DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU
2 | Tetezani Cuma Canu
CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
Tsiku lililonse, anthu ambili amavutika kupeza zinthu zofunikila pa umoyo. N’zacisoni kuti mavuto aakulu a m’dzikoli, amapangitsa zimenezi kukhala zovuta kwambili. Cifukwa ciyani?
-
M’madela amene kwacitika matsoka aakulu, zinthu monga cakudya komanso pokhala zimakwela mtengo kwambili.
-
Izi zimapangitsa kuti anthu ambili azilandila malipilo ocepa kapenanso kucotsedwa nchito kumene.
-
Matsoka angawononge kapena kusokoneza mabizinesi a anthu, nyumba zawo, na katundu wawo. Ndipo izi zingapangitse ambili kukhala paumphawi.
Zimene Muyenela Kudziŵa
-
Ngati mumaseŵenzetsa bwino ndalama zanu, mudzakwanitsa kupilila pa nthawi ya mavuto.
-
Kumbukilani kuti citetezo ca ndalama sicokhalitsa. Ndalama zimene mumapeza, zimene mumasunga ku banki, na zinthu zanu zamtengo wapatali zingathe mphamvu.
-
Pali zinthu zina zimene ndalama siingagule, monga cimwemwe komanso mgwilizano wabanja.
Zimene Mungacite Pali Pano
Baibo imati: “Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.
Kukhala okhutila kumatanthauza kusalakalaka zambili, komanso kukhala wacimwemwe malinga ngati tili na zofunikila za tsiku na tsiku. Izi n’zofunika kwambili makamaka ngati tili na ndalama zocepa.
Kuti mukhale wokhutila, mungafunike kusinthako zinthu zina pa umoyo wanu. Ngati mumagula zinthu zodula kuposa ndalama zimene mumapeza, mudzakhala na mavuto aakulu a ndalama.