Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mu 1881 ku Praslin, Seychelles kumene Gordon, mkulu wa asilikali, anaona kuti wapeza munda wa Edeni

Paradaiso Padziko Lapansi—Ni Yeni-yeni Kapena ni Maloto Cabe?

Paradaiso Padziko Lapansi—Ni Yeni-yeni Kapena ni Maloto Cabe?

Paradaiso! Ife anthu tikaona malo okongola m’mabuku, m’magazini, kapena pa TV, timafuna kuyenda kumalo amenewo a “paradaiso” kukasangalala ndi kuiŵalako mavuto athu. Koma tikabwelako, timadziŵa kuti umoyo udzakhalanso mmene unalili tisanapite.

Komabe, anthu amacita cidwi kwambili na paradaiso. Pa cifukwa cimeneci, timadzifunsa kuti: ‘Kodi “paradaiso” ni nkhani yongolota cabe? Ngati ni yongolota, n’cifukwa ciani anthu amacita nayo cidwi? Nanga kodi paradaiso ingakhaledi yeni-yeni?’

PARADAISO YAKALE

Kwa zaka zambili, anthu akhala akucita cidwi na nkhani ya paradaiso. Ambili anakhala ndi cidwi cimeneci cifukwa cakuti Baibo imachula za “munda ku Edeni, cakum’mawa.” N’ciani cinapangitsa mundawo kukhala wokongola kwambili? Baibo imatiuza kuti: “Yehova Mulungu anameletsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” Munda umenewo unali wokongola komanso malo abwino okhalamo. Copambana zonse n’cakuti panalinso “mtengo wa moyo pakati pa mundawo.”—Genesis 2:8, 9.

Kuwonjezela apo, nkhani ya m’Genesis imachula za mitsinje inayi yocokela m’mundawo. Iŵili mwa mitsinjeyo ikudziŵika mpaka lelo. Woyamba ni Hidekeli, umene lomba umachedwa Tigris, ndipo waciŵili ni Firate. (Genesis 2:10-14) Mitsinje iŵili imeneyi imathila madzi m’Nyanja ya Perisiya, kupitila m’dziko limene tsopano ni Iraq, dela la Perisiya wakale.

N’zosadabwitsa kuti paradaiso wa padziko lapansi amasonyezedwa m’zinthu zambili za cikhalidwe ca Aperisiya. Mwacitsanzo, kapeti ya Aperisiya ya m’zaka za m’ma 1500 ku Philadelphia Museum of Art ku Pennsylvania, m’dziko la America, anaikongoletsa mwa kusokelapo pikica yoonetsa munda wochingidwa wa mitengo na maluŵa. Mau a Ciperisiya akuti “munda wochingidwa” amatanthauzanso “paradaiso.” Ndipo pikica yolembedwa pa kapeti imeneyo, imayelekezela mmene munda wa Edeni wochulidwa m’Baibo unalili wokongola.

Kuzungulila dziko lonse lapansi, anthu a zinenelo na zikhalidwe zosiyana-siyana amakamba nkhani zokhudza paradaiso. Anthu atayamba kusamukila m’madela osiyana-siyana padziko lapansi, iwo anasunga nkhani zokhudza munda weni-weni wa Edeni. Ndiyeno pambuyo pa zaka mahandiledi ambili, nkhanizo zinasakanizana ndi zikhulupililo ndi nthano zawo. Ngakhale masiku ano, mwacizoloŵezi anthu amachula malo okongola kwambili kuti paradaiso.

KUFUNA-FUNA PARADAISO

Akatswili ofufuza malo amakamba kuti anapeza malo amene panali paradaiso wakale. Mwacitsanzo, Charles Gordon, mkulu wa asilikali a Britain, anayendela dziko la Seychelles mu 1881. Iye anacita cidwi kwambili ataona malo ena okongola m’dzikomo ochedwa Vallée de Mai, amene tsopano ni malo a zacilengedwe ofunika kwambili padziko lonse. Anakamba kuti malowo ni munda wa Edeni. Mu 1492, Christopher Columbus, katswili wofufuza malo waciitaliyani, anaona kuti watsala pang’ono kupeza munda wa Edeni atafika pa cisumbu ca Hispaniola, cimene tsopano ni maiko a Dominican Republic ndi Haiti.

Buku ina ya mbili yamakono yakuti Mapping Paradise, ili ndi nkhani zokhudza mamapu akale oposa 190. Ambili amaonetsa mapikica a Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Imodzi mwa mamapu amenewo kaonekedwe kake n’kacilendo, ndipo ali pa mpukutu wa m’zaka za m’ma 1200 wochedwa Beatus wa ku Liébana. Pamwamba pa mapuwo pali kapikica koonetsa paradaiso. Palinso mitsinje inayi yocedwa “Tigrisi,” “Firate,” “Pisoni,” na “Geon” ku makona anayi a mapuwo. Mitsinjeyo ikuganizilidwa kuti ikuimila kufalikila kwa Cikhristu ku mbali zinayi za dziko lapansi. Mapikica a conco amaonetsa kuti ngakhale kuti malo amene panali Paradaiso yeni-yeni sadziŵika, zimene amakumbukila zokhudza paradaiso ameneyo zakhalabe zocititsa cidwi kuyambila kale.

John Milton, mzungu wina wolemba ndakatulo wa m’zaka za m’ma 1600, amadziŵika cifukwa ca ndakakuto yake yakuti Paradise Lost (Paradaiso Wotaika), yozikidwa pankhani ya m’buku ya Genesis yokhudza kucimwa kwa Adamu ndi kuthamangitsidwa kwake m’munda wa Edeni. M’ndakatulo imeneyo, anaunikila lonjezo lakuti anthu adzabwezeletsedwa ku moyo wamuyaya padziko lapansi, pokamba kuti: “Panthawiyo, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso.” Pambuyo pake, Milton analembanso ndakatulo ina yakuti Paradise Regained (Paradaiso Wobwezeletsedwa).

KUSINTHA KWA ZINTHU

N’zoonekelatu kuti nkhani yokhudza paradaiso wotaika padziko lapansi yakhala yodziŵika kwambili m’mbili yonse ya anthu. Nanga n’cifukwa ciani anthu masiku ano akuinyalanyaza? Malinga na buku yakuti Mapping Paradise, cifukwa n’cakuti “akatswili a zacipembedzo . . . alibe cidwi cofuna kudziŵa malo kumene paradaiso anali.”

Anthu ambili m’machechi amaphunzitsidwa kuti kwawo kweni-kweni kokakhala ni kumwamba, osati m’paradaiso padziko lapansi. Komabe, pa Salimo 37:29 Baibo imati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” Popeza dziko lathu lapansi si paradaiso masiku ano, kodi tingatsimikize bwanji kuti lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwa?

DZIKO LONSE LAPANSI LIDZAKHALADI PARADAISO

Yehova Mulungu, amene anapanga Paradaiso woyambilila, analonjeza kuti adzabwelezeletsa zimene zinataika. Kodi adzacita bwanji zimenezi? Kumbukilani kuti Yesu anatiphunzitsa kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumuwo ni boma imene idzalamulila dziko lonse lapansi, ndipo Mfumu yake ni Yesu Khristu. Udzaloŵa m’malo ulamulilo uliwonse wa anthu. (Danieli 2:44) Ufumuwo ukadzayamba kulamulila, cifunilo ca Mulungu cokhudza paradaiso padziko lapansi ‘cidzacitika.’

Kale, mneneli Yesaya anauzilidwa kulemba mmene zinthu zidzakhalila m’Paradaiso wolonjezedwa. Mavuto onse amene amazunza anthu masiku ano adzacotsedwapo. (Yesaya 11:6-9; 35:5-7; 65:21-23) Tikupemphani kupatulako mamineti ocepa kuti muŵelenge mavesi amenewo m’Baibo yanu. Kucita zimenezo kudzakupatsani cidalilo pa zinthu zimene Mulungu wasungila anthu omvela. Anthu amene adzapezekamo adzasangalala ndi paradaiso komanso ubwenzi na Mulungu, zimene Adamu anataya.—Chivumbulutso 21:3.

N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti Paradaiso imene tiyembekezela padziko lapansi si maloto koma ni yeni-yeni? Baibo imati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, Koma dziko lapansi analipeleka kwa ana a anthu.” Conco, Paradaiso padziko lapansi ni cinthu cimene “Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.” (Salimo 115:16; Tito 1:2) Ha! n’ciyembekezo cokondweletsa cotani nanga cimene Baibo imatipatsa—Paradaiso wamuyaya!