N’zotheka Kukhala na Umoyo Wacimwemwe Pali Pano
KUTSOGOLO, palibe amene azidzadwala, kukalamba, kapena kufa. Ndipo na imwe mungakakhale na umoyo wabwino umenewo! Koma masiku ano umoyo ni wodzala na mavuto ambili. Nanga n’ciani cingakuthandizeni kukhala na umoyo wacimwemwe? Baibo imapeleka malangizo amene angakuthandizeni pali pano kukhala na umoyo wacimwemwe, komanso wokhutilitsa. Onani ena mwa mavuto amene timakumana nawo, na mmene Baibo ingatithandizile.
KUKHALA WOSAKHUTILA
Malangizo a m’Baibo: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—Aheberi 13:5.
Masiku ano, pali zinthu zambili-mbili zimene anthu amakamba kuti tifunika kukhala nazo. Koma Baibo imakamba kuti tifunika kukhala ‘okhutila ndi zimene tili nazo pa nthawiyo.’ Motani?
Pewani “kukonda ndalama.” Anthu amalolela kucita zilizonse, ngakhale zowononga thanzi lawo, banja lawo, maubwenzi awo, makhalidwe awo abwino, komanso kucita zinthu zodzitaila ulemu, cabe cifukwa ca “kukonda ndalama.” (1 Timoteyo 6:10) Koma kucita izi n’kulakwitsa kwambili! Cifukwa munthu wokonda cuma “sakhutila.”—Mlaliki 5:10.
Anthu ni ofunika kuposa zinthu. N’zoona kuti zinthu zakuthupi zingatithandize. Koma zinthu sizingationetse cikondi kapena kutiyamikila. Anthu cabe ndiwo angacite izi. Ndipo kukhala na “bwenzi leni-leni” kungatithandize kuti tikhale okhutila mu umoyo.—Miyambo 17:17.
TINGAPANGITSE UMOYO WATHU KUKHALA WACIMWEMWE PALI PANO, MWA KUTSATILA MALANGIZO A M’BAIBO
KUPILILA PAMENE TIDWALA
Malangizo a m’Baibo: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa.”—Miyambo 17:22.
Monga “mankhwala ocilitsa,” cimwemwe cingatithandize kupilila matenda. Koma kodi tingacite ciani kuti tikhale acimwemwe pamene tidwala?
Khalani woyamikila. Ngati tiganizila maningi za mavuto athu, “masiku onse” adzaoneka monga oipa. (Miyambo 15:15) M’malo mwake, “sonyezani kuti ndinu oyamikila.” N’zimene Baibo imakamba (Akolose 3:15) Muziyamikila zinthu zabwino mu umoyo, olo zing’ono-zing’ono. Kukhala oyamikila pa zinthu monga kukongola kwa dzuŵa pamene iloŵa, kamphepo kayeziyezi, munthu amene timam’konda akatimwetulila, zingatipindulitse kwambili.
Muzithandiza ena. Ngakhale kuti thanzi lathu si ili bwino, “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Pamene ena ayamikila kuyesayesa kwathu powathandiza, timakhala wokhutila, ndipo izi zingatithandize kusaganizila kwambili za mavuto athu. Pamene tithandiza ena kukhala na umoyo wabwino, na ife timapindula.
KULIMBITSA CIKWATI
Malangizo a m’Baibo: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” —Afilipi 1:10.
Kwa okwatilana amene sakhala na nthawi yokwanila yoceza, cimakhala capafupi mgwilizano wawo kusokonezeka. Conco, ni cinthu canzelu kwa okwatilana kuika cikwati cawo patsogolo. Ndipo aziciona kuti ni cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili mu umoyo wawo.
Muzicitila zinthu pamodzi. M’malo mocita mwekha zinthu zimene mumakonda, bwanji osapanga pulogilamu yocitila zinthu pamodzi? Baibo imati: “Awili amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Capamodzi, mungaphike cakudya, kucita maseŵela olimbitsa thupi, kumwa zozizilitsa kukhosi, kapena kucita zinthu zina zimene mumakonda.
Onetsani mnzanu wa m’cikwati kuti mumam’konda. Baibo imalimbikitsa okwatilana kukondana na kulemekezana. (Aefeso 5:28, 33) Kumwetulilana, kukumbatilana mwacikondi, kapena kupatsanako tumphatso kungalimbitse cikwati canu. Cinanso, okwatilana afunika kukhala okhulupilika, ndipo safunika kugonana na munthu wina kupatulapo mkazi wawo kapena mwamuna wawo.—Aheberi 13:4.