Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Tizisonyezana Cikondi Ceni-ceni m’Zocita Zathu”

“Tizisonyezana Cikondi Ceni-ceni m’Zocita Zathu”

“Tisamakondane ndi mau okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceni-ceni m’zocita zathu.”—1 YOH. 3:18.

NYIMBO: 72, 124

1. Kodi cikondi capamwamba kwambili n’citi? Nanga n’cifukwa ciani takamba conco? (Onani pikica pamwambapa.)

CIKONDI cozikidwa pa mfundo za m’Baibo (a·gaʹpe) ni mphatso yocokela kwa Yehova. Iye ndiye Gwelo la cikondi cimeneci. (1 Yoh. 4:7) Cikondi cimeneci ndiye capamwamba kwambili. Cikondi ca a·gaʹpe cimaphatikizapo kukhala wokoma mtima ndi waubwenzi. Koma cimaonekela kwambili mwa zocita zathu zoonetsa kuti timaganizila anthu ena. Buku lina linakamba kuti, cikondi ca a·gaʹpe “cimaonekela kwambili mwa zimene munthu amacita.” Tikamaonetsa ena cikondi copanda dyela kapena ngati ena ationetsa cikondi cimeneci, timakhala na umoyo waphindu, komanso wodzala na cimwemwe.

2, 3. Kodi Yehova waonetsa bwanji cikondi copanda dyela kwa anthu?

2 Yehova anaonetsa kuti amakonda anthu ngakhale asanalenge Adamu na Hava. Iye analenga dziko kuti tikhalepo kwamuyaya. Anaikamo zonse zofunikila kuti tikhale na moyo, na kuti tizikhala osangalala. Yehova anacita zonsezi cifukwa cotikonda, osati kuti apindulepo kenakake. Iye anaonetsanso cikondi copanda dyela mwa kupatsa Adamu na Hava ciyembekezo cokhala na moyo wosatha m’Paradaiso amene anawakonzela.

3 Adamu na Hava atapanduka, Yehova anacita cinthu cacikulu kwambili coonetsa kuti ali na cikondi copanda dyela. Iye anakonza zakuti awombole mbadwa za anthu aŵili opandukawo, podziŵa kuti ena mwa ana awo adzayamikila cikondi cake. (Gen. 3:15; 1 Yoh. 4:10) Ndipo pamene Yehova analonjeza za Mpulumutsi, kwa iye zinali monga kuti nsembeyo yapelekedwa kale. Ndiyeno, patapita zaka 4,000, Yehova modzimana anapeleka nsembe yamtengo wapatali ya Mwana wake wobadwa yekha kuti awombole anthu. (Yoh. 3:16) Timam’yamikila kwambili Yehova cifukwa cotionetsa cikondi copanda dyela cimeneci.

4. N’ciani cionetsa kuti n’zotheka anthu opanda ungwilo kuonetsa cikondi copanda dyela?

4 Timakwanitsa kuonetsa cikondi codzimana cifukwa Mulungu anatilenga m’cifanizilo cake. Koma cifukwa ca ucimo umene tinatengela kwa makolo athu, cimakhala covuta kwa ise kuonetsa cikondi. Ngakhale n’conco, n’zotheka ndithu kuonetsa khalidweli. Abele anaonetsa cikondi cake pa Mulungu mwa kupeleka nsembe zinthu zabwino kwambili zimene anali nazo. (Gen. 4:3, 4) Nayenso Nowa anaonetsa kuti anali kukondadi anthu mwa kuwalalikila uthenga wa Mulungu kwa zaka zambili, ngakhale kuti sanali kulabadila. (2 Pet. 2:5) Panthawi ina, Mulungu analamula Abulahamu kuti apeleke mwana wake Isaki nsembe. Abulahamu anaonetsa kuti anali kukonda Mulungu ngako, mwa kulolela kucita zimenezo ngakhale kuti anali kum’konda mwanayo. (Yak. 2:21) Molingana ndi amuna okhulupilika amenewa, na ise tifunika kuonetsa cikondi, ngakhale kuti nthawi zina zingakhale zovuta.

CIKONDI CENI-CENI NA CIKONDI CACINYENGO

5. Fotokozani njila zimene tingaonetsele cikondi ceni-ceni.

5 Baibo imakamba kuti tisamakondane “ndi mau okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceni-ceni m’zocita zathu.” (1 Yoh. 3:18) Kodi izi zitanthauza kuti sitingaonetse cikondi mwa zokamba zathu? Iyai. (1 Ates. 4:18) Koma zitanthauza kuti tisamaonetse cikondi m’mau cabe, maka-maka ngati munthu wina afunikila thandizo. Mwacitsanzo, Mkhristu mnzathu akasoŵa zinthu zofunikila pa umoyo, tingafunike kum’thandiza, osati kungokamba mau a mafuno abwino. (Yak. 2:15, 16) Mofananamo, kukonda Yehova ndi anansi athu kumatilimbikitsa kugwila nchito yolalikila mwakhama, osati kungopempha Mulungu ‘kuti atumize anchito okakolola.’—Mat. 9:38.

6, 7. (a) Kodi “cikondi copanda cinyengo” cimatanthauza ciani? (b) Fotokozani zitsanzo za cikondi cacinyengo.

6 Mtumwi Yohane analemba kuti tifunika kusonyezana cikondi “ceni-ceni m’zocita zathu.” Conco, cikondi cathu sicifunika ‘kukhala caciphamaso,’ koma cifunika kukhala “copanda cinyengo.” (Aroma 12:9; 2 Akor. 6:6) Izi zitanthauza kuti cikondi ceni-ceni cimakhala cocokela pansi pamtima, osati conamizila cabe. Mwina tingafunse kuti, ‘Kodi cikondi caciphamaso n’cikondidi?’ Iyayi. N’cinyengo cabe.

7 Onani zitsanzo zina izi za cikondi caciphamaso. M’munda wa Edeni, Satana anaonetsa monga kuti anali kufunila Hava zabwino, koma m’ceni-ceni zocita zake zinali zadyela ndi zacinyengo. (Gen. 3:4, 5) M’nthawi ya mfumu Davide, Ahitofeli anaonetsa kuti ubwenzi wake na mfumuyo unali waciphamaso. Panthawi inayake, iye anagwilizana ndi adani a Davide poganiza kuti angapeze phindu. (2 Sam. 15:31) Mofananamo, masiku ano anthu ampatuko ndi ena amene amayambitsa magaŵano mumpingo, amakamba “mau okopa ndi acinyengo,” n’colinga cakuti azioneka ngati acikondi, pamene colinga cawo ceni-ceni n’cadyela.—Aroma 16:17, 18.

8. Ni funso liti limene tiyenela kudzifunsa?

8 Anthu amaonetsa cikondi caciphamaso pofuna kupusitsa anzawo. Koma Yehova sangam’pusitse. Ndipo Yesu anakambilatu kuti anthu a ciphamaso adzalandila “cilango coopsa.” (Mat. 24:51) Monga atumiki a Yehova, sitifuna kuonetsa cikondi caciphamaso. Komabe, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nthawi zonse nimaonetsa cikondi ceni-ceni, osati cadyela kapena cacinyengo?’ Tiyeni tikambilane zinthu 9 zimene tingacite zoonetsa kuti tili na cikondi “copanda cinyengo.”

MMENE TINGAONETSELE “CIKONDI CENI-CENI M’ZOCITA ZATHU”

9. Kodi cikondi ceni-ceni cimatisonkhezela kucita ciani?

9 Muzitumikila mokondwela ngakhale kuti ena saona zimene mumacita. Tifunika kuyesetsa kucitila abale athu zinthu zabwino ‘mwamseli,’ kapena kuti mosadzionetsela kwa ena. (Ŵelengani Mateyu 6:1-4.) Hananiya na Safira analephela kucita zimenezi. M’malo mocita copeleka mwamseli, iwo ananama kuti apeleka ndalama zonse zimene anagulitsa munda, ndipo analangiwa cifukwa cocita zinthu mwacinyengo. (Mac. 5:1-10) Mosiyana na zimenezi, cikondi ceni-ceni cimatisonkhezela kutumikila abale athu mwacimwemwe, popanda kudzionetsela kapena kufuna kuchukilapo. Mwacitsanzo, abale amene amathandiza Bungwe Lolamulila kukonza cakudya cauzimu, saulula kuti ndiwo amacita zimenezo. Iwo safuna kudzichukitsa. Komanso saulula zimene amaseŵenzelapo.

10. Fotokozani mmene tingakhalile patsogolo poonetsa ulemu kwa ena.

10 Khalani patsogolo poonetsa ulemu kwa ena. (Ŵelengani Aroma 12:10.) Yesu anapeleka citsanzo cabwino pankhani yolemekeza ena mwa kucita nchito zotsika kwambili. (Yoh. 13:3-5, 12-15) Pamafunika khama kuti tikhaledi odzicepetsa na kuonetsa ulemu kwa ena mwanjila imeneyi. Ngakhale atumwi, poyamba sanamvetsetse cifukwa cake Yesu anawasambitsa mapazi. Koma anamvetsetsa atalandila mzimu woyela. (Yoh. 13:7) Tingaonetse kuti timalemekeza ena mwa kupewa kudziona monga ndise ofunika ngako cifukwa ca maphunzilo athu, cuma, kapena utumiki na udindo umene tili nawo m’gulu la Yehova. (Aroma 12:3) Komanso, m’malo mocitila kaduka munthu amene akupatsidwa ulemu pa zimene anacita, tiyenela kukondwela naye limodzi ngakhale tiona kuti nafenso tinafunika kulandila ulemu wofananawo. Sitiyenelanso kucita nsanje olo kuti tinam’thandiza pa zimene anacitazo.

11. N’cifukwa ciani ciyamikilo cathu ciyenela kukhala cocokela pansi pa mtima?

11 Muziyamikila abale mocokela pansi pa mtima. Tiyenela kufuna-funa mipata yoyamikila ena cifukwa kucita zimenezi ‘kumalimbikitsa.’ (Aef. 4:29) Komabe, ciyamikilo cathu ciyenela kukhala cocokela pansi pa mtima. Apo ayi, ndiye kuti tikumugwila m’maso munthu kapena tikuopa kumupatsa uphungu. (Miy. 29:5) Kuyamikila munthu koma tikakhala kuseli n’kumamunena, ni cinyengo. Mtumwi Paulo anapewa khalidwe limeneli, ndipo anapeleka citsanzo cabwino pankhani yoonetsa cikondi ceni-ceni poyamikila ena. Mwacitsanzo, anayamikila Akhristu a ku Korinto moona mtima pa zimene anali kucita bwino. (1 Akor. 11:2) Koma akaona kuti pena pake sanacite bwino, anali kuwauza mokoma mtima ndi momveka bwino cifukwa cake anafunika kuwongolela.—1 Akor. 11:20-22.

Kupeleka thandizo kwa abale athu ovutika ni njila imodzi yoonetsela kuti timawakonda, ndipo ndise oceleza (Onani palagilafu 12)

12. Kodi cikondi ceni-ceni tingacionetse bwanji poceleza ena?

12 Khalani woceleza. Yehova anatilamula kuti tiziceleza abale na alongo athu ndi kuwapatsako zinthu zofunikila. (Ŵelengani 1 Yohane 3:17.) Komabe, tiyenela kucita zimenezo na zolinga zabwino, osati zadyela. Tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimakonda kuceleza mabwenzi anga okha-okha, anthu ochuka, ndi aja amene nimaona kuti nthawi ina adzanicitilako zabwino monga zimene nawacitila? Kapena nimayesetsa kupeza mipata yothandiza abale na alongo amene siniwadziŵa bwino kapena amene ni osoŵa?’ (Luka 14:12-14) Komanso bwanji ngati Mkhristu mnzathu wagwa m’mavuto azacuma cifukwa cosayendetsa bwino zinthu kapena ngati sanayamikile pa zabwino zimene tinamucitila? Zikakhala conco, tiyenela kutsatila malangizo akuti: “Muzicelezana popanda kudandaula.” (1 Pet. 4:9) Ngati titsatila malangizo amenewa, tidzapeza cimwemwe cimene cimabwela cifukwa copatsa ena zinthu tili na colinga cabwino.—Mac. 20:35.

13. (a) N’cifukwa ciani nthawi zina zingakhale zovuta kuthandiza ofooka? (b) N’zinthu ziti zimene tingacite kuti tithandize ofooka?

13 Muzithandiza ofooka. Tingaonetse kuti tilidi na cikondi ceni-ceni ngati titsatila lamulo la m’Baibo lakuti “thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14) Ngakhale kuti abale na alongo ambili ofooka pambuyo pake amalimba m’cikhulupililo, ena timafunika kupitilizabe kuwathandiza moleza mtima. Tingacite zimenezo mwa kuwauzako mfundo zolimbikitsa za m’Malemba, kuwapempha kuti tiyende nawo mu ulaliki, kapena kuwamvetsela pamene afotokoza mavuto awo. Cinanso, si bwino kumangoganizila za kuti m’bale cite ni “wolimba” kapena mlongo cite ni “wofooka.” Tifunika kukumbukila kuti tonse tili na zofooka, ndi kuti pali zinthu zina zimene timacita bwino. Ngakhale mtumwi Paulo anavomeleza zofooka zake. (2 Akor. 12:9, 10) Conco, tonse timafunikila thandizo la Akhristu anzathu.

14. Tingacite ciani kuti tikhalebe pamtendele na abale athu?

14 Muzikhazikitsa mtendele. Timayesetsa kukhala mwamtendele ndi abale na alongo athu ngakhale pamene atilakwila. (Ŵelengani Aroma 12:17, 18.) Kupepesa kungathandize kuthetsa mkwiyo, koma sikufunika kukhala kwaciphamaso. Mwacitsanzo, m’malo mokamba kuti, “Pepani kuti mwakhumudwa,” mungakambe kuti, “Pepani kuti zimene nakamba zakukhumudwitsani.” Komanso, mtendele ni wofunika ngako m’banja. Mwamuna na mkazi sayenela kuonetsa ngati kuti amakondana akakhala pagulu, koma akakhala aŵili n’kumanyozana, osakambitsana, kapena kumenyana kumene.

15. Tingaonetse bwanji kuti takhululuka na mtima wonse?

15 Muzikhululukila ena na mtima wonse. Timakhululukila munthu mwa kuiŵalako zimene watilakwila na kusamusungila mkwiyo. Mwa ‘kulolelana m’cikondi ndi kuyesetsa na mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele,’ tingakhululukile na mtima wonse anthu amene anatilakwila mosadziŵa. (Aef. 4:2, 3) Kuti tikhululukile ena mocokela pansi pa mtima, tiyenela kupewa ‘kusunga zifukwa.’ (1 Akor. 13:4, 5) Kusungila munthu cakukhosi, kungawononge ubwenzi wathu ndi m’bale kapena mlongo wathu. Koma coopsa kwambili, kungawononge ubwenzi wathu na Yehova. (Mat. 6:14, 15) Tingaonetsenso kuti takhululuka na mtima wonse mwa kupemphelela anthu amene atilakwila.—Luka 6:27, 28.

16. Kodi maudindo tiyenela kuwaona bwanji m’gulu la Yehova?

16 Muziika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zanu. Tikalandila udindo kapena utumiki wina wake m’gulu la Yehova, tifunika kuuona monga mwayi wathu woonetsa kuti tili na cikondi ceni-ceni mwa kupewa ‘kudzifunila zopindulitsa ife tokha basi, koma zopindulitsanso ena.’ (1 Akor. 10:24) Mwacitsanzo, pa misonkhano ikulu-ikulu, akalinde amafika mwamsanga ena asanafike. Abale amenewa saona udindo wawo monga mwayi wodzipezela malo abwino okhalapo na mabanja awo. M’malomwake, ambili mwa iwo amakhala pa malo ena alionse, ngakhale amene si abwino kweni-kweni m’cigawo cimene apatsidwa kuti ayang’anile. Kuika zofuna za ena patsogolo mwanjila imeneyi, kumaonetsa kuti ali na cikondi copanda dyela. Ifenso tingacite bwino kutengela citsanzo cawo cabwino.

17. Kodi cikondi ceni-ceni cimalimbikitsa munthu kucita ciani ngati wacita chimo lalikulu?

17 Kuulula macimo na kuwaleka. Akhristu ena amene anacita chimo lalikulu amabisa cifukwa coopa kucita manyazi kapena kukhumudwitsa ena. (Miy. 28:13) Koma kubisa chimo n’kusoŵa cikondi cifukwa sikuvulaza cabe wolakwayo, koma kumavulazanso Akhristu ena. Kungalepheletse mzimu woyela kugwila nchito bwino mumpingo. Komanso kungasokoneze mtendele mumpingo. (Aef. 4:30) Koma cikondi ceni-ceni cimalimbikitsa Mkhristu amene wacita chimo lalikulu kuulula chimolo kwa akulu kuti amupatse thandizo.—Yak. 5:14, 15.

18. N’cifukwa ciani kukhala na cikondi ceni-ceni n’kofunika ngako?

18 Cikondi ni khalidwe lalikulu kwambili pa makhalidwe onse. (1 Akor. 13:13) Cimatidziŵikitsa kuti ndise otsatila a Yesu. Komanso, kukhala na cikondi kumaonetsa kuti tikutengela Yehova, Gwelo la cikondi. (Aef. 5:1, 2) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati. . . ndilibe cikondi, sindili kanthu.” (1 Akor. 13:2) Conco, tiyeni tipitilize kuonetsana “cikondi ceni-ceni m’zocita zathu,” osati na “mau okha.”