Musamaone Cabe Maonekedwe a Munthu
DON, mmodzi wa Mboni za Yehova ku Canada, amayesetsa kulalikila anthu ovutika amene amakhala m’miseu. Don anafotokoza zokhudza mmodzi wa anthu amenewa. Iye anati: “Peter anali mmodzi wa anthu adothi kwambili okhala m’miseu. Anali woipa m’maonekedwe, ndipo anali kukonda kuopseza anthu. Anthu akafuna kum’thandiza, anali kukana.” Don anacita zinthu moleza mtima kwa zaka zoposa 14, kuti athandize munthu wosoŵa kokhala ameneyu.
Tsiku lina Peter anafunsa Don kuti: “Kodi iwe uvutikilanji na ine? Anthu onse amangonileka. N’cifukwa ciani umanidela nkhawa?” Don atamva zimenezo, mwanzelu anaseŵenzetsa malemba atatu poyankha Peter momufika pamtima. Coyamba, Don anafunsa Peter kuti akambe ngati adziŵa kuti Mulungu ali na dzina. Ndiyeno, anam’pempha kuti adziŵelengele yekha m’Baibo pa Salimo 83:18. Caciŵili, pofuna kumuonetsa cifukwa cake amamudela nkhawa, Don anauza Peter kuti aŵelenge pa Aroma 10:13, 14, pamene pamakamba kuti “aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Potsiliza, Don anaŵelenga Mateyu 9:36. Pambuyo pake anapempha Peter kuti adziŵelengele yekha vesiyo. Vesi imeneyi imati: “Poona cikhamu ca anthu, [Yesu] anawamvela cisoni, cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” Peter ataŵelenga lembali, misozi inalengeza m’maso mwake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi ndine mmodzi wa nkhosa zaconco?”
Peter anayamba kusintha. Anayamba kusamba, kudulila ndevu, ndi kuvala zovala zabwino zimene Don anam’patsa. Iye anapitiliza kukhala waukhondo ndi wooneka bwino.
Peter anali na kabuku kolembamo zocitika za pa umoyo wake. Kuciyambi kwa kabuku kameneko, iye analemba zinthu zomvetsa cisoni, koma zimene analemba posacedwapa, zinali zabwino ndi zokondweletsa. Zina zimene analemba n’zakuti: “Lelo nadziŵa dzina la Mulungu. Lomba nikamapemphela, nidzayamba kupemphela kwa Yehova. Ndine wokondwela ngako kudziŵa dzina lake. Don
anakamba kuti Yehova angakhale mnzanga wapamtima, amene anganimvetsele paciliconse cimene ningapemphe panthawi iliyonse.”Mau otsiliza amene Peter analemba, anali opita kwa abululu ake. Analemba kuti:
“Lelo sinimvela bwino. Cioneka kuti lomba nakalamba. Koma olo lelo litakhala tsiku langa lothela, nidziŵa kuti nidzaonananso naye mnzanga [Don] m’Paradaiso. Ndipo ngati mukuŵelenga izi, dziŵani kuti ine kulibenso. Koma ngati pamalilo anga mudzaona munthu wacilendo, mukakambe naye, ndipo conde muŵelenge kabuku aka kabuluu, [kutanthauza buku lakuti “Coonadi Cimene Cimatsogolela ku Moyo Wamuyaya,” lothandiza pophunzila Baibo limene iye analandila zaka zambili m’mbuyomo]. * Kamakamba kuti nidzaonananso na mnzangayo m’Paradaiso. Nikhulupilila zimenezi na mtima wanga wonse. Ndine m’bale wanu wokondedwa, Peter.”
Ataika malilo, Ummi, mlongosi wake wa Peter, anauza Don kuti: “Zaka ziŵili zapitazo n’nakambilana ndi Peter. Iyi inali nthawi yoyamba, pambuyo pa zaka zambili, kumuona Peter ali wacimwemwe. Anacita kumwetulila. Buku limene iye anakamba n’dzaliŵelenga, cifukwa cimene m’bale wanga angalandile, ciyenela kukhala capadela.” Ummi anavomeleza kuphunzila na Mboni za Yehova m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni.
Nafenso tisamaone cabe maonekedwe akunja, koma tizionetsa cikondi ceni-ceni, ndi kukhala oleza mtima na anthu amitundu yonse. (1 Tim. 2:3, 4) Tikatelo, tidzathandiza anthu amene, monga Peter, ni osaoneka bwino m’maso mwa anthu, koma ali na mtima wabwino. Tikhulupilila kuti Mulungu, amene “amaona mmene mtima ulili,” adzakulitsa coonadi m’mitima ya anthu a maganizo oyenela.—1 Sam. 16:7; Yoh. 6:44.
^ par. 7 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma lomba analeka kulipulinta.