Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Njila Yopezela Ufulu Weni-weni

Njila Yopezela Ufulu Weni-weni

“Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.” —YOH. 8:36.

NYIMBO: 54, 36

1, 2. (a) Pali umboni wanji woonetsa kuti anthu amafunafuna kukhala na ufulu? (b) Nanga zoyesa-yesa zawo zakhala na zotulukapo zanji?

MASIKU ANO, anthu ambili amakonda kukamba za kukhala na ufulu. Anthu m’maiko ambili amafuna kukhala omasuka ku mavuto monga umphawi, tsankho, na kupondelezedwa. Ena amafuna kukhala na ufulu wolankhula komanso wodzisankhila zocita. Inde, anthu kulikonse padzikoli amalakalaka kukhala na ufulu wocita zilizonse zimene afuna na kukhala na umoyo mmene afunila.

2 Komabe, ambili amaseŵenzetsa njila zolakwika pofuna kudzipezela ufulu. Anthu ambili andale na ena amakonda kucita zionetselo za kusakondwa, kuukila boma, na kucita makampeni ofuna kusintha zinthu m’dziko. Koma kodi kucita zimenezi kumawathandiza kupezadi ufulu? Kutalitali. Nthawi zambili kumabweletsa mavuto na kuwonongetsa miyoyo ya anthu. Zonsezi zimaonetsa kuti mau ouzilidwa a Mfumu Solomo ni oona. Iye anati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—Mlal. 8:9.

3. N’ciani cimene tingacite kuti tipeze cimwemwe ceni-ceni?

3 Mtumwi Yakobo anafotokoza cimene cingatithandize kukhala na cimwemwe ceni-ceni na kukhala okhutila. Anati: “Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwilo limene limabweletsa ufulu, amene amalimbikila kutelo, adzakhala wosangalala policita.” (Yak. 1:25) Yehova, amene anapeleka lamulo langwilo limenelo amadziŵa bwino zimene anthu amafunikila kuti akhale na cimwemwe ceni-ceni. Iye anapatsa Adamu na Hava zinthu zonse zofunikila kuti akhale na cimwemwe, komanso kuti akhale na ufulu weni-weni.

PAMENE ANTHU ANALI NA UFULU WENI-WENI

4. Ni ufulu wanji umene Adamu na Hava anali nawo? (Onani pikica kuciyambi.)

4 Pamene tiŵelenga macaputa aŵili oyambilila a Genesis, timaona kuti Adamu na Hava anali na ufulu weni-weni umene anthu masiku ano amaulakalaka. Panalibe cowayofya, sanali kusoŵa ciliconse, ndiponso panalibe amene anali kuwapondeleza. Komanso sanali kudela nkhawa za cakudya, matenda, na imfa. Analinso na nchito yabwino. (Gen. 1:27-29; 2:8, 9, 15) Koma kodi izi zitanthauza kuti Adamu na Hava anali na ufulu wocita ciliconse cimene anali kufuna? Tiyeni tikambilane.

5. Mosiyana ndi zimene ambili amaganiza, kodi n’ciani cofunika kuti anthu akhale na ufulu?

5 Anthu oculuka masiku ano amaganiza kuti kukhala na ufulu weni-weni kumatanthauza kucita ciliconse cimene munthu akufuna, mosasamala kanthu kuti padzakhala zotulukapo zotani. Buku lochedwa The World Book Encyclopedia limakamba kuti ufulu umatanthauza “kukhala na mwayi wopanga zosankha na kuzikwanilitsa.” Koma limakambanso kuti, “Pa za malamulo, anthu amakhala na ufulu ngati m’dziko muli malamulo acilungamo, oyenelela, komanso osapondeleza.” Izi zionetsa kuti m’dziko mumafunika kukhala malamulo kuti munthu aliyense apindule na ufulu umene ali nawo. Lomba funso n’lakuti, n’ndani amene ali woyenela kutiikila malamulo acilungamo, oyenelela, komanso osapondeleza?

6. (a) N’cifukwa ciani Yehova yekha ndiye ali na ufulu wocita ciliconse? (b) Ni ufulu wa mtundu wanji umene anthu ali nawo? Nanga n’cifukwa ciani takamba conco?

6 Pamene tikambilana za ufulu, ni bwino kukumbukila kuti Yehova Mulungu yekha ndiye ali na ufulu wocita ciliconse—ufulu wopanda malile. Cifukwa ciani? Cifukwa iye ni Mlengi wa zinthu zonse komanso ni Mfumu Yamphamvuzonse m’cilengedwe conse. (1 Tim. 1:17; Chiv. 4:11) Kumbukilani mau ocititsa cidwi amene Mfumu Davide inakamba ponena za udindo wapamwamba ndi wapadela wa Yehova. (Ŵelengani 1 Mbiri 29:11, 12.) Conco, ufulu umene anthu na angelo ali nawo uli na malile. Iwo amafunika kuzindikila kuti Yehova Mulungu ali na mphamvu yoika malamulo alionse amene waona kuti ni acilungamo, oyenelela, ndi osapondeleza. Izi n’zimene iye anacita kwa anthu oyambilila atangowalenga.

7. N’zinthu zina ziti zimene timacita mwacibadwa, zimene zimatipatsa cimwemwe?

7 Olo kuti poyamba Adamu na Hava anali na ufulu m’njila zambili, Mulungu anawaikila malile kapena kuti malamulo. Ena mwa malamulowo anali acibadwa, koma anali malamulo ndithu. Mwacitsanzo, makolo athu oyamba anali kudziŵa kuti anafunika kucita zinthu monga kudya, kupuma, na kugona kuti akhalebe na moyo. Kodi iwo anali kuona kuti kucita zimenezi kunali kuwalanda ufulu? Iyai, cifukwa Yehova anawalenga m’njila yakuti azimvela bwino na kukondwela pocita zinthu zimenezi. (Sal. 104:14, 15; Mlal. 3:12, 13) N’ndani amene sakondwela ngati apuma mpweya wabwino, kudya cakudya cokoma, kapena kugona tulo twabwino? Timakondwela kucita zinthu zofunika zimenezi, ndipo sitiona kuti n’zovuta kapena zolemetsa. Mwacionekele, umu ni mmenenso Adamu na Hava anali kumvelela.

8. Ni lamulo liti limene Mulungu anapeleka kwa makolo athu oyamba? Nanga colinga cake cinali ciani?

8 Yehova analamula Adamu na Hava kuti abeleke ana na kudzaza dziko lapansi, komanso kuti azilisamalila. (Gen. 1:28) Kodi lamulo limeneli linawaphwanyila ufulu? Kutalitali! Mulungu anapeleka lamuloli kwa anthu pofuna kuwapatsa mwayi wom’thandiza pokwanilitsa colinga cake copanga dziko lapansi kukhala paladaiso, kuti anthu angwilo akhalemo kwamuyaya. (Yes. 45:18) Masiku ano, anthu angasankhe kusakwatila kapena kukwatila koma osabeleka ana. Ndipo kucita izi si kosemphana na cifunilo ca Yehova. Komabe, anthu ambili amakwatila na kubeleka ana olo kuti umoyo wa banja uli na zovuta zake. (1 Akor. 7:36-38) N’cifukwa ciani amatelo? Cifukwa nthawi zambili kucita zimenezi kumawabweletsela cimwemwe. (Sal. 127:3) Adamu na Hava akanamvela Mulungu, akanasangalala na umoyo wa banja kwamuyaya.

MMENE ANTHU ANATAYILA UFULU WENI-WENI

9. N’cifukwa ciani tikamba kuti lamulo la Mulungu la pa Genesis 2:17 silinali lopondeleza kapena losafunikila?

9 Yehova anapatsanso Adamu na Hava lamulo lina, ndipo anawauzilatu cilango cimene adzalandila ngati sadzamvela. Iye anati: “Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:17) Kodi lamulo limeneli linali losafunikila kapena lopondeleza? Kodi linawalanda ufulu anthuwo? Iyai. Ndipo akatswili ena a Baibo amakamba kuti lamuloli linali lofunika ndi loyenelela. Mwacitsanzo, katswili wina anati: “Lamulo la Mulungu [pa Genesis 2:16, 17] limaonetsa kuti Mulungu yekha ndiye amadziŵa cimene cili cabwino . . . kwa anthu ndi kuti Mulungu yekha ndiye amadziŵa cimene si cabwino . . . kwa iwo. Kuti anthu akhale na umoyo ‘wabwino,’ afunika kudalila Mulungu na kumumvela. Apo ayi, adzafunika kudziŵa okha cabwino . . . na coipa.” Koma anthu paokha sangakwanitse kudziŵa cabwino na coipa.

Zimene Adamu na Hava anasankha kucita zinabweletsa mavuto ambili (Onani palagilafu 9-12)

10. Pali kusiyana kwanji pakati pa ufulu wodzisankhila zocita na udindo wodziŵitsa cabwino ndi coipa?

10 Anthu ambili masiku ano akaŵelenga lamulo limene Yehova anapatsa Adamu, amaona kuti Adamu anamanidwa ufulu wocita zofuna zake. Koma iwo amaiŵala kuti olo kuti anthufe tili na ufulu wosankha zocita, sitinalengedwe na udindo wodziikila tekha miyezo ya cabwino na coipa. Adamu na Hava anali na ufulu wosankha kumvela Mulungu kapena kusamumvela. Komabe, Yehova yekha ndiye ali na udindo wodziŵitsa anthu cabwino na coipa, ndipo “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa,” umene unali m’munda wa Edeni, unali kuimila udindo wake umenewu. (Gen. 2:9) Kukamba zoona, nthawi zambili ise anthu sitidziŵa kuti zosankha zathu zidzakhala na zotulukapo zabwanji. Sitidziŵa kuti kaya zinthu zidzatiyendela bwino kapena ayi. Ndiye cifukwa cake ngakhale anthu apange zosankha zooneka zabwino, nthawi zina zimawabweletsela mavuto na masoka. (Miy. 14:12) Izi zionetsa kuti pali zinthu zina zimene anthufe patekha sitingakwanitse kucita. Conco, pamene Yehova anapatsa Adamu na Hava lamulo, anali kuwaphunzitsa njila yokhalila na ufulu weni-weni. Kodi makolo athu oyambilila anacita bwanji na lamulo limenelo?

11, 12. N’cifukwa ciani zimene Adamu na Hava anasankha kucita zinabweletsa mavuto? Fotokozani citsanzo.

11 Makolo athu oyambilila anasankha kusamvela Mulungu. Hava anakopeka na mfundo yabodza ya Satana yakuti “maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.” (Gen. 3:5) Kodi zimene Adamu na Hava anasankha kucita zinawaonjezela ufulu? Iyai. Iwo sanalingane na Mulungu monga mmene Satana anakambila. M’malomwake, anadzionela okha kuti kukana citsogozo ca Yehova kumabweletsa mavuto aakulu. (Gen. 3:16-19) Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova sanapatse anthu ufulu wodziikila okha miyezo ya cabwino na coipa.—Ŵelengani Miyambo 20:24; Yeremiya 10:23.

12 Izi tingaziyelekezele na zimene woyendetsa ndeke amacita. Kuti akafike bwino kumene akupita, amafunika kutsatila njila ya ndeke imene amuuza kuyendamo. Amacita izi poseŵenzetsa makina a m’ndeke olongoza malo. Komanso amakambilana ndi anthu amene ali pansi, amene nchito yawo ni kumuuza nthawi imene afunika kunyamuka, kumene afunika kupitila, na nthawi imene afunika kutela. Koma bwanji ngati woyendetsa ndeke wanyalanyaza malangizowo na kutenga njila ina imene iye wafuna? Angacite ngozi yoopsa kwambili. Mofanana ndi woyendetsa ndeke ameneyo, Adamu na Hava anasankha kuyenda m’njila yawo-yawo. Anakana kutsogoleledwa na Mulungu. Mapeto ake, anacita ngozi yoopsa, titelo kukamba kwake. Anadzibweletsela ucimo na imfa, ndipo zimenezi zinafalikila kwa mbadwa zawo zonse. (Aroma 5:12) Cifukwa cokana kutsogoleledwa na Mulungu, iwo anataya ufulu weni-weni umene anali nawo poyamba.

MMENE TINGAPEZELE UFULU WENI-WENI

13, 14. N’ciani cimene tifunika kucita kuti tikapeze ufulu weni-weni?

13 Anthu ena amaganiza kuti kukhala na ufulu woculuka n’kumene kungawathandize kukhala na umoyo wabwino. Koma zoona zake n’zakuti kukhala na ufulu wopanda malile kumabweletsa mavuto. N’zoona kuti ufulu uli na ubwino wake. Koma ganizani cabe mmene zinthu zikanaipila pa dzikoli pakanakhala popanda malamulo aliwonse. M’pake kuti buku lakuti The World Book Encyclopedia limati: “Malamulo a m’dziko lililonse amapanga msakanizo wovuta kumvetsa wa maufulu ambili na ziletso zake.” Ndithudi, mau akuti “wovuta kumvetsa” ndi oyenelela. Tangoganizilani cabe za mabuku masauzande-masauzande a zamalamulo amene anthu alemba, komanso maloya na oweluza ambili-mbili amene nchito yawo ni kufotokoza tanthauzo la malamulowo na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa.

14 Mosiyana ndi zimenezi, Yesu Khristu anachula njila yosavuta yopezela ufulu weni-weni. Anati: “Mukamasunga mau anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Malinga n’zimene Yesu anakamba, pali zinthu ziŵili zimene tifunika kucita kuti tidzapeze ufulu weni-weni: Coyamba, kuphunzila coonadi cimene iye anaphunzitsa, ndipo caciŵili, kukhala wophunzila wake. Kucita izi kudzatithandiza kukapeza ufulu weni-weni. Ufulu womasuka ku ciani? Yesu anati: “Aliyense wocita chimo ndi kapolo wa chimo. . . . Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”—Yoh. 8:34, 36.

15. N’cifukwa ciani tingakambe kuti ufulu umene Yesu anatilonjeza udzakhaladi weni-weni?

15 N’zacidziŵikile kuti ufulu umene Yesu analonjeza ophunzila ake ni weni-weni. Sungalingane na ufulu wa zacikhalidwe kapena wa zandale umene anthu ambili amaulakalaka masiku ano. Pamene Yesu anakamba kuti: “Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka,” anali kukamba za kumasuka ku ‘ukapolo wa ucimo,’ umene wasautsa anthu kwambili kuposa ukapolo wina uliwonse. Ucimo umatisonkhezela kucita zoipa. Komanso umatilepheletsa kucita zinthu zimene tidziŵa kuti ndiye zabwino, kapena zimene tiona kuti tingazikwanitse. Mwanjila imeneyi, ise anthu ndise akapolo a ucimo. Zotulukapo za ukapolo umenewu n’zakuti timakhala na nkhawa, timavutika, ndipo pamapeto pake timafa. (Aroma 6:23) Nthawi ina, zimenezi zinapangitsa mtumwi Paulo kuvutika kwambili maganizo. (Ŵelengani Aroma 7:21-25.) Tikadzamasulidwa ku ukapolo wa ucimo, m’pamene tidzakhala na ufulu weni-weni ngati umene makolo athu oyambilila anali nawo.

16. Tingacite ciani kuti tidzakhale na ufulu weni-weni?

16 Pamene Yesu anakamba kuti “mukamasunga mawu anga nthawi zonse,” anaonetsa kuti pali zinthu zina zimene tifunika kucita kapena malamulo amene tifunika kutsatila kuti iye atimasule. Monga Akhristu odzipeleka, tinadzikana tekha ndipo tinasankha kukhala na umoyo wotsatila ziphunzitso za Khristu monga ophunzila ake. (Mat.16:24) Monga mmene Yesu analonjezela, tidzakhala na ufulu weni-weni pamene tidzalandila madalitso onse a nsembe ya dipo lake.

17. (a) Tiyenela kucita ciani kuti tikhale na umoyo wacimwemwe na wokhutilitsa? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Kutsatila ziphunzitso za Yesu monga ophunzila ake, kudzatithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe na wokhutilitsa. Tikacita zimenezi, tidzakhala na mwayi wodzamasulidwa kothelatu ku ukapolo wa ucimo na imfa. (Ŵelengani Aroma 8:1, 2, 20, 21.) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene tingaseŵenzetsele mwanzelu ufulu umene tili nawo, kuti tipitilize kulemekeza Yehova, Mulungu wa ufulu weni-weni mpaka muyaya.