Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

NYIMBO 65 Pita Patsogolo!

Inu Abale Acinyamata​​—Tengelani Citsanzo ca Maliko ndi Timoteyo

Inu Abale Acinyamata​​—Tengelani Citsanzo ca Maliko ndi Timoteyo

“Ubwelenso ndi Maliko cifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.”​—2 TIM. 4:11.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene citsanzo ca Maliko ndi Timoteyo cingathandizile abale acinyamata kukulitsa makhalidwe ofunikila kuti atumikile ena mokulilapo.

1-2. Ndi zopinga ziti zikanalepheletsa Maliko ndi Timoteyo kutumikila ena mokulilapo?

 INU abale acinyamata, kodi mumafuna kucita zambili potumikila Yehova komanso pothandiza ena mu mpingo mwanu mokulilapo? N’zosacita kufunsa. N’zosangalatsa zedi kuona kuti acinyamata ambili ali ndi mtima wofunitsitsa kutumikila ena. (Sal. 110:3) Komabe mungakumane ndi zopinga pocita zimenezo. Kodi mumazengeleza kuwonjezela utumiki wanu cifukwa coopa za m’tsogolo? Kodi nthawi ina munakanapo kucita utumiki winawake cifukwa coona kuti simungaukwanitse? Ngati n’telo, si ndinu woyamba kumvapo conco.

2 Maliko ndi Timoteyo anamvapo conco. Koma sanalole mantha oopa za m’tsogolo komanso kusadziwa zambili pa umoyo kuwalepheletsa kutumikila ena. N’kutheka kuti Maliko anali kukhala ndi amayi ake m’nyumba yabwino pomwe anaitanidwa kuti ayende ndi mtumwi Paulo komanso Baranaba pa ulendo wawo woyamba waumishonale. (Mac. 12:​12, 13, 25) Koma anacoka m’dela limene anazolowelalo kuti awonjezele utumiki wake. Coyamba anapita ku mzinda wa Antiyokeya. Kenako anapita ndi Paulo komanso Baranaba ku malo ena akutali. (Mac. 13:​1-5) Mofananamo, n’kutheka kuti nayenso Timoteyo anali kukhala ndi makolo ake pomwe Paulo anamuitana kuti aziyenda naye m’nchito yolalikila. Pokhala kuti anali wacinyamata komanso wosadziwa zambili pa umoyo, Timoteyo akanalola zimenezo kumulepheletsa kuyamba kuyenda ndi Paulo. (Yelekezelani ndi 1 Akorinto 16:​10, 11 komanso 1 Timoteyo 4:12.) Komabe iye anavomela kuyamba kuyenda ndi Paulo ndipo analandila madalitso ambili.​—Mac. 16:​3-5.

3. (a) N’ciyani cionetsa kuti Paulo anali kuyamikila kwambili Maliko ndi Timoteyo? (2 Timoteyo 4:​6, 9, 11) (Onaninso zithunzi.) (b) Ndi mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

3 Maliko ndi Timoteyo anaphunzila maluso othandiza komanso mmene angasenzele maudindo akuluakulu akali acinyamata. Paulo anali kuwayamikila kwambili acinyamata amenewa moti pambuyo pake iye anali kufuna kuti anyamatawo akhale pa mbali pake, iye atazindikila kuti moyo wake uli kumapeto. (Welengani 2 Timoteyo 4:​6, 9, 11.) Ndi makhalidwe ati omwe Maliko ndi Timoteyo anali nawo omwe anacititsa Paulo kuwakonda komanso kuwadalila? Kodi abale acinyamata angacite ciyani kuti atengele citsanzo cawo? Kodi abale acinyamata angapindule motani ndi malangizo acikondi a Paulo?

Maliko ndi Timoteyo anakhala ofunika kwa Paulo mwa kusenza maudindo aakulu akali acinyamata (Onani ndime 3) b


KHALANI OFUNITSITSA KUTUMIKILA POTENGELA MALIKO

4-5. Kodi Maliko anaonetsa motani kuti anali wofunitsitsa kutumikila ena?

4 Malinga ndi buku lina, mawu akuti kutumikila, angatanthauze kuthandiza ena “mwakhama mosasamala kanthu za zovuta zimene zingakhalepo.” Maliko anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhaniyi. Pomwe Paulo anakana kumutenga pa ulendo wawo waciwili waumishonale, n’kutheka kuti izi zinamupweteka mtima ndipo analinso wokhumudwa. (Mac. 15:​37, 38) Koma izi sizinamufooketse kuti asiye kutumikila abale ndi alongo ake.

5 M’malomwake, Maliko anayamba kutumikila limodzi ndi msuweni wake Baranaba. Patapita zaka ngati 11, Paulo atamangidwa koyamba ku Roma, Maliko anali mmodzi mwa anthu amene anali kum’thandiza. (Filim. 23, 24) Ndipo Paulo anayamikila kwambili thandizo la Maliko, moti ponena za iye anati, “amandilimbikitsa kwambili.”​—Akol. 4:​10, 11.

6. Kodi Maliko anapindula motani cifukwa coceza ndi Akhristu okhwima? (Onaninso mawu a m’munsi.)

6 Maliko anapindula kwambili cifukwa coceza ndi Akhristu okhwima. Atakhala ndi Paulo ku Roma kwakanthawi, anapita ku Babulo kukakhala ndi mtumwi Petulo. Petulo anakhala pa ubwenzi wolimba ndi iye, moti Petulo anamucha “mwana wanga.” (1 Pet. 5:13) N’kutheka kuti pomwe Petulo anali kugwila nchito ndi Maliko, anafotokozela mnzake wacinyamatayo zinthu zambili zocititsa cidwi zokhudza umoyo wa Yesu komanso utumiki wake, moti pambuyo pake Maliko analemba zinthu zimenezo m’buku la Uthenga Wabwino lodziwika ndi dzina lake. a

7. Kodi m’bale wacinyamata Seung-Woo, anatengela motani citsanzo ca Maliko? (Onaninso cithunzi.)

7 Maliko anakhalabe wokangalika mu utumiki wake ndipo anali kugwilizana kwambili ndi abale okhwima. Kodi mungatengele bwanji citsanzo cake? Ngati nthawi ina simunayenelele utumiki winawake, dzilezeleni mtima ndipo pitilizani kufunafuna mipata ina yotumikila Yehova komanso abale anu mu mpingo. Ganizilani citsanzo ca Seung-Woo amene tsopano akutumikila monga mkulu. Ali wacinyamata, iye anali kudziyelekezela ndi abale ena acinyamata. Ena mwa abalewo analandila mautumiki amene iye anali asanalandile. Seung-Woo anali wokhumudwa poona kuti akunyalanyazidwa. Ndipo m’kupita kwa nthawi, anadandaula kwa abale okhwima. Mmodzi wa akuluwo pomulimbikitsa anamuuza kuti ndi bwino kucita zimene angathe potumikila ena ngakhale kuti ena sangaone zabwino zimene akucita. Cifukwa ca ulangizi umenewu, Seung-Woo anayamba kuthandizila okalamba komanso aja ofunikila thandizo la mayendedwe popita kumisonkhano. Pokumbukila za nthawiyo iye anati: “N’namvetsa bwino lomwe zomwe ndiyenela kucita kuti nditumikile ena mofikapo. N’napeza cimwemwe coculuka cifukwa cothandiza ena.”

Kodi abale acinyamata angapindule motani akamaceza kawilikawili ndi abale okhwima? (Onani ndime 7)


ONETSANI KUTI MUMASAMALA ZA ENA POTENGELA TIMOTEYO

8. N’ciyani cinapangitsa Paulo kusankha Timoteyo monga woyenda naye? (Afilipi 2:​19-22)

8 Paulo anafunikila mabwenzi olimba mtima oyenda nawo paulendo pomwe anali kubwelela mu mizinda momwe anthu anali kumutsutsa. Woyamba yemwe anasankha anali Sila, Mkhristu yemwe anali ciyambakale, kuti aziyenda naye. (Mac. 15:​22, 40) Pambuyo pake, Paulo anasankhanso Timoteyo monga woyenda naye. Kodi n’ciyani cinali capadela mwa Timoteyo? Iye anali ndi mbili yabwino. (Mac. 16:​1, 2) Analinso wosamala za ena moona mtima.​—Welengani Afilipi 2:​19-22.

9. Kodi Timoteyo anaonetsa bwanji kuti anali kusamaladi za abale ndi alongo ake?

9 Kungocokela pamene Timoteyo anayamba kutumikila ndi Paulo, iye anaonetsa kuti anali kusamala kwambili za ena kuposa za iyemwini. Ici n’cifukwa cake Paulo anasiya Timoteyo ku Bereya kuti alimbikitse ophunzila atsopano. (Mac. 17:​13, 14) N’zosakaikitsa kuti Timoteyo anapindula kwambili ndi citsanzo ca Sila, yemwenso anatsalila ku Bereya. Komabe, pambuyo pake Paulo anatuma Timoteyo ku mzinda wa Tesalonika kukalimbikitsa Akhristu kumeneko. (1 Ates. 3:2) Kwa zaka 15 zotsatila, Timoteyo anaphunzila ‘kulila ndi anthu amene akulila,’ poonetsa kuti anali kuwamvela cisoni amene anali kuvutika. (Aroma 12:15; 2 Tim. 1:4) Kodi inu Akhristu acinyamata, mungatengele motani citsanzo ca Timoteyo?

10. Kodi m’bale wina dzina lake Woo Jae, anaphunzila motani kuonetsa ena cidwi?

10 M’bale wina dzina lake Woo Jae anaphunzila zimene angacite kuti azionetsa ena cidwi mokulilapo. Ali wacinyamata, zinali kumuvuta kukambilana ndi abale komanso alongo acikulile. Akawaona pa misonkhano, anali kungowapatsa moni n’kuwadutsa. Mkulu wina anauza Woo Jae kuti angayambe makambilano ndi okhulupilila anzake mwa kuwauza zimene amayamikila mwa iwo. Mkuluyo anauzanso Woo Jae kuti aziganizilanso zimene munthu winayo angacite nazo cidwi. Iye anayamba kugwilitsa nchito ulangizi umenewu pokambilana ndi ena. Tsopano Woo Jae akutumikila monga mkulu. Iye anati: “Tsopano zimakhala zosavuta kukhala ndi makambilano atanthauzo ndi anthu amisinkhu yosiyanasiyana. Ndimamva bwino podziwa kuti ndimazimvetsa bwino nkhawa za anthu ena. Izi zandithandiza kudziwa zimene abale ndi alongo akufunikiladi komanso zimene ndingacite powathandiza.’’

11. Kodi abale acinyamata angakulitse bwanji cidwi pa ena mu mpingo mwawo? (Onaninso cithunzi.)

11 Inunso abale acinyamata mungaphunzile kuonetsa ena cidwi. Mukakhala pa misonkhano, muzilankhulako ndi anthu amisinkhu yosiyanasiyana komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Muziwafunsa mmene umoyo ulili, kenako muziwamvetsela. M’kupita kwa nthawi mudzazindikila mmene mungawathandizile. N’kutheka mungazindikile kuti banja lina lacikulile lifunikila thandizo la mmene lingagwilitsile nchito JW Library®. N’kuthekanso mungazindikile kuti lilibe munthu wopita nalo mu ulaliki. Kodi mungathandize otelo kudziwa mmene angagwilitsile nchito zipangizo zawo kapena kulinganiza kuti mupite nawo mu ulaliki? Mukadzipeleka kuti muthandize abale ndi alongo anu mwa njila imeneyi, mudzakhala citsanzo cabwino mu mpingo mwanu.

Abale acinyamata angathandize mpingo m’njila zambili (Onani ndime 11)


PINDULANI NDI MALANGIZO ACIKONDI A PAULO

12. Kodi abale acinyamata angapindule motani ndi ulangizi wa Paulo wopita kwa Timoteyo?

12 Paulo anapatsa Timoteyo malangizo omuthandiza kukhala umoyo wacimwemwe komanso kuti akhale wopambana mu ulaliki. (1 Tim. 1:18; 2 Tim. 4:5) Inunso abale acinyamata mungapindule ndi malangizo acikondi a Paulo. Motani? Powelenga makalata awili a Paulo opita kwa Timoteyo, muziwaona ngati analembela inu, ndipo muzionamo malangizo amene mungagwilitse nchito pa umoyo wanu. Tiyeni tioneko zitsanzo zingapo.

13. Kodi cofunika n’ciyani kuti munthu akhale wokhulupilika kwa Mulungu?

13 “Uzidziphunzitsa n’colinga coti ukhalebe wodzipeleka kwa Mulungu.” (1 Tim. 4:7b) Kodi kukhala wodzipeleka kwa Mulungu kumatanthauza ciyani? Kumatanthauza kukhala wokhulupilika kwa Yehova komanso kukhala ndi cikhumbo cofuna kum’kondweletsa. Popeza sitibadwa nalo khalidwe limeneli, timafunika kucita kulikulitsa. Tingalikulitse motani? Mawu a Cigiriki omwe anawamasulila kuti “uzidziphunzitsa,” nthawi zambili anali kuwagwilitsa nchito pofotokoza masewela olimbitsa thupi amene othamanga anali kucita pokonzekela mpikisano. Othamangawo anafunika kupewa zilizonse zimene zikanawasokoneza, ndi kuika maganizo awo pa kupambana. Nafenso tiyenela kupewa zinthu zimene zingaticeutse kuti tikulitse makhalidwe amene angatithandize kupambana.

14. Pamene tiwelenga Baibulo, kodi tiyenela kukhala ndi colinga canji? Pelekani citsanzo.

14 Pamene mukulitsa cizolowezi canu cowelenga Baibulo, muzikumbukila kuti colinga canu ndi kuyandikila Yehova. Mwacitsanzo, yelekezani kuti mukuwelenga nkhani ya wolamulila wacinyamata wa cuma. (Maliko 10:​17-22) Wolamulila wacinyamatayu anali kukhulupilila kuti Yesu ndiye analidi Mesiya, koma cikhulupililo cakeco cinali cocepa moti sicinathe kum’sonkhezela kuti akhale wotsatila wake. Ngakhale n’telo, Yesu “anamukonda.” Kodi simunakhudzike mtima poona mmene Yesu analankhulila ndi mnyamatayo? N’zoonekelatu kuti Yesu anali kufuna kuti mnyamatayo apange cisankho canzelu. Yesu analinso kuonetsa cikondi cimene Yehova anali naco pa mnyamatayo. (Yoh. 14:9) Pamene mukuganizila za nkhaniyi komanso mikhalidwe ya pa umoyo wanu, dzifunseni kuti, ‘Mosiyana ndi wolamulila wacinyamatayu, kodi ndiyenela kucita ciyani kuti ndiyandikile Yehova komanso kutumikila ena mofikapo?’

15. N’cifukwa ciyani m’bale wacinyamata ayenela kukhala citsanzo cabwino kwa ena? Pelekani citsanzo. (1 Timoteyo 4:​12, 13)

15 ‘Khalani citsanzo kwa okhulupilika.’ (Welengani 1 Timoteyo 4:​12, 13.) Paulo sanangolimbikitsa Timoteyo kukhala ndi maluso monga kuwelenga ndi kuphunzitsa, koma anamulimbikitsanso kuti akhale ndi makhalidwe monga cikondi, cikhulupililo, ndi khalidwe loyela. Cifukwa ciyani? Cifukwa anthu amakhulupilila kwambili zocita za munthu kuposa mawu ake. Tinene kuti mwapatsidwa nkhani yofotokoza zimene munthu angacite kuti awonjezele cangu cake mu ulaliki. Simudzacita manyazi kuikamba nkhaniyo ngati inuyo ndinu citsanzo cabwino mu ulaliki. Omvela adzalimbikitsidwa kutsatila malangizo omwe mukuwapatsa m’nkhani yanu potengela citsanzo canu.​—1 Tim. 3:13.

16. (a) Kodi Mkhristu wacinyamata angakhale citsanzo cabwino m’mbali zisanu ziti? (b) Kodi m’bale wacinyamata angakhale bwanji citsanzo cabwino “m’kalankhulidwe”?

16 Monga yaonetsela 1 Timoteyo 4:​12, Paulo anachula mbali zisanu zimene m’bale wacinyamata angakhalile citsanzo cabwino. Pa phunzilo lanu la munthu mwini, bwanji osaganizilapo pa mbalizo, iliyonse payokha? Tinene kuti mufuna kukhala citsanzo cabwino “m’kalankhulidwe.” Muyenela kuganizila mmene mungagwilitsile nchito mawu anu polimbikitsa ena. Mwacitsanzo, ngati mukukhalabe pa nyumba ya makolo, kodi mungawonjezele ciyamikilo pa zimene amakucitilani? Pambuyo pa misonkhano, kodi mungayamikile wina pa zimene wacita bwino pa mbali imene anali nayo? Mungayesenso kupeleka mayankho m’mawu anuanu pa misonkhano. Khama lanu pokhala citsanzo cabwino m’kalankhulidwe lidzaonetsa kuti mukupita patsogolo kuuzimu.​—1 Tim. 4:15.

17. Kodi n’ciyani cingathandize m’bale wacinyamata kukwanilitsa zolinga zauzimu? (2 Timoteyo 2:22)

17 “Thawa zilakolako za unyamata, koma tsatila cilungamo.” (Welengani 2 Timoteyo 2:22.) Paulo anauza Timoteyo kuti alimbane ndi zilakolako zimene zingamulempheletse kukwanilitsa zolinga zake zauzimu komanso zimene zingawononge ubale wake ndi Yehova. Koma mungazindikile kuti zinthu zina, ngakhale kuti si zolakwika pa izo zokha, zingakuwonongeleni nthawi yocita zinthu zauzimu. Mwacitsanzo, ganizilani nthawi imene mumathela pocita zamasewela, pa intaneti, komanso posewela magemu a pa kompyuta. Kodi mungagwilitseko nchito ina ya nthawi imeneyo pocita zinthu zauzimu? Mwina mungadzipeleke kukonza Nyumba za Ufumu za kwanuko kapena kucitako ulaliki wa poyela. Mukamatengamo mbali m’zocitika ngati zimenezi, n’kutheka mudzapeza mabwenzi atsopano amene adzakuthandizani kudziikila zolinga zauzimu ndi kuzikwanilitsa.

KUTUMIKILA ENA KUMABWELETSA MADALITSO

18. N’cifukwa ciyani tinganene kuti Maliko ndi Timoteyo anakhala umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa?

18 Maliko ndi Timoteyo anadzimana zinthu zina kuti atumikile ena ndi mtima wonse. Izi zinacititsa kuti akhale umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa. (Mac. 20:35) Potumikila okhulupilila anzake, Maliko anayenda m’madela osiyanasiyana akutali. Analembanso za nkhani yocititsa cidwi yonena za umoyo wa Yesu ndi utumiki wake. Timoteyo anathandiza Paulo kukhazikitsa mipingo yatsopano komanso kulimbikitsa abale ndi alongo. N’zosacita kufunsa kuti Yehova anasangalala ndi mzimu wodzimana umene Maliko ndi Timoteyo anaonetsa.

19. N’cifukwa ciyani abale acinyamata ayenela kuyesetsa kutsatila ulangizi wa Paulo kwa Timoteyo? Nanga padzakhala zotulukapo zotani?

19 Tingaone kuti Paulo anali kumukonda kwambili Timoteyo. Izi zimaonekela bwino m’mawu amene Paulo anagwilitsa nchito m’makalata amene analembela mnzake wacinyamatayo Timoteyo. Makalata ouzilidwawa amaonetsanso kuti Yehova amakukondani kwambili inuyo abale acinyamata. Iye amafuna kuti mukhale acimwemwe pomutumikila. Conco citani zonse zimene mungathe kuti mutsatile malangizo acikondi a Paulo ndi kukulitsa cikhumbo canu cofuna kutumikila ena mofikapo. Mukatelo, mudzakhala ndi umoyo wacimwemwe palipano, ndipo ‘mudzagwila mwamphamvu moyo weniweniwo’ umene ukubwela.​—1 Tim. 6:​18, 19.

NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’

a Popeza Petulo sanali kubisa mmene anali kumvela, n’kutheka anafotokozela Maliko mmene Yesu anali kumvela komanso kucitila zinthu pa umoyo wake. Ici ciyenela kuti ndiye cifukwa cake Maliko anafotokoza kwambili mmene Yesu anali kumvela komanso kucitila zinthu.​—Maliko 3:5; 7:34; 8:12.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Maliko akuthandiza Paulo ndi Baranaba pa ulendo wawo waumishonale. Mofunitsitsa, Timoteyo akuyendela abale ku mpingo winawake kuti awalimbikitse ndi kuwathandiza.