Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acicepele, Mlengi Wanu Amafuna Kuti Mukhale Acimwemwe

Acicepele, Mlengi Wanu Amafuna Kuti Mukhale Acimwemwe

“Akukukhutilitsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.”—SAL. 103:5.

NYIMBO: 135, 39

1, 2. Pamene tifuna kudziikila zolinga mu umoyo, n’cifukwa ciani n’cinthu canzelu kumvela malangizo a Mlengi wathu? (Onani mapikica pamwambapa.)

NGATI ndimwe wacicepele, mwacionekele mwalandilapo malangizo osiyana-siyana okhudza tsogolo lanu. Mwina matica kapena anthu ena, amakulimbikitsani kucita maphunzilo apamwamba kuti mukapeze nchito ya ndalama zambili. Koma Yehova amakulimbikitsani kukhala na zolinga zosiyana na zimenezi. Iye amafuna kuti muzicita khama pa maphunzilo anu kuti mukadzatsiliza sukulu, mudzakwanitse kudzisamalila mwekha. (Akol. 3:23) Koma posankha zinthu zofunika kuika patsogolo mu umoyo wanu, Yehova amafuna kuti muzitsogoleledwa na mfundo zake zothandiza, zimene n’zogwilizana na colinga cake kwa ise masiku ano otsiliza.—Mat. 24:14.

2 Komanso, kumbukilani kuti Yehova ndiye amadziŵa bwino zimene zingatithandize mu umoyo, cifukwa amadziŵa zimene zidzacitika pa dzikoli, ngakhale nthawi yeni-yeni imene lidzawonongedwa. (Yes. 46:10; Mat. 24:3, 36) Cinanso, Yehova ndiye amatidziŵa bwino. Amadziŵa zimene zingatithandize kukhala acimwemwe ndi okhutila, komanso zimene zingatibweletsele mavuto na kutilanda cimwemwe. Conco, olo malangizo ocokela kwa anthu ataoneka monga anzelu kwambili, sakhala othandiza ngati sagwilizana na Mawu a Mulungu.—Miy. 19:21.

‘PALIBE NZELU . . . YOTSUTSANA NDI YEHOVA’

3, 4. Kodi kumvela malangizo oipa kunabweletsa mavuto anji kwa Adamu na Hava, komanso kwa ana awo?

3 Kupeleka malangizo olakwika kunayamba kale kwambili pamene Satana ananamiza makolo athu oyambilila. Podziika yekha monga mlangizi, Satana anauza Hava kuti iye na mwamuna wake adzakhala na cimwemwe coculuka ngati asankha kumangocita zofuna zawo popanda kutsogoleledwa na Mulungu. (Gen. 3:1-6) Koma Satana anali na zolinga zadyela. Anali kufuna kuti Adamu na Hava, kuphatikizapo mbadwa zawo zakutsogolo, azimvela iye na kum’lambila m’malo molambila Yehova. Koma kodi Satana anali atawapatsako ciani? Palibe! Zonse zimene anali nazo anawapatsa ni Yehova. Iye anawapatsa banja labwino, malo okhala okongola, na matupi angwilo, amene akanakhala kwamuyaya.

4 N’zodandaulitsa kuti Adamu na Hava sanamvele Mulungu. Mwa ici, iwo anawononga ubwenzi wawo na Yehova. Ndipo zotulukapo zake zinali zomvetsa cisoni kwambili. Mofanana na maluŵa amene amafota na kuuma akathothoka, Adamu na Hava anayamba kukalamba, ndipo pamapeto pake anafa. Kusamvela kwawo kunabweletsanso mavuto aakulu kwa ana awo. (Aroma 5:12) Ngakhale n’conco, anthu ambili masiku ano amasankhabe kusamvela Mulungu. Iwo amangofuna kucita zofuna zawo. (Aef. 2:1-3) Zotulukapo zake zaonetselatu kuti ‘palibe nzelu . . . zotsutsana ndi Yehova.’—Miy. 21:30.

5. Kodi Mulungu anali na cidalilo cakuti anthu adzacita ciani? Kodi zimenezo zikucitikadi?

5 Komabe, Yehova anadziŵa kuti anthu ena, kuphatikizapo acicepele acitsanzo cabwino, adzaphunzila za iye na kum’tumikila. (Sal. 103:17, 18; 110:3) Ndithudi, Yehova amawakonda kwambili acicepele amenewa! Kodi imwe ndimwe mmodzi wa iwo? Ngati n’telo, ndiye kuti mukupindula na “zinthu zabwino” zambili zimene Mulungu wakupatsani, zomwe zimakupangitsani kukhala na cimwemwe coculuka. (Ŵelengani Salimo 103:5; Miy. 10:22) Lomba tiyeni tikambilane zina mwa “zinthu zabwino” zimenezo. Zinthu zake ni cakudya cauzimu coculuka, mabwenzi abwino koposa, zolinga zaphindu, na ufulu weni-weni.

YEHOVA AMAKUPATSANI ZOSOŴA ZANU ZAUZIMU

6. N’cifukwa ciani muyenela kuyesetsa kukhutilitsa zosoŵa zanu zauzimu? Nanga Yehova amakupatsani bwanji zosoŵa zauzimu?

6 Mosiyana na zinyama, ise anthu tili na zosoŵa zauzimu. Ndipo ni Mlengi wathu cabe amene angatipatse zosoŵa zimenezi. (Mat. 4:4) Ngati imwe acicepele mumvetsela kwa Yehova, mudzakhala na nzelu, luso la kuzindikila, na cimwemwe. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Mulungu amakupatsani zosoŵa zanu zauzimu kupitila m’Mawu ake, Baibo. Komanso, amacita izi mwa kupeleka cakudya cauzimu coculuka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Ndipo kukamba zoona, cakudya cauzimu cimene tili naco n’ca mwana alilenji.—Yes. 65:13, 14.

7. Ni mapindu anji amene mungapeze ngati muyesetsa kudya cakudya cauzimu cimene Mulungu amapeleka?

7 Cakudya cauzimu cimene Mulungu amapeleka cidzakuthandizani kukhala oganiza bwino ndi anzelu. Makhalidwe amenewa adzakutetezani m’njila zambili. (Ŵelengani Miyambo 2:10-14.) Mwacitsanzo, adzakuthandizani kuzindikila ziphunzitso zabodza, monga cakuti kulibe Mlengi. Adzakutetezaninso ku bodza lakuti kukhala na cuma ndiye cisinsi copezela cimwemwe. Cinanso, kuganiza bwino na nzelu zidzakuthandizani kupewa zilako-lako zoipa komanso makhalidwe amene angakubweletseleni mavuto. Conco, pitilizani kufuna-funa nzelu zocokela kwa Mulungu na luntha la kuganiza, ndipo muziona zimenezi monga cuma canu ca mtengo wapatali. Mukakhala na makhalidwe ofunika amenewa, mudzadzionela mwekha kuti Yehova amakukondani, ndiponso kuti amakufunilani zabwino.—Sal. 34:8; Yes. 48:17, 18.

8. N’cifukwa ciani ino ndiyo nthawi yofunika kulimbitsa ubwenzi wanu na Mulungu? Nanga kucita izi kudzakuthandizani bwanji kutsogolo?

8 Posacedwa, dziko lonse la Satana lidzawonongedwa, ndipo Yehova yekha ndi amene adzakhala malo athu acitetezo. Pa nthawiyo, tidzafunika kudalila kwambili Yehova kuti tipeze zofunikila mu umoyo, kuphatikizapo cakudya ca tsiku na tsiku. (Hab. 3:2, 12-19) Conco, ino ndiyo nthawi yofunika kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova, komanso kuphunzila kum’dalila kwambili. (2 Pet. 2:9) Mukacita izi, ndiye kuti kaya mukumane na mavuto otani, mudzamvela ngati mmene wamasalimo Davide anamvelela, pamene analemba kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”—Sal. 16:8.

YEHOVA WAKUPATSANI MABWENZI ABWINO KWAMBILI

9. (a) Malinga na Yohane 6:44, kodi Yehova amacita ciani? (b) Kodi kukumana na munthu amene si Mboni kumasiyana bwanji na kukumana na Mboni inzathu?

9 Yehova amakoka anthu oona mtima kuti azim’lambila monga banja lake lauzimu. (Ŵelengani Yohane 6:44.) Ngati mwakumana na munthu amene si Mboni kwa nthawi yoyamba, pamakhala zambili zimene simudziŵa zokhudza munthuyo. Mwina mungadziŵeko cabe maonekedwe ake kapena dzina lake ngati wakuuzani. Koma bwanji ngati mwakumana na mtumiki wa Yehova? Olo atakhala kuti ni wa cikhalidwe cina, dziko lina, kapena mtundu wina, pamakhala zambili zimene mumadziŵa zokhudza iye, komanso zimene iye amadziŵa zokhudza imwe.

Yehova amafuna kuti tikhale na zolinga zauzimu komanso mabwenzi abwino (Onani palagilafu 9-12)

10, 11. Kodi anthu a Yehova amafanana pa zinthu ziti? Nanga kufanana kumeneku kuli na ubwino wanji?

10 Mwacitsanzo, mwamsanga mumazindikila kuti nonse mumakamba “cilankhulo coyela,” cimene ni coonadi. (Zef. 3:9) Conco, mumadziŵa kuti zimene mumakhulupilila n’zofanana, kaya ni zokhudza Mulungu, mfundo za makhalidwe abwino, ciyembekezo ca kutsogolo, na zina zambili. Kudziŵa zimenezi n’kofunika kwambili cifukwa n’kumene kumathandiza kuti muyambe kudalilana, ndipo kumayala maziko a ubwenzi wabwino komanso wolimba.

11 Kukamba zoona, monga mtumiki wa Yehova, muli na mabwenzi oculuka komanso abwino kwambili. Mabwenzi amenewa amapezeka pa dziko lonse lapansi, kungoti mukalibe kukumana nawo kuti muwadziŵe. N’ndaninso ena amene ali na mwayi ngati umenewu, umene ise anthu a Yehova tili nawo?

YEHOVA AMAKUTHANDIZANI KUKHALA NA ZOLINGA ZAPHINDU

12. Ni zolinga zauzimu ziti zimene mungadziikile?

12 Ŵelengani Mlaliki 11:9 mpaka caputa 12:1. Kodi muli na zolinga zauzimu zimene mukuyesetsa kuzikwanilitsa? Mwina munadziikila colinga cakuti muziŵelenga macaputa angapo a Baibo tsiku lililonse. Kapena mukuyesetsa kukulitsa luso la kukamba nkhani na kuphunzitsa. Kodi mumamvela bwanji ngati mwaona kuti mukupita patsogolo, kapena ngati wina waona kupita patsogolo kwanu na kukuyamikilani? Mwacionekele, mumamvela bwino komanso mumakhala na cimwemwe. Cifukwa ciani? Cifukwa mudziŵa kuti mukucita cifunilo ca Mulungu, monga mmene Yesu anacitila.—Sal. 40:8; Miy. 27:11.

13. N’cifukwa ciani kutumikila Mulungu n’kwabwino kwambili kusiyana na kukhala na zolinga zakuthupi?

13 Ngati muika maganizo anu pa kutumikila Yehova, mumakhala acimwemwe podziŵa kuti zimene mukucita sizingapite pacabe. Mtumwi Paulo anati: “Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye, podziŵa kuti zonse zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe.” (1 Akor. 15:58) Mosiyana na zimenezi, anthu amene amaika maganizo awo onse pa zolinga zakuthupi, angaoneke kuti zinthu zikuwayendela, koma pamapeto pake amagwilitsidwa mwala. (Luka 9:25) Mfumu Solomo anadzionela yekha kuti mfundo imeneyi ni ya zoona. Ndipo ise tingaphunzilepo kanthu pa citsanzo cake.—Aroma 15:4.

14. Kodi tingaphunzile ciani pa zimene Solomo anacita pofuna kukhala na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa?

14 Solomo anali munthu wolemela kwambili, komanso anali na ulamulilo wamphamvu. Iye anacita zinthu zosiyana-siyana zom’kondweletsa kuti aone ngati padzakhala zotulukapo zabwino. (Mlal. 2:1-10) Solomo anamanga nyumba zambili, anadzipangila minda na mapaki okongola, ndipo anacita ciliconse cimene mtima wake unali kulaka-laka. Kodi anamvela bwanji pambuyo pake? Kodi anakhutila? Kodi anapeza cimwemwe? Solomo iye mwini anafotokoza mmene anamvelela. Anati: “Ndinaganizila nchito zonse zimene manja anga anagwila . . . , ndinaona kuti zonse zinali zacabecabe . . . Padziko lapansi pano panalibe caphindu ciliconse.” (Mlal. 2:11) Ndithudi, apa pali phunzilo lamphamvu kwambili kwa imwe acicepele!

15. N’cifukwa ciani cikhulupililo n’cofunika? Malinga na Salimo 32:8, kodi kukhala naco kuli na phindu lanji?

15 Yehova amafuna kuti muzimumvela kuti mupewe mavuto. Koma pamafunika cikhulupililo kuti muzimumvela na kuika cifunilo cake patsogolo. Kukhala na cikhulupililo n’kofunika kwambili, ndipo mukakhala naco simudzagwilitsidwa mwala. Yehova sadzaiŵala “cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Conco, yesetsani kulimbitsa cikhulupililo canu. Mukatelo, mudzatha kupanga zosankha mwanzelu, ndipo mudzaona kuti Atate wanu wakumwamba amakufunilani zabwino.—Ŵelengani Salimo 32:8.

YEHOVA AMAKUPATSANI UFULU WENI-WENI

16. N’cifukwa ciani tiyenela kuyamikila ufulu umene Mulungu watipatsa komanso kuuseŵenzetsa mwanzelu?

16 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Yehova ndiye Mzimu, ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” (2 Akor. 3:17) Yehova ni Mulungu waufulu, ndipo anakupatsani mtima wofuna kukhala na ufulu. Komabe, iye amafuna kuti muziseŵenzetsa ufulu wanu mwanzelu, cifukwa kucita zimenezi n’citetezo kwa imwe. Mwina mudziŵako acicepele ena amene amatamba zamalisece, kucita zaciwelewele, maseŵela oika moyo paciopsezo, kumwa moŵa mwaucidakwa, na kuseŵenzetsa am’kolabongo. N’zoona kuti angasangalale na zinthu zimenezi kwa kanthawi. Koma nthawi zambili zotulukapo zake zimakhala mavuto aakulu, monga matenda, ngakhale imfa kumene. Kuwonjezela apo, amakhala akapolo a zilako-lako zawo. (Agal. 6:7, 8) Acicepele amene amacita zinthu zimenezi angaone monga ali pa ufulu, koma m’ceni-ceni amadziika mu ukapolo.—Tito 3:3.

17, 18. (a) Kodi kumvela Mulungu kumatithandiza bwanji kukhala na ufulu? (b) Kodi ufulu umene Adamu na Hava anali nawo mu Edeni usiyana bwanji na ufulu umene anthu ali nawo masiku ano?

17 Mosiyana na zimenezi, kutsatila miyezo ya m’Baibo kumatiteteza. Conco, n’zoonekelatu kuti kumvela Yehova kungakuthandizeni kukhala na ufulu komanso thanzi labwino. (Sal. 19:7-11) Cinanso, ngati museŵenzetsa ufulu wanu mwanzelu, kapena kuti mogwilizana na malamulo angwilo a Mulungu komanso mfundo zake, mumaonetsa kuti ndimwe munthu wodalilika. Yehova komanso makolo anu adzakudalilani, nokupatsani ufulu woculukilapo. Ndipo colinga ca Mulungu n’cakuti kutsogolo adzapatse atumiki ake okhulupilika ufulu weni-weni, umene Baibo imaucha “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.

18 Adamu na Hava anaulaŵako ufulu wotelo. Ganizilani cabe: Kodi ni malamulo angati amene Mulungu anawapatsa m’munda wa Edeni? Limodzi lokha. Anawaletsa kudya zipatso za mtengo umodzi cabe. (Gen. 2:9, 17) Kodi tingakambe kuti lamulo limenelo linawalanda ufulu? Kutalitali! Yelekezelani zimenezi na malamulo ambili-mbili amene anthu akhazikitsa masiku ano n’kumakakamiza anthu anzawo kuti aziwatsatila.

19. Kodi Mulungu amatiphunzitsa bwanji kukhala anthu aufulu?

19 Yehova amacita nase zinthu mwanzelu kwambili ise atumiki ake. Iye sanatipatse malamulo ambili-mbili. Koma moleza mtima amatiphunzitsa kuti tizicitilana zinthu mwacikondi. Iye amafuna kuti tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino na kuzonda zoipa. (Aroma 12:9) Pa Ulaliki wa pa Phili, Mwana wake Yesu anafotokoza cimene cimapangitsa anthu kucita zoipa. (Mat. 5:27, 28) Pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, m’dziko latsopano Khristu adzapitiliza kutiphunzitsa kuona zabwino na zoipa monga mmene iye amazionela. (Aheb. 1:9) Komanso, adzatithandiza kukhala angwilo. Panthawiyo, sitidzakhalanso na zilakolako za ucimo, kapena kukumana na zoŵaŵa zobwela cifukwa ca ucimo. Ndiyeno, tidzakondwela na “ufulu waulemelelo” umene Yehova analonjeza.

20. (a) Kodi Yehova amauseŵenzetsa bwanji ufulu wake? (b) Nanga imwe acicepele mungapindule bwanji ngati mutengela citsanzo cake?

20 Komabe, ngakhale m’dziko latsopano, ufulu umene tidzakhala nawo, udzakhala na malile. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti nthawi zonse, tidzafunika kucita zinthu motsogoleledwa na cikondi cathu pa Mulungu komanso pa anthu anzathu. Mwa kucita zimenezo, tidzaonetsa kuti tikutengela citsanzo ca Yehova. Ngakhale kuti iye ali na ufulu wopanda malile, amauseŵenzetsa mwacikondi pocita zinthu na angelo komanso anthu ake. (1 Yoh. 4:7, 8) Conco, tingakambe kuti ufulu umakhala weni-weni ngati timauseŵenzetsa motsogoleledwa na cikondi monga mmene Mulungu amacitila.

21. (a) Kodi Davide anakamba ciani ponena za Yehova? (b) Nanga m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

21 Imwe acicepele, kodi mumayamikila “zinthu zabwino” zambili zimene Yehova wakupatsani? Iye wakupatsani cakudya cauzimu ca mwana alilenji, mabwenzi abwino, zolinga zaphindu, komanso ufulu weni-weni. (Sal. 103:5) Ngati n’conco, ndiye kuti mwina mumamvela monga mmene Mfumu Davide anamvelela, pamene anati: “Mudzandidziwitsa njila ya moyo. Cifukwa ca nkhope yanu, munthu adzakondwela mokwanila. Kudzanja lanu lamanja kuli cimwemwe mpaka muyaya.” (Sal. 16:11) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mfundo zina zofunika za mu Salimo 16. Kukambilana mfundo zimenezo kudzakuthandizani kudziŵa zinthu zina zimene zimathandiza munthu kukhala na cimwemwe ceni-ceni mu umoyo.