KWA OKWATILANA
3: Kulemekezana
ZIMENE KUMATANTHAUZA
Okwatilana amene amalemekezana, amacita zinthu moganizilana olo pamene asemphana maganizo. “Iwo saumilila maganizo awo. Koma amapitiliza kukambilana kuti athetse kusemphana maganizo. Aliyense wa iwo amamvetsela maganizo a mnzake mwaulemu, ndipo capamodzi amapeza njila yothetsela vutolo, imene onse angakhutile nayo.” N’zimene imakamba buku yakuti, Ten Lessons to Transform Your Marriage.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Cikondi . . . sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akorinto 13:4, 5.
“Kwa ine, kulemekeza mkazi wanga kumatanthauza kumuona kuti ni wofunika, ndipo sinifuna kucita ciliconse cimene cingam’khumudwitse, kapena kuwononga cikwati cathu.”—Micah.
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA
Ngati okwatilana salemekezana, angayambe kukamba mokalipilana, monyozana, komanso mopeputsana. Ocita kafuku-fuku amakamba kuti makhalidwe amenewa ni cizindikilo cakuti akhoza kudzasudzulana m’tsogolo.
“Kukamba mau onyoza mkazi wanu mom’pita mbali, kapena kum’kambila nthabwala zoipa, kudzapangitsa kuti ayambe kudziona kuti ni wosafunika, komanso angaleke kukudalilani, ndipo izi zingaononge cikwati canu.”—Brian.
ZIMENE MUNGACITE
DZIFUFUZENI
Kwa wiki imodzi, yesani kuona mmene mumakambila na mmene mucitila zinthu ndi mnzanu wa m’cikwati. Ndiyeno dzifunseni kuti:
-
‘Kodi mnzanga wa m’cikwati nam’nena kangati pa zimene walakwitsa? Nanga namuyamikilako kangati pa zimene wacita bwino?’
-
‘Kodi n’zinthu ziti zimene nacita zoonetsa kuti nimam’lemekeza mnzanga wa m’cikwati?’
KAMBILANANI NA MNZANU WA M’CIKWATI
-
Kodi mungacite ziti, kapena kukamba mau ati amene angathandize aliyense wa inu kudzimva kuti amalemekezedwa?
-
Kodi ni zocita ziti, kapena mau ati amene amapangitsa aliyense wa inu kudzimva kuti salemekezedwa?
MUNGACITENSO IZI
-
Lembani zinthu zitatu zimene mufuna kuti mnzanu wa m’cikwati azicita, zoonetsa kuti amakulemekezani. Ndipo pemphani mnzanuyo kucita cimodzi-modzi. Sinthanani zimene mwalemba, ndiyeno yambani kuseŵenzelapo pa mbali zimenezo kuti muzionetsana ulemu.
-
Lembani makhalidwe a mnzanu wa m’cikwati amene mumakonda. Ndiyeno muuzeni kuti mumawakonda kwambili makhalidwe amenewa.
“Kwa ine, kulemekeza mwamuna wanga kumatanthauza kumuonetsa m’zocita zanga kuti nimam’konda, ndipo nimafuna kuti azikondwela. Sikuti nthawi zonse nifunika kucita zinthu zazikulu, nthawi zina ngakhale m’zocita zing’ono-zing’ono ningamuonetse ulemu weni-weni.”—Megan.
Conco, cofunika kwambili n’cakuti mnzanu aziona kuti mumam’patsadi ulemu. Zilibe kanthu kaya imwe mumadziona kuti ndimwe aulemu kapena ayi.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Valani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”—Akolose 3:12.