Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Ngati mwamuna na mkazi osakwatilana anakhala m’nyumba imodzi usiku wonse popanda zifukwa zomveka, kodi lingakhale chimo lofunika komiti yaciweluzo?
Inde, ngati palibe zifukwa zomveka zimene anacitila zimenezo, komiti yaciweluzo ingapangidwe cifukwa umenewo ni umboni wamphamvu woonetsa kuti anthuwo anacita ciwelewele.—1 Akor. 6:18.
Bungwe la akulu limapenda mosamala nkhaniyo kuti lidziŵe ngati komiti yaciweluzo ifunika kupangidwa. Mwacitsanzo: Kodi anthuwo ali pa cibwenzi? Kodi anapatsidwapo uphungu wokhudza mmene amacitila zinthu kwa wina na mnzake? Kodi n’zocitika zanji zimene zinapangitsa kuti akhale m’nyumba imodzi usiku wonse? Kodi zinali zocita kukonzekela? Kodi anacita mwadala, kapena panali zifukwa zomveka, monga zinthu zosayembekezeleka kapena zakugwa mwadzidzidzi zimene zinapangitsa kuti asacitile mwina koma kukhala m’nyumba imodzi usiku wonse? (Mlal. 9:11) Kodi anagona m’cipinda cimodzi kapena zosiyana? Popeza zocitika zimasiyana-siyana, pangakhalenso mfundo zina zimene akulu angapende.
Pambuyo pofufuza zeni-zeni zimene zinacitika, bungwe la akulu lidzaona ngati anthuwo ni ofunika kuwapangila komiti yaciweluzo kapena ayi.