Onetsani Cikondi
Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
Tsankho limatenga nthawi kuti lithe. Mofanana na kalombo koyambitsa matenda, kamene kamafuna khama na nthawi kuti tikagonjetse, tsankho nalonso limafuna nthawi na khama kuti tilithetse. Kodi mungacite ciani kuti mucotse tsankho mumtima mwanu?
Mfundo ya m’Baibo
“Valani cikondi, pakuti cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” —AKOLOSE 3:14.
Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? Kucitila ena zinthu zabwino kumathandiza kuti muyambe kugwilizana nawo. Ndipo ngati muyesetsa kuonetsa cikondi kwa anthu, tsankho limacepela-cepela mumtima mwanu. Cikondi cikamakula mumtima mwanu, nawonso maganizo oipidwa na ŵanthu ŵena amacepa.
Zimene Mungacite
Ganizilani zimene mungacite poonetsa cikondi kwa anthu amene mumawaganizila kuti sali bwino. Zinthu zake sizicita kufunikila kukhala zapamwamba. Yesani kucita zinthu monga izi:
Cinthu ciliconse cabwino cimene mwacitila munthu, cimakuthandizani kucepetsa tsankho mumtima mwanu
Onetsani ulemu kwa anthu amenewo mwa kuwagwilila citseko kuti aloŵe kapena kupatsa mmodzi wa iwo malo anu okhala pamene muli pa ulendo.
Yesani kucezako nawo mwacidule, olo kuti mwina sadziŵa kukamba bwino citundu canu.
Khalani oleza mtima ngati acita zinthu m’njila imene muona kuti ni yacilendo.
Pamene afotokoza mavuto awo, onetsani kuti muwamvelela cifundo.