Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 1 2018 | Kodi Baibo Ikali Yothandiza Masiku Ano?

KODI BAIBO IKALI YOTHANDIZA MASIKU ANO?

Popeza kuti pali cidziŵitso cambili-mbili m’dziko lamakono, kodi Baibo ni yakale kwambili cakuti siingatithandize masiku ano? Baibo imakamba kuti:

“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

Kope ino ya Nsanja ya Mlonda ipeleka umboni woonetsa kuti Baibo ingatithandize m’mbali zonse za umoyo wathu.

 

Kodi Malangizo a m’Baibo Akali Othandiza Masiku Ano?

Poona malangizo onsewa a panthawi yake, kodi pangakhale cifukwa coŵelengela malangizo a m’Baibo, buku imene inalembedwa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo?

Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse

Mfundo za m’Baibo siziloŵedwa m’malo, ndipo ziphunzitso zake n’zozikidwa pa mfundo zimene n’zothandiza nthawi zonse.

Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?

Baibo si buku la sayansi, koma zimene limakamba zokhudza sayansi zingakucititseni cidwi.

1 Thandizo pa Kupewa Mavuto

Onani mmene nzelu za Mulungu zathandizila anthu kupewa mavuto ena aakulu.

2 Thandizo pa Kuthetsa Mavuto

Baibo ingatithandize kupeza nzelu zothetsela mavuto okhalitsa ndi othetsa nzelu, mavuto monga kukhala na nkhawa mopambanitsa, kuzengeleza kucita zinthu, na kusungulumwa.

3 Thandizo pa Kupilila Mavuto

Nanga bwanji za mavuto amene sitingawapewe kapena kuwathetsa, monga matenda osacilitsika komanso imfa?

Baibo na Tsogolo Lanu

Mau a Mulungu angatithandize kulimbana na mavuto amene tonsefe timakumana nawo tsiku na tsiku m’dziko loipali. Koma Baibo imatithandizanso m’njila zina. Imatithandiza kudziŵa bwino zam’tsogolo.

Muganiza Bwanji?

Onani zimene ena amakhulupilila, komanso zimene Baibo imaphunzitsa ponena za funso limeneli.