Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Napindula Cifukwa Coyenda ndi Anthu Anzelu

Napindula Cifukwa Coyenda ndi Anthu Anzelu

TSIKU lina m’maŵa ku Brookings, m’dela la South Dakota, ku U.S.A, kunazizila, ndipo ine n’nadziŵilatu kuti posacedwa kudzazizila kwambili. Koma mungadabwe kuti patsikulo, ine ndi anzanga ena tinali m’nyumba ya pa famu yosungilamo zinthu, imene munali mozizila. Tinaimilila pafupi ndi cibafa cacikulu comwelamo ziweto, cimene munalinso madzi ozizila. Lekani nikuuzeni zina zokhudza umoyo wanga kuti mudziŵe cifukwa cake n’napezeka pa malo amenewa.

MBILI YA BANJA LATHU

Atate ndi akulu awo a Alfred

N’nabadwa pa 7 March, mu 1936. Tinabadwa ana anayi m’banja lathu, ndipo ine ndine wothela. Tinali kukhala pa famu yaing’ono kum’maŵa kwa South Dakota. Nchito yaikulu imene tinali kugwila pa banja lathu ni yaulimi, koma sikuti ndiyo inali nchito yofunika kwambili pa umoyo wathu. Makolo anga anabatizika n’kukhala Mboni za Yehova mu 1934. Iwo anadzipeleka kwa Atate wawo wakumwamba, Yehova, ndipo kucita cifunilo ca Mulungu ndiye cinali cinthu cofunika kwambili pa umoyo wawo. Atate, dzina lawo a Clarence, ndi akulu awo, a Alfred, onse anatumikilapo monga mtumiki wa mpingo (tsopano mgwilizanitsi wa bungwe la akulu) mu mpingo wathu waung’ono ku Conde, m’dela la South Dakota.

Pa banja lathu, tinali kukonda kusonkhana ndi kupita ku nyumba ndi nyumba kukauzako ena za ciyembekezo ca m’Baibo ca tsogolo labwino. Citsanzo cabwino ca makolo athu ndiponso zimene anali kutiphunzitsa, zinatithandiza anafe kuti tiyambe kukonda Mulungu. Ine ndi mlongo wanga, Dorothy, tinakhala ofalitsa uthenga wa Ufumu pamene tinali na zaka 6. Mu 1943, n’naloŵa Sukulu ya Ulaliki, imene inangoyamba kumene.

Kucita upainiya mu 1952

Tinali kukondanso kupezeka pa misonkhano yadela ndi yacigawo. Mwacitsanzo, mu 1949, M’bale Grant Suiter ndiye anali mlendo pa msonkhano wacigawo umene unacitikila ku Sioux Falls, m’dela la South Dakota. Nimakumbukilabe nkhani imene iye anakamba, ya mutu wakuti, “Ni M’mbuyo mwa Alendo!” Iye anagogomeza mfundo yakuti, Akhristu onse odzipeleka afunika kugwila nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi mtima wonse. Nkhani imeneyi inanilimbikitsa kuti nidzipeleke kwa Yehova. Conco, pa msonkhano wadela wotsatila umene unacitikila ku Brookings, n’nabatizika. N’cifukwa cake n’napezeka m’nyumba yozizila ya pa famu imene nachula poyamba paja. N’nali kuyembekezela kubatizika. Ine ndi anzanga atatu tinabatizikila m’cibafa cija pa November 12, 1949.

Pambuyo pake, n’naganiza zoyamba upainiya. N’nayamba upainiyawo pa 1 January, 1952, pamene n’nali ndi zaka 15. Baibo imati: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” Panali acibale ambili amene ananilimbikitsa kuyamba upainiya. (Miy. 13:20) Akulu awo a atate, a Julius, amene anali ndi zaka 60, ndiwo anali mnzanga wocita naye upainiya. Ngakhale kuti tinali kusiyana ndi zaka zambili, tinali kusangalala kucitila pamodzi utumiki. N’napeza nzelu zoculuka kwa iwo cifukwa anali kudziŵa zambili. Patapita nthawi yocepa, Dorothy nayenso anakhala mpainiya.

N’NALIMBIKITSIDWA NDI OYANG’ANILA DELA

Pamene n’nali wacicepele, makolo anga nthawi zambili anali kuitana oyang’anila dela ndi akazi awo kuti tikakhale nawo kunyumba kwathu kwakanthawi. Mmodzi mwa woyang’anila dela amene ananithandiza kwambili ni M’bale Jesse Cantwell ndi mkazi wake, Lynn. Ndipo cimodzi mwa zinthu zimene zinanithandiza kuti niyamba upainiya ndi cilimbikitso cawo. Cikondi cimene ananionetsa cinanilimbikitsa kukhala na zolinga zauzimu. Nthawi zina akamatumikila mipingo ya pafupi ndi kwathu, anali kunipempha kuti nipite nawo mu ulaliki. Nthawi imeneyo inali yosangalatsa ngako.

Pambuyo pake, M’bale Bud Miller ndi mkazi wake, Joan, anayamba kutumikila m’dela lathu monga woyang’anila dela. Panthawiyo, n’nali na zaka 18, ndipo n’nali kuyang’anizana ndi nkhani yongena usilikali. Poyamba, bungwe lolemba anthu usilikali m’dela lathu, linaniika m’gulu la anthu ofunika kuloŵa usilikali. N’naona kuti zimenezo zinali zosemphana ndi lamulo la Yesu lakuti otsatila ake safunika kutengako mbali m’zandale. Ine n’nali kufuna kuti nizigwila nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Yoh. 15:19) Conco, n’napita kukapempha akulu-akulu a bungwelo kuti anipatse mwayi wodziŵika monga mtumiki wa Mulungu.

N’nakondwela kuona kuti M’bale Miller wadzipeleka kupita nane kukakambilana ndi akulu-akulu a bungwelo. Mwacibadwa, iye anali munthu wansangala ndi wolimba mtima. N’nalimbikitsidwa kwambili kukhala ndi m’bale wauzimu amene anali wokonzeka kunithandiza. Pambuyo pokambilana ndi akulu-akulu a bungwelo, m’caka comweco ca 1954 anavomeleza kuniona monga mtumiki wa Mulungu. Zimenezi zinanipatsa mwayi wokwanilitsa colinga cina cauzimu.

Naimilila pa galimoto ya pa famu, nitangofika kumene ku Beteli

Patapita nthawi yocepa, n’naitanidwa kuti nikatumikile ku Beteli, ndipo n’nayamba kuseŵenzela ku Watchtower Farm, m’dela la Staten Island, ku New York. N’natumikila pa famu imeneyi kwa zaka pafupi-fupi zitatu. N’nali kusangalala kwambili ndi utumiki kumeneko cifukwa tinali kuseŵenza ndi anthu ambili anzelu.

UTUMIKI WA PA BETELI

Tili pa nyumba ya wailesi ya WBBR pamodzi na M’bale Franz

Pa famu ya ku Staten Island panali nyumba ya wailesi ya Mboni yochedwa WBBR. Mboni za Yehova zinali kugwilitsila nchito wailesi imeneyi kuyambila mu 1924 mpaka mu 1957. Pa famuyo panali kuseŵenzela atumiki a pa Beteli okwana cabe 15 mpaka 20. Ambili amene tinali kumeneko tinali acicepele ndi osadziŵa zambili. Koma tinalinso ndi m’bale wacikulile Eldon Woodworth, amene anali wodzozedwa. Iye anaonetsadi kuti anali munthu wanzelu. Anali kutikonda monga tate ŵathu ndipo zimenezi zinatilimbikitsa mwauzimu. Nthawi zina tikakhumudwitsana cifukwa ca kupanda ungwilo, M’bale Woodworth anali kukamba kuti, “Zimene Ambuye acita n’zocititsa cidwi ngakhale kuti akuseŵenzetsa anthu opanda ungwilo.”

M’bale Harry Peterson anali wacangu kwambili pa ulaliki

Tinalinso na mwayi kukhala ndi m’bale Frederick W. Franz. Iye anali wanzelu ndi wodziŵa bwino Malemba ndipo anali citsanzo cabwino kwa tonse. M’bale Franz anali kutikonda tonsefe. M’bale Harry Peterson ndi amene anali kutiphikila. Zinali zosavuta kwa ife kumuchula ndi dzina lake lotsiliza lakuti Peterson m’malo mochula dzina lake leni-leni, lakuti Papargyropoulos. M’bale ameneyu analinso wodzozedwa ndipo anali wacangu panchito yolalikila. M’baleyu anali kugwila mokhulupilika nchito yake pa Beteli, koma sanali kunyalanyaza nchito yolalikila. Anali kugaŵila magazini ambili-mbili pamwezi. Analinso kudziŵa bwino Malemba cakuti anali kuyankha mafunso ambili amene tinali nawo.

N’NAPHUNZILA ZAMBILI KWA ALONGO ANZELU

Zokolola za pa famu tinali kuzikonza ndi kuzisungila pa famu pomwepo. Caka ciliconse, tinali kukonza ndi kusunga zipatso ndi ndiwo zamasamba zodzaza zitini 45,000 monga cakudya ca banja la Beteli. Panthawi imeneyi, n’nali na mwayi wotumikila ndi mlongo Etta Huth, amene anali mayi wanzelu. Iye ndi amene anali kutipatsa malangizo pa nchito yokonza ndi kusunga zipatso ndi ndiwo. Nyengo yogwila nchito imeneyi ikakwana, alongo a kufupi ndi famuyo anali kubwela kudzaseŵenza nafe, ndipo mlongo Etta anali kuwayang’anila. Ngakhale kuti mlongo Etta anali kucita mbali yaikulu pa nchitoyo, iye anapeleka citsanzo cabwino pankhani yolemekeza abale amene anali kuyang’anila pa famupo. N’nali kumuona kuti n’citsanzo cabwino pankhani yogonjela otsogolela m’gulu.

Ine ndi Angela, tili na mlongo Etta Huth

Angela Romano ni mmodzi wa alongo amene anali kubwela kudzaseŵenza nafe. Mlongo Etta anam’thandizako Angela akali watsopano m’coonadi. Conco, pamene n’nali kutumikila pa Beteli, m’pamene n’nakumana ndi Angela, mlongo wanzelu amene tsopano natumikila naye kwa zaka 58. Ine ndi Angie tinakwatilana mu April 1958, ndipo monga banja, tasangalala ndi mautumiki osiyana-siyana. M’zaka zonsezi, Angie wakhala wokhulupilika kwambili kwa Yehova. Zimenezi zapangitsa banja lathu kukhala lolimba. Nimam’dalila kwambili ngakhale tikumane na mavuto aakulu.

NCHITO YA UMISHONALE NDI YOYENDELA DELA

Wailesi ya WBBR imene inali ku Staten Island itagulitsidwa mu 1957, n’nakatumikilako ku Beteli ya ku Brooklyn kwakanthawi. Koma n’nacoka pa Beteli n’takwatila Angie. Kwa zaka pafupi-fupi zitatu, tinali kucita upainiya ku Staten Island. Komanso kwa nthawi yocepa, ndinaseŵenzako kwa amene anagula wailesi ya WBBR, imene iwo anayamba kuicha WPOW.

Ine ndi Angie tinayesetsa kukhala na umoyo wosalila zambili kuti tikhale okonzeka kukatumikila kulikonse kumene tingafunike. Conco, mu 1961 atatipempha kuti tikatumikile monga apainiya apadela ku Falls City, m’dela la Nebraska, tinavomela. Titangoyamba utumiki umenewu, anatiitana kuti tikaloŵe Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku South Lansing, mumzinda wa New York. Panthawiyo, sukuluyi inali ya mwezi umodzi. Tinakondwela kwambili na sukuluyo ndipo tinali kuyembekezela kukagwilitsila nchito zimene tinaphunzila tikabwelela ku Nebraska. Koma mosayembekezela, tinalandilanso utumiki watsopano. Anatiuza kuti tikatumikile ku Cambodia monga amishonale. Titafika m’dziko lokongola limeneli, limene lili kum’mwela cakum’maŵa kwa Asia, tinaona ndi kumva zinthu zosiyana kwambili ndi zimene tinazoloŵela ndiponso tinali kudya zakudya zacilendo. Tinali ofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino m’dzikolo.

Koma m’dzikolo munabuka mavuto a zandale, ndipo tinasamukila ku South Vietnam. Mwatsoka lanji, patangopita zaka ziŵili n’nadwala matenda aakulu. Conco anatiuza kuti tibwelele kwathu. Kwa nthawi ndithu, n’nafunika kukhala osaseŵenza kuti mphamvu zibwelelemo, koma n’tacila, tinayambanso utumiki wa nthawi zonse.

Nili na Angela mu 1975, kuyembekezela kuti atifunse mafunso pa TV

Mu March 1965, tinapatsidwa mwayi wotumikila mipingo m’nchito yoyendela dela. Kwa zaka 33, ine ndi Angie tinali mu utumiki woyang’anila dela ndi zigawo. Tinalinso kusangalala ndi nchito yokonzekela misonkhano ikulu-ikulu. Nakhala nikuikonda kwambili misonkhano imeneyi, ndipo n’nali kusangalala kugwila nawo nchito yopanga makonzedwe okhudza misonkhanoyi. Pa zaka zocepa zimene tinakhala ku New York City, misonkhano ingapo yacigawo inacitikila ku Yankee Stadium.

KUBWELELA KU BETELI NDI MASUKULU OPHUNZITSA AKHRISTU

Monga mmene zimakhalila kwa abale ndi alongo ambili amene ali mu utumiki wa nthawi zonse wapadela, ine ndi Angie tinapatsidwa mautumiki atsopano ndiponso ovutilapo. Mwacitsanzo, mu 1995, n’napatsidwa nchito yophunzitsa abale m’Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Patapita zaka zitatu, tinaitanidwa kuti tikatumikile ku Beteli. N’nakondwela kubwelelanso kumene n’nayambila utumiki wanthawi zonse wapadela zaka zoposa 40 m’mbuyomo. Kwa kanthawi, n’natumikilako mu Dipatimenti ya Utumiki ndiponso monga mlangizi wa masukulu osiyana-siyana. Mu 2007, Bungwe Lolamulila linakonza zakuti masukulu amene anali kucitikila pa Beteli aziyang’anilidwa ndi Dipatimenti ya Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu. Ndipo kwa zaka ndithu, n’nali na mwayi wotumikila m’dipatimenti imeneyi monga woyang’anila.

M’zaka zaposacedwa, masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu asintha kwambili. Mwacitsanzo, mu 2008, kunayamba Sukulu ya Akulu. M’zaka ziŵili zotsatilapo, akulu oposa 12,000 analoŵa m’sukulu imeneyi ku Patterson ndi ku Beteli ya ku Brooklyn. Sukuluyi ikucitikabe m’madela ena ambili, ndipo abale ophunzitsidwa bwino ndi amene amatumikila monga alangizi. Mu 2010, Sukulu Yophunzitsa Utumiki inayamba kuchedwa Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila, ndipo panakhazikitsidwa sukulu yatsopano yochedwa Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Akristu Ali Pabanja.

Kuyambila m’caka ca utumiki ca 2015, masukulu aŵili amenewa anaphatikizidwa m’kupanga sukulu imodzi, imene imachedwa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Anthu oloŵa sukulu imeneyi angakhale apabanja, abale osakwatila, kapena alongo osakwatiwa. Abale ambili anakondwela atamva kuti sukuluyi idzayamba kucitika m’nthambi zambili. N’zokondweletsa kuona kuti mwayi woloŵa masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu ukuwonjezeka. Nimayamikila kwambili mwayi woonana ndi abale ndi alongo ambili amene amadzipeleka kukalandila maphunzilo amenewa.

Nikaganizila umoyo wanga kucokela pamene n’nali kuyembekezela kubatizika m’cibafa comwelamo ziweto cija, nimayamikila Yehova cifukwa ca anthu anzelu amene ananithandiza poyenda m’njila ya coonadi. Ena mwa anthu amenewa sanali a msinkhu wanga kapena a cikhalidwe colingana ni canga. Koma mumtima, anali anthu okonda Mulungu. Zocita zawo ndi kaganizidwe kawo zinali kuonetsa kuti anali kukonda kwambili Yehova. M’gulu la Mulungu, tili na abale na alongo ambili anzelu amene tingayende nawo. Izi n’zimene ine nakhala nikucita ndipo napindula ngako.

Nimakondwela kuonana ndi ophunzila ocokela m’maiko osiyana-siyana padziko lonse