Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu kwa Osonkhana

Mawu kwa Osonkhana

AKALINDE Akalinde alipo kuti akutumikileni. Conde, gwilizanani nawo mwa kutsatila malangizo awo okhudza koika mamotoka, kutsogolela anthu, kusungilatu malo okhala, na nkhani zina.

UBATIZO Opita ku ubatizo ayenela kukhala pamalo amene awasungila kutsogolo kwa pulatifomu, kusiyapo ngati pakonzedwa malo ena. Ayenela kutelo ikalibe kuyamba nkhani ya ubatizo pa Tsiku Laciŵili kum’maŵa. Aliyense ayenela kubweletsa thaulo na covala caulemu coloŵa naco m’madzi.

ZOPELEKA Pamatayika ndalama zambili kuti palinganizidwe malo okhala okwanila, zolankhulila, na zina zonse zofunikila kuti msonkhano ukhale wotsitsimula, na kutithandiza kuyandikila Yehova. Ndalama zimenezo zimacokela pa zopeleka zanu zaufulu, ndipo zimathandizanso panchito yathu ya padziko lonse. Pofuna kupeputsa zinthu, mudzaona tumabokosi tolembedwa bwino pamalo osiyana-siyana pamsonkhano uno. Mungacitenso zopeleka kupitila pa intaneti mwa kuyenda pa copeleka. donate.jw.org. Timayamikila kwambili zopeleka zanu zonse. Maka-maka Bungwe Lolamulila limayamikila ngako kuwolowa manja kwanu kocilikiza zinthu za Ufumu.

CITHANDIZO CA ODWALA Conde, kumbukilani kuti Dipatimenti ya Cithandizo ca Odwala ni ya zakugwa mwadzidzidzi cabe.

CIPINDA CA ZOTAIKA Zinthu zonse zopezeka ziyenela kupelekedwa ku Dipatimenti ya Zotaika. Ngati mwataya ciliconse, pitani ku dipatimenti imeneyi kuti mukafotokoze cimene mwataya. Ana amene asoŵa kwa makolo awo, nawonso ayenela kupelekedwa ku dipatimenti imeneyi. Komabe, kuti tisavutitse ena, conde tiyeni tisamale bwino ana athu, na kukhala nawo pamodzi.

MALO OKHALA Conde, ganizilani anzanu. Kumbukilani kuti, mungangosungila malo anthu amene mudzayenda nawo pamodzi, amene mukhala nawo nyumba imodzi, kapena amene mumaphunzila nawo Baibo. Conde, ngati simusungila wina malo, musaike zinthu pamalo amene ena afunika kukhalapo.

NCHITO YODZIPELEKA Ngati mufuna kuthandizako nchito pa msonkhano uno, pitani ku Dipatimenti ya Nchito Yodzipeleka, ndipo adzakuuzani zofunika kucita.

MITING’I YAPADELA

Sukulu ya Alengezi a Ufumu Apainiya a zaka zapakati pa 23 na 65 amene afuna kuwonjezela utumiki wawo, akupemphedwa kukapezeka pamiting’i ya ofuna kuloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, pa Tsiku Lacitatu la msonkhano uno. Tidzalengeza malo na nthawi pasadakhale.

Wokonzedwa na Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova

© 2020 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania