Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 1

Kodi Uthenga Wabwino n’Ciani?

Kodi Uthenga Wabwino n’Ciani?

1. Kodi uthenga wocokela kwa Mulungu ndi wotani?

Mulungu afuna kuti anthu asangalale ndi umoyo padziko lapansi. Iye analenga dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo cifukwa cakuti amakonda anthu. Posacedwapa, adzacitapo kanthu kuti abweletse tsogolo labwino kwa anthu onse. Iye adzapulumutsa mtundu wa anthu ku mavuto onse.—Ŵelengani Yeremiya 29:11.

Palibe boma limene linakwanitsapo kuthetsa ciwawa, matenda, kapena imfa. Koma uthenga wabwino ndi wakuti, posacedwapa, boma la Mulungu lidzaloŵa m’malo mwa maboma onse a anthu. Nzika zake zidzakhala ndi thanzi labwino ndipo zidzakhala pamtendele.—Ŵelengani Yesaya 25:8; 33:24; Danieli 2:44.

2. N’cifukwa ciani uthenga wabwino uli wofunika kwambili?

Mavuto adzatha kokha pamene Mulungu adzacotsa anthu oipa padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) Kodi zimenezi zidzacitika liti? Mau a Mulungu anakambilatu za mavuto amene angaononge mtundu wa anthu. Zinthu zoipa zimene zicitika pa dziko lapansi zimaonetsa kuti nthawi yakuti Mulungu acitepo kanthu ili pafupi kwambili.—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5.

3. Kodi tiyenela kucita ciani?

Tiyenela kuphunzila za Mulungu m’Mau ake, Baibo. Ili ngati kalata imene atate acikondi atilembela. Imatiuza mmene tingakhalile ndi umoyo wabwino panthawi ino, ndi mmene tingakhalile ndi moyo wosatha mtsogolo pa dziko lapansi. N’zoona kuti anzanu ena sangakonde kuti anthu ena azikuthandizani kumvetsetsa Baibo. Koma popeza kuti Mulungu watilonjeza tsogolo labwino, musalole kuti anthu ena akulepheletseni kuphunzila Baibo.—Ŵelengani Miyambo 29:25; Chivumbulutso 14:6, 7.