Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?
Pamela atayamba kudwala matenda aakulu, anapita kucipatala. Komanso anapemphela kwa Mulungu kuti amuthandize kupilila. Kodi kupemphela kunamuthandiza?
Pamela anati: “Pamene n’nali kulandila thandizo pa matenda anga a khansa, nthawi zambili n’nali kukhala na mantha kwambili. Koma nikapemphela kwa Yehova Mulungu, mtima unali kukhala m’malo. Sin’nali kukhalanso na mantha kwambili. Nimamvelabe kuŵaŵa nthawi zonse. Koma pemphelo limanithandiza kucepetsa nkhawa. Anthu akanifunsa kuti, ‘Mumvelako bwanji?’ Nimawayankha kuti, ‘Sinimvela bwino, koma ndine wacimwemwe!’”
Koma sikuti timafunika kucita kuyembekezela kukumana na mavuto aakulu kuti tipemphele. Tonsefe timakumana na mavuto, aakulu komanso aang’ono, ndipo nthawi zambili timadziŵa kuti tifunika thandizo kuti tipilile mavutowo. Kodi pemphelo lingatithandize?
Baibo imati: “Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Salimo 55:22) Kodi si zolimbikitsa zimenezi? Inde, n’zolimbikitsadi! Ndiye kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji? Ngati mwapemphela kwa Mulungu m’njila yoyenela, iye adzakupatsani zimene mufunikila kuti mukwanitse kupilila mavuto anu.—Onani bokosi yakuti ““ Zimene Mudzalandila Ngati Mupemphela.”