Cikondi—Khalidwe Lamtengo Wapatali
MOUZILIDWA, mtumwi Paulo analemba makhalidwe 9 amene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Iye anakamba kuti makhalidwe ocititsa cidwi amenewa, onse pamodzi ni “cipatso ca Mzimu.” (Buku Lopatulika) * Komanso, makhalidwe amenewa ni mbali ya “umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) Monga mmene mtengo umabalila zipatso ngati usamalidwa bwino, nayenso munthu amaonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala ngati alola mzimuwo kum’tsogolela.—Sal. 1:1-3.
Khalidwe loyamba limene Paulo anachula pa makhalidwe amene mzimu woyela umabala ni cikondi. Limeneli ni khalidwe lamtengo wapatali. Kodi n’lamtengo wapatali motani? Poonetsa kufunika kwa khalidweli, Paulo anakamba kuti popanda cikondi, sembe iye ‘sali kanthu.’ (1 Akor. 13:2) Koma kodi cikondi n’ciani? Ndipo tingacitenji kuti tikhale naco? Nanga tingacionetse bwanji mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku?
MMENE BAIBO IMAFOTOKOZELA CIKONDI
Ngakhale kuti n’zovuta kufotokoza kuti cikondi n’ciani, Baibo imatiuza mmene munthu amaonetsela cikondi. Mwacitsanzo, timaŵelenga kuti cikondi “n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Komanso, cikondi “cimakondwela ndi coonadi. Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” Cikondi cimaphatikizaponso kukomela mtima ena, kuwadela nkhawa, ndi kukhala nawo paubwenzi. Ngati munthu alibe cikondi, amakhala wansanje, wonyada, wodzikonda, waukali ndi wosakhululukila ena, ndiponso amacita zinthu zosayenela. Ise sitifuna kukhala na makhalidwe monga amenewa. M’malomwake, timafuna kukhala na cikondi, cimene “sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4-8.
YEHOVA NA YESU NI ZITSANZO ZABWINO PANKHANI YOONETSA CIKONDI
“Mulungu ndiye cikondi.” Zoonadi, Yehova ndiye cimake ca cikondi. (1 Yoh. 4:8) Zonse zimene analenga ndiponso zimene amacita zimaonetsa kuti iye ni wacikondi. Njila yaikulu imene anaonetsela cikondi kwa anthu ni mwa kutumiza Yesu kuti adzavutike ndi kutifela. Mtumwi Yohane anati: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye. Cikondi cimeneci cikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba macimo athu.” (1 Yoh. 4:9, 10) Cifukwa ca cikondi ca Mulungu, tikhoza kukhululukidwa macimo, kukhala na ciyembekezo, ndi kudzapeza moyo wosatha.
Yesu anaonetsa cikondi cake kwa anthu mwa kucita cifunilo ca Mulungu modzipeleka. Paulo anagwila mau a Yesu akuti: “Taonani! Ine ndabwela kudzacita cifunilo canu.” Kenako, Paulo anati: “Mwa ‘cifunilo’ cimeneco, tayeletsedwa kudzela m’thupi la Yesu Khristu lopelekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheb. 10:9, 10) Palibe munthu angaonetse cikondi cacikulu kuposa cimene Yesu anationetsa. Yesu anati: “Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Kodi ise anthu opanda ungwilo tingakwanitse kutengela cikondi cimene Yehova na Yesu anationetsa? Inde. Tiyeni tione mmene tingacitile zimenezo.
“YENDANIBE M’CIKONDI”
Paulo anati: “Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’cikondi, monganso Khristu anakukondani n’kudzipeleka yekha cifukwa ca inu.” (Aef. 5:1, 2) ‘Timayenda m’cikondi’ mwa kuonetsa khalidwe limeneli m’mbali zonse za moyo wathu. Timaonetsa cikondi cimeneci mwa zocita zathu osati mwa mau cabe. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mau okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceniceni m’zocita zathu.” (1 Yoh. 3:18) Mwacitsanzo, timaonetsa kuti timakonda Mulungu ndi anzathu mwa kulengeza “uthenga wabwino wa ufumu.” (Mat. 24:14; Luka 10:27) Timayendanso m’cikondi mwa kukhala oleza mtima, okoma mtima, ndi okhululuka. N’cifukwa cake Baibo imatilangiza kuti: “Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.”—Akol. 3:13.
Koma ngati tipatsa ena uphungu, kapena kuwaongolela sizitanthauza kuti tilibe cikondi. Mwacitsanzo, pofuna kutonthoza mwana, makolo ena amapatsa mwanayo ciliconse cimene wafuna. Koma kholo limene limakondadi mwana wake, limakana kum’patsa ngati zimene akufunazo n’zosafunikila. Mofananamo, Yehova ndiye cikondi, koma “amalanga aliyense amene iye amamukonda.” (Aheb. 12:6) Ifenso tingaonetse kuti tikuyenda m’cikondi mwa kupeleka uphungu kwa ena pakakhala pofunikila kutelo. (Miy. 3:11, 12) Pocita izi, tifunika kukumbukila kuti nafenso ndife opanda ungwilo ndipo tingathe kulakwila anzathu. Conco, tonse tili na mbali zina zofunika kuwongolela kuti tikulitse khalidwe la cikondi. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Tiyeni tione njila zitatu.
TINGACITE CIANI KUTI TIKULITSE KHALIDWE LA CIKONDI?
Coyamba, muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu wake umene udzakuthandizani kukhala na cikondi. Yesu anakamba kuti Yehova amapeleka “mzimu woyela kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Ngati tipempha mzimu woyela ndi ‘kupitiliza kuyenda mwa mzimuwo,’ tidzayamba kucita zinthu mwacikondi kwambili ndi ena. (Agal. 5:16) Mwacitsanzo, ngati ndinu mkulu mumpingo, mungapemphe mzimu woyela kuti ukuthandizeni kupeleka uphungu wa m’Malemba mwacikondi kwa ena. Ndipo ngati ndinu kholo, mungapemphe mzimu wa Mulungu kuti ukuthandizeni kulanga ana anu mwacikondi osati mwaukali.
Caciŵili, muziganizila mmene Yesu anaonetsela cikondi ngakhale pamene anali kunyozedwa. (1 Pet. 2:21, 23) Tifunika kuganizila kwambili citsanzo ca Khristu maka-maka ngati ena atikhumudwitsa kapena aticitila zinthu zopanda cilungamo. Zikakhala conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu akanacita ciani pamenepa?’ Mlongo wina, dzina lake Leigh anaona kuti kuganizila funso limeneli kunamuthandiza kucita zinthu mwanzelu. Iye anati: “Nthawi ina, mnzanga kunchito analemba meseji yoipa yokhudza khalidwe langa ndi kagwilidwe kanga ka nchito, n’kuitumiza kwa anzanga amene nimaseŵenza nawo. Izi zinanikhumudwitsa kwambili. Koma n’nadzifunsa kuti, ‘Ningatengele bwanji Yesu pocita zinthu na munthu ameneyu?’ Pambuyo poganizila zimene Yesu akanacita, n’nasankha kungoiŵalako nkhaniyo, osalimbana naye. Patapita nthawi, n’namva kuti mnzangayo ali na matenda aakulu, ndipo amavutika kwambili na nkhawa. Conco, n’naona kuti mwina analemba mesejiyo cifukwa covutika maganizo. Kuganizila mmene Yesu anaonetsela cikondi ngakhale pamene anali kunyozedwa, kunanithandiza kunyalanyaza colakwa ca mnzanga wakunchito.” Zoonadi, ngati titengela Yesu, nthawi zonse tidzayamba kucita zinthu mwacikondi.
Cacitatu, mufunika kukulitsa cikondi codzimana, cimene n’cizindikilo ca Akhristu oona. (Yoh. 13:34, 35) Pa mfundo imeneyi, Malemba amatilimbikitsa kuti tiyenela kukhala na “maganizo” amenenso Yesu anali nawo. Pamene iye anacoka kumwamba, “anasiya zonse zimene anali nazo” ‘mpaka kufa’ cifukwa ca ise. (Afil. 2:5-8) Ngati titengela cikondi cake cololela kuvutikila ena, mtima ndi maganizo athu zidzakhala ngati za Khristu, ndipo tidzayamba kuika zofuna za ena patsogolo osati zofuna zathu. Ni mapindu ena ati amene timapeza ngati tionetsa cikondi?
MAPINDU AMENE TIMAPEZA NGATI TIONETSA CIKONDI
Tikamaonetsa cikondi, timapeza madalitso okhalitsa. Mwacitsanzo, onani madalitso aŵili awa:
-
UBALE WA PADZIKO LONSE: Cifukwa cakuti timakondana, timadziŵa kuti tikapita ku mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova padziko lapansi, abale ndi alongo adzatilandila bwino kwambili. Ndithudi, ni dalitso lalikulu kwambili kukondedwa na ‘gulu lonse la abale m’dzikoli.’ (1 Pet. 5:9) Kulibenso kwina kumene tingapeze cikondi ngati cimene cili pakati pa anthu a Mulungu.
-
MTENDELE: ‘Kulolelana m’cikondi’ kumatithandiza kukhala pa mtendele, umene uli “monga comangila cotigwilizanitsa.” (Aef. 4:2, 3) Timadzionela tekha mtendele umenewu tikakhala pa misonkhano yampingo, yadela, ndi yacigawo. Kodi si zoona kuti mtendele umenewu ni wapadela kwambili m’dzikoli, limene ni logaŵikana? (Sal. 119:165; Yes. 54:13) Ngati tiyesetsa kukhala mwamtendele na ena, timaonetsa kuti timawakonda kwambili, ndipo zimenezi zimakondweletsa Atate wathu wakumwamba.—Sal. 133:1-3; Mat. 5:9.
“CIKONDI CIMAMANGILILA”
Paulo analemba kuti: “Cikondi cimamangilila.” (1 Akor. 8:1) Kodi cimamangilila bwanji? M’caputa 13 ca kalata yoyamba imene mtumwi Paulo analembela Akorinto, anafotokoza mmene cikondi cimagwilizanitsila Akhristu. Njila imodzi ni yakuti cikondi cimalimbikitsa munthu kuika patsogolo zofuna za ena. (1 Akor. 10:24; 13:5) Kuwonjezela apo, munthu wacikondi, amaganizila ena, amakhala woleza mtima, komanso wokoma mtima. Izi zimathandiza kuti anthu m’banja azikondana kwambili ndipo mipingo imakhala yogwilizana.—Akol. 3:14.
Kukonda Mulungu ndiye kofunika kwambili ndipo kumatilimbikitsa ngako. Kumagwilizanitsa anthu osiyana mitundu, kocokela, ndi zinenelo kuti azitumikila Yehova mwacimwemwe ndi “mogwilizana.” (Zef. 3:9) Conco, tiyeni tiziyesetsa tsiku lililonse kuonetsana cikondi, cimene ndi khalidwe lamtengo wapatali limene mzimu woyela wa Mulungu umabala.
^ par. 2 Iyi ni nkhani yoyamba pa nkhani 9 zimene zidzafotokoza khalidwe lililonse limene mzimu woyela umabala.