Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 39

NYIMBO 125 “Acifundo ni Acimwemwe!”

Pezani Cimwemwe Coculuka Cimene Cimabwela Cifukwa Copatsa

Pezani Cimwemwe Coculuka Cimene Cimabwela Cifukwa Copatsa

“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”​—MAC. 20:35.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tiphunzile njila zosiyana-siyana za mmene tingakhalile opatsa, komanso cifukwa cake kupatsa kumatibweletsela cimwemwe

1-2. Timapindula bwanji cifukwa cakuti Yehova anatilenga m’njila yakuti tizikhala na cimwemwe coculuka tikakhala opatsa?

 YEHOVA anatilenga m’njila yakuti tizikhala na cimwemwe coculuka tikakhala opatsa kuposa tikalandila zinazake. (Mac. 20:35) Kodi izi zitanthauza kuti sitingakhale na cimwemwe tikapatsidwa mphatso? Ayi. Tidziŵa kuti tonse timakhala acimwemwe tikalandila mphatso. Komabe, timakhala na cimwemwe coposelapo ngati ndife tapeleka mphatsoyo. Kunena zoona, timapindula cifukwa cakuti Yehova anatilenga mwa njila imeneyi. N’cifukwa ciyani tikutelo?

2 Potilenga mwa njila imeneyi, Yehova anatipatsa mwayi wowonjezela cimwemwe cathu. Tingawonjezele cimwemwe cathu mwa kuganizila njila zosiyana-siyana za mmene tingakhalile opatsa. Kodi si zosangalatsa kuti Yehova anatilenga mwa njila imeneyi?​—Sal. 139:14.

3. N’cifukwa ciyani Yehova amachedwa “Mulungu wacimwemwe”?

3 Malemba amatitsimikizila kuti kupatsa kumabweletsa cimwemwe. Conco m’pomveka kuti Baibo imacha Yehova kuti ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Iye ndiye anali woyamba kupatsa ena zinthu, ndipo palibe amene angapatse ena zoculuka kuposa Yehova. Izi n’zogwilizana na zimene mtumwi Paulo anakamba kuti “cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:28) Inde, “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo imacokela” kwa Yehova.​—Yak. 1:17.

4. N’ciyani cingatithandize kukhala na cimwemwe coculuka?

4 N’zoonekelatu kuti tonse timafuna kupeza cimwemwe coculuka cimene cimabwela cifukwa cokhala opatsa. Tingakhale naco mwa kutengela citsanzo ca Yehova ca kuwolowa manja. (Aef. 5:1) Tiyeni tikambilane zimene tingacite kuti titengele citsanzo ca Yehova ca kuwolowa manja. Pokambilana zimenezi, tiphunzilenso zimene tingacite ngati tiona kuti anthu ena sayamikila kuwolowa manja kwathu. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kuti tipitilize kukhala opatsa na kuwonjezela cimwemwe cathu.

TENGELANI CITSANZO CA YEHOVA CA KUWOLOWA MANJA

5. Chulani zinthu zina zakuthupi zimene Yehova amatipatsa.

5 Kodi Yehova amaonetsa kuti ni wowolowa manja m’njila ziti? Tiyeni tioneko zocepa. Yehova amatipatsa zinthu zakuthupi zimene timafunikila. Mwina Yehova sangacititse kuti tikhale na umoyo wapamwamba. Koma amaonetsetsa kuti tili na zofunikila pa umoyo. Mwa citsanzo iye amatithandiza kupeza cakudya, zovala, komanso pogona. (Sal. 4:8; Mat. 6:31-33; 1 Tim. 6:6-8) Koma, kodi Yehova amatipatsa zofunika za paumoyo, cabe cifukwa cakuti ni udindo wake kutelo? Kutalitali! Nanga n’cifukwa ciyani amatipatsa?

6. Tiphunzilapo ciyani pa Mateyo 6:25, 26?

6 Mwacidule tinganene kuti Yehova amatipatsa zofunikila za pa umoyo cifukwa amatikonda. Ganizilani mawu a Yesu a pa Mateyo 6:25, 26. (Ŵelengani). Yesu anaseŵenzetsa za m’cilengedwe poonetsa kuti Yehova amatisamalila cifukwa cotikonda. Pokamba za mbalame iye anati: “Sizifesa mbewu ayi, kapena kukolola, kapenanso kututila m’nkhokwe.” Koma onani zimene ananena pambuyo pake. Iye anati: “Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa.” Kenako Yesu anafunsa kuti: “Kodi inu si sindinu ofunika kwambili kuposa mbalame?” Kodi iye anali kufuna kutiphunzitsa mfundo yanji pamenepa? Yehova amaona alambili ake okhulupilika kukhala amtengo wapatali kuposa nyama. Ngati Yehova amasamalila nyama, ndiye kuti sangalephele kutisamalila. Monga mmene tate wacikondi amasamalila banja lake, nayenso Yehova amasamalila banja lake cifukwa amalikonda.​—Sal. 145:16; Mat. 6:32.

7. Chulani njila imodzi imene tingakhalile owolowa manja monga Yehova. (Onaninso cithunzi.)

7 Tingatengele citsanzo ca Yehova pa nkhaniyi mwa kupatsa ena zinthu cifukwa cowakonda. Mwa citsanzo, kodi mudziŵako wokhulupilila mnzanu amene afunikila cakudya kapena zovala? Yehova angapitile mwa inu kuti apeleke thandizo kwa munthuyo. Anthu a Yehova amadziŵika kuti ni owolowa manja maka-maka pa nthawi ya tsoka. Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, abale na alongo anapeleka zakudya, zovala, komanso zinthu zina kwa abale amene anali kufunikila zinthuzo. Ambili anacitanso zopeleka mowolowa manja pothandizila nchito ya padziko lonse. Izi zinacititsa kuti tikwanitse kupeleka thandizo lofunikila kwa abale na alongo pa nthawi ya mlili padziko lonse. Abale na alongo amene anapeleka thandizo anatsatila uphungu wa pa Aheberi 13:16, pamene pamati: “Musaiŵale kucita zabwino ndi kugaŵila ena zomwe muli nazo, cifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zotelozo.”

Tonsefe tingatengele citsanzo ca Yehova ca kuwolowa manja (Onani ndime 7)


8. Timapindula bwanji Yehova akatipatsa mphamvu? (Afilipi 2:13)

8 Yehova amatipatsa mphamvu. Yehova ali na mphamvu zopanda malile, ndipo amakhala wokondwela kugaŵilako atumiki ake okhulupilika mphamvuzo. (Ŵelengani Afilipi 2:13.) Kodi munayamba mwapemphelapo kwa Mulungu kuti akuthandizeni kukaniza ciyeso? Kapena kodi munayamba mwamupemphapo mphamvu zokuthandizani kupilila mayeso ovuta? Mwinanso munapemphelapo kuti akupatseni mphamvu zokuthandizani kucita zimene munafunikila kucita pa tsikulo. Ngati iye anakupatsani mphamvuzo mutamupempha, ndiye kuti mungagwilizane na zimene mtumwi Paulo anakamba. Iye anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikila.”​—Afil. 4:13.

9. Tingaseŵenzetse bwanji mphamvu zathu potengela citsanzo ca Yehova ca kuwolowa manja? (Onaninso cithunzi.)

9 Tilibe mphamvu zopanda malile monga zilili na Yehova. Ndipo sitingapatse ena mphamvu mmene iye amacitila. Koma tingatengele citsanzo cake mwa kuseŵenzetsa mphamvu zathu pothandiza ena. Mwa citsanzo, tingathandize abale na alongo okalamba komanso odwala mwa kukawagwilila nchito za pakhomo. Tingawathandizenso kukagula zinthu ku sitolo. Ngati mungakwanitse, mungathandize kuyeletsa komanso kukonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Tikamaseŵenzetsa mphamvu zathu mwa njila imeneyi, tidzacita zambili pothandiza abale na alongo athu.

Tingaseŵenzetse mphamvu zathu kuthandiza ena (Onani ndime 9)


10. Kodi tingaseŵenzetse bwanji mawu athu polimbikitsa ena?

10 Muzikumbukila kuti mungalimbikitse ena na mawu anu. Kodi mudziŵako aliyense amene angalimbikitsidwe mukamuyamikila pa zimene amacita? Kodi mudziŵako munthu amene afunikila cilimbikitso? Ngati alipo, citam’poni kanthu poonetsa anthuwo kuti mumawakonda. Mungapite kukawaona, kuwatumila foni, kuwalembela khadi, kapena kuwatumizila meseji. Musadele nkhawa kuti mudzafunika kukamba zoculuka. Mawu ocepa koma ocokela pansi pa mtima, angathandize m’bale kapena mlongo wanu kukhalabe wokhulupilika pa tsikulo kapena kuona zinthu moyenela.​—Miy. 12:25; Aef. 4:29.

11. Kodi Yehova amaziseŵenzetsa bwanji nzelu zake?

11 Yehova amatipatsa nzelu. Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu . . . cifukwa iye amapeleka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka popanda kupezela aliyense zifukwa.” (Yak. 1:5; mawu a m’munsi) Mawuwa amaonetsa kuti Yehova samana nzelu zake. Amagaŵilako ena nzeluzo mowolowa manja. Yakobo anakambanso kuti Yehova akapeleka nzelu “amapeleka mosatonza,” kapena kuti “amapeleka popanda kupezela aliyense zifukwa.” Iye saticititsa manyazi tikapempha citsogozo cake. M’malomwake, amatilimbikitsa kuti tizipempha citsogozo cakeco.​—Miy. 2:1-6.

12. Timakhala na mipata iti yophunzitsako ena zimene tidziŵa?

12 Nanga bwanji ife? Nafenso tingatengele citsanzo ca Yehova mwa kuphunzitsako ena zimene tidziŵa. (Sal. 32:8) Anthu a Yehova ali na mipata yambili imene angaseŵenzetse kuphunzitsa ena zimene adziŵa. Mwa citsanzo, nthawi zambili timaphunzitsa ofalitsa atsopano mmene angacitile ulaliki. Nawonso akulu moleza mtima, amaphunzitsa atumiki othandiza komanso abale obatizika mmene angasamalile maudindo awo mumpingo. Kuwonjezela apo, abale na alongo amene ali na maluso m’dipatimenti ya za mamangidwe, amaphunzitsako ena mmene angagwilile nchito zomanga za gulu.

13. Tingakhale bwanji owolowa manja monga Yehova pamene tikuphunzitsa ena zimene tidziŵa?

13 Muziyesetsa kutengela citsanzo ca Yehova pamene mukuphunzitsa ena. Muzikumbukila kuti iye amapeleka nzelu zake mowolowa manja. Mofananamo, nafenso tifunika kuphunzitsa ena mosanyinyilika zimene tidziŵa. Sitiyenela kuopa kuphunzitsa munthu poganiza kuti m’kupita kwa nthawi angadzatiloŵe m’malo. Sitiyenelanso kukhala na maganizo akuti: ‘N’nadziphunzitsa nekha nchitoyi, iyenso adziphunzitse yekha.’ Palibe mtumiki wa Yehova aliyense amene ayenela kukhala na maganizo amenewa. M’malomwake, timakhala okondwela kuwaphunzitsa zimene tidziŵa “komanso kupeleka miyoyo yathu yeniyeniyo” kwa amene tikuphunzitsa. (1 Ates. 2:8) Timayembekezela kuti m’kupita kwa nthawi, “nawonso adzakhala oyenelela kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:1, 2) Ngati aliyense wa ife amaphunzitsako ena zimene adziŵa, tonsefe tidzaphunzila zinthu zambili, ndipo tidzakhala acimwemwe.

TIKAONA KUTI ANTHU SAYAMIKILA KUWOLOWA MANJA KWATHU

14. Kodi anthu ambili amacita ciyani tikawacitila zinthu mowolowa manja?

14 Tikakhala owolowa manja maka-maka kwa abale ana alongo athu, nthawi zambili amatiyamikila. Iwo angatitumizile uthenga wotiyamikila kapena angaonetse ciyamikilo cawo m’njila zina. (Akol. 3:15) Akatiyamikila, timakhala na cimwemwe couluka.

15. Tizikumbukila ciyani ngati ena sanaonetse kuyamikila pa zimene tawacitila?

15 Koma nthawi zina, anthu saonetsa kuyamikila pa zimene tawacitila. Nthawi zina tingaseŵenzetse nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu pothandiza munthu. Koma pambuyo pake zingaoneke kuti munthuyo sanayamikile zimene tamucitilazo. Za conco zikacitika, n’ciyani cingatithandize kukhalabe acimwemwe na kupewa kukhumudwa? Muzikumbukila mawu a pa Machitidwe 20:35, limene ndilo lemba la mutu wa nkhani ino. Cimwemwe cimene timakhala naco cifukwa copatsa, sicidalila zimene anthu acita kuti atiyamikile. Tingasankhebe kuti tizipatsa mwacimwemwe ngakhale zioneke kuti ena satiyamikila. N’ciyani cingatithandize kucita zimenezi? Tiyeni tikambilane zocepa zimene zingatithandize.

16. N’ciyani cingatithandize kukhalabe acimwemwe pamene tipatsa ena?

16 Muzitengela citsanzo ca Yehova. Iye amapatsa anthu zinthu zabwino, kaya anthuwo ayamikile kapena ayi. (Mat. 5:43-48) Yehova analonjeza kuti ngati nafenso timapatsa popanda ‘kuyembekezela kulandila kalikonse,. . . mphoto yathu idzakhala yaikulu.’ (Luka 6:35) Mawu akuti “kalikonse” angaphatikizepo mawu oyamikila. Kaya anthu atiyamikile kapena ayi pa zimene tawacitila, Yehova nthawi zonse adzatibwezela cifukwa ca zabwino zimene tacita pothandiza ena. Adzatibwezela cifukwa ‘timapeleka mosangalala.’​—Miy. 19:17; 2 Akor. 9:7.

17. N’ciyani cina cimene tingacite potengela citsanzo ca Yehova pa nkhani yopatsa? (Luka 14:12-14)

17 Cina cimene tingacite potengela citsanzo ca Yehova pa nkhani yopatsa ni kutsatila mawu a Yesu a pa Luka 14:12-14. (Ŵelengani.) Sikulakwa kuceleza kapena kucitila zabwino anthu amene nawonso angathe kuticitila zabwino. Koma bwanji ngati tazindikila kuti nthawi zina timapatsa ena cifukwa coyembekezela zinazake? Ngati zili conco tingayese kucita zimene Yesu anakamba. Tingacitile zabwino munthu amene tidziŵa kuti sangathe kutibwezela. Tikatelo, tidzakhala acimwemwe cifukwa tikutengela citsanzo ca Yehova. Tikaona zinthu mwa njila imeneyo tidzakhalabe acimwemwe pamene tikupatsa ena ngakhale kuti saonetsa kuyamikila.

18. Kodi tiyenela kupewa kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani?

18 Pewani kuganiza kuti anthu ena ni osayamika. (1 Akor. 13:7) Ngati ena sanaonetse kuyamikila tingadzifunse kuti: ‘Kodi sanayamikiledi kapena anangoiŵala kuyamikila?’ N’kutheka kuti pali zifukwa zina zimene zinapangitsa kuti asayamikile mmene tinali kuyembekezela. Ena angakhale kuti amayamikila kwambili, koma amavutika kuonetsa ciyamikilo cawo. Angacite manyazi kulandila thandizo maka-maka ngati m’mbuyomu ndiwo anali kuthandiza ena. Mulimonse mmene zingakhalile, cikondi ca Cikhristu cidzatithandiza kupewa kuwaganizila zoipa abale athu.​—Aef. 4:2.

19-20. N’cifukwa ciyani tifunika kukhala oleza mtima tikacitila ena zabwino? (Onaninso cithunzi.)

19 Khalani oleza mtima. Pokamba za kukhala owolowa manja, Mfumu Solomo anati: “Ponya mkate wako pamadzi cifukwa pakapita masiku ambili udzaupezanso.” (Mlal. 11:1) Mawu amenewa aonetsa kuti anthu ena angaonetse kuyamikila kwawo “pakapita masiku ambili.” Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina.

20 Zaka zingapo zapitazo, mkazi wa woyang’anila dela wina, analembela kalata mlongo amene anali atangobatizika kumene kuti amulimbikitse. M’kalatayo anam’limbikitsa kuti afunika kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Patapita zaka 8, mlongo uja analembela kalata mkazi wa woyang’anila delayo. Kalatayo anailemba kuti: “Mwina simukudziŵa, koma nifuna kukuuzani kuti kalata yanu inanithandiza kwambili m’zaka zapitazi.” Anakambanso kuti: “Kalata yanu inali yolimbikitsa. Lemba limene munachula lija linanifika pamtima kwambili. Ndipo n’nali kulikumbukila nthawi zonse.” a Pambuyo pofotokoza mavuto amene anali kukumana nawo, mlongo uja anati: “Nthawi zina n’nali kufuna kungoleka. N’nali kufuna kuleka kutumikila Yehova. Koma nthawi zonse n’nali kukumbukila lemba limene munachula m’kalata lija. Ndipo linali kunithandiza kukhalabe wokhulupilika. M’zaka 8 zapitazi, palibe cina ciliconse cimene cinanilimbikitsa kuposa kalata yanu, komanso lemba limene munanichulila lija.” Tangoganizani cimwemwe cimene mkazi wa woyang’anila dela anali naco atalandila kalata imeneyi ‘patapita masiku ambili’! Ifenso tingalandile ciyamikilo patapita nthawi yaitali pambuyo pothandiza munthu m’njila inayake.

Munthu wina angatiyamikile patapita nthawi yaitali kucokela pamene tinamucitila zabwino (Onani ndime 20) b


21. N’cifukwa ciyani tiyenela kupitiliza kutengela citsanzo ca Yehova ca kuwolowa manja?

21 Monga taphunzilila, Yehova anatilenga m’njila yapadela. Ngakhale kuti timasangalala tikalandila mphatso, timakhala na cimwemwe coculuka tikamapatsa ena. Timakhala acimwemwe tikakwanitsa kuthandiza okhulupilila anzathu. Ndipo timakondwela akatiyamikila pa zimene tacitazo. Komabe, kaya atiyamikile kapena ayi, timakhalabe acimwemwe podziŵa kuti tacita cinthu coyenela. Musaiŵale kuti zilizonse zimene mungapatse ena, “Yehova akhoza kukupatsani zambili kuposa zimenezo.” (2 Mbiri 25:9) Anthufe sitingathe kupatsa ena zambili kuposa zimene Yehova amatipatsa. Ndipo kulibe zosangalatsa kuposa zimene Yehova amatibwezela tikacitila ena zabwino. Conco tiyeni tisaleke kutengela citsanzo ca Atate wathu wa kumwamba ca kuwolowa manja.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

a Lemba limene mkazi wa woyang’anila dela analembela mlongo uja linali 2 Yohane 8, limene limati: “Samalani kuti musataye zinthu zimene tinakuthandizani kuti muzipeze nʼcolinga coti mudzalandile madalitso onse amene Mulungu wakukonzelani.”

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Zithunzi izi n’zoyelekezela. Zikuonetsa zimene mkazi wa woyang’anila dela uja anacita. Iye analembela mlongo wina kalata yomulimbikitsa. Patapita zaka zambili, mlongo uja analemba kalata yomuyamikila.