Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 15

N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?

N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?

1. Kodi mudzapindula bwanji mukapitiliza kuphunzila Baibo?

Mosakaikila, ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo zimene mwaphunzila zalimbitsa cikondi canu pa Yehova. Tifunikila kupitiliza kulimbitsa cikondi cimeneci. (1 Petulo 2:2) Kuti mukakhale ndi moyo wosatha mufunika kupitiliza kuyandikila kwa Mulungu mwa kuphunzila Mau ake.​—Ŵelengani Yohane 17:3; Yuda 21.

Mukamudziŵa bwino kwambili Mulungu, cikhulupililo canu cidzakhala colimba ndipo cidzakuthandizani kumukondweletsa. (Aheberi 11:1, 6) Cidzakulimbikitsani kulapa ndi kusintha zinthu pa umoyo wanu.​—Ŵelengani Machitidwe 3:19.

2. Kodi kudziŵa kwanu Mulungu kungathandize bwanji ena?

Mungakhale ndi ubwenzi wapadela ndi Yehova

Mwacibadwa, mudzafuna kuuzako ena zimene mwaphunzila. Tonse timakondwela tikamalalikila uthenga wabwino. Pamene mupitiliza kuphunzila Baibo, mudzaphunzila mmene mungaigwilitsile nchito pofotokoza cikhulupililo canu mwa Yehova. Ndipo mudzaphunzilanso mmene mungaigwilitsile nchito pofotokoza uthenga wabwino.​—Ŵelengani Aroma 10:13-15.

Anthu ambili amayamba kuuzako mabwenzi kapena acibanja ao uthenga wabwino. Koma muzikhala osamala pocita zimenezi. M’malo moŵauza kuti zimene amakhulupilila n’zabodza, muziŵauza za malonjezo a Mulungu. Ndiponso, muzikumbukila kuti nthawi zambili anthu amacita cidwi ndi khalidwe lanu kuposa zimene mumakamba.​—Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, 25.

3. Kodi ndi ubwenzi wanji umene mungakhale nao ndi Mulungu?

Kuphunzila Mau a Mulungu kudzakuthandizani kuti mukule kuuzimu. Posapita nthawi, mungakhale paubwenzi wapadela ndi Yehova. Mungakhalenso m’banja lake.​—Ŵelengani 2 Akorinto 6:18.

4. Kodi mufunika kucita ciani kuti mupitilize kukula kuuzimu?

Mungakule kuuzimu mwa kupitiliza kuphunzila Mau a Mulungu. (Aheberi 5:13, 14) Pemphani mmodzi wa Mboni za Yehova kuti ayambe kuphunzila nanu Baibo m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Mukaphunzila zambili ponena za Mau a Mulungu, m’pamene umoyo wanu udzakhala waphindu.​—Ŵelengani Salimo 1:1-3; 73:27, 28.

Uthenga wabwino umacokela kwa Yehova, amene ndi Mulungu wacimwemwe. Mungamuyandikile Mulungu mwa kuyandikila anthu ake. (Aheberi 10:24, 25) Mukamapitiliza mwakhama kukondweletsa Yehova, ndiye kuti mukuyesa-yesa kuti mukapeze moyo weni-weni umene ndi moyo wosatha. Kuyandikila Mulungu ndi cinthu cabwino kwambili cimene mungacite.​—Ŵelengani 1 Timoteyo 1:11; 6:19.