilila mwana wake, nayenso Yehova amasamalila alambili ake okhulupilika. Amatitsogolela, kutithandiza kupeza zosowa, kutiteteza, komanso kutitonthoza. Timatengela citsanzo ca Atate wathu wacikondi wakumwamba pamene tikuthandiza komanso kulimbikitsa amene akukumana ndi mavuto. Ngakhale tikumane ndi mavuto komanso zopweteka mtima, tisakaike m’pang’ono pomwe kuti Yehova ali nafe. Ndi iko komwe, iye analonjeza kuti: “Usacite mantha, cifukwa ndili ndi iwe.” (Yes. 41:10) Izi zimatipatsa cidalilo cacikulu cakuti sitinakhalepo tokha.

NYIMBO 100 Alandileni na Manja Aŵili

a Onani nkhani yakuti “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2011.

b Onani ndime 11-14 za nkhani yakuti “Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2024.

c Mungapeze zitsanzo zaposacedwa pa jw.org ku Chichewa mwa kulemba m’danga lofufuzila mawu akuti “nchito yothandiza ena pakagwa tsoka.”

d Onani “Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2017.

e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pambuyo pa tsoka la zacilengedwe, abale ndi alongo akulandila thandizo lakuthupi ndi lakuuzimu ku Malawi.