PHUNZILO 37
Yehova Akamba na Samueli
Mkulu wa Ansembe wina, Eli, anali ndi ana aamuna aŵili amene anali kutumikila pa cihema. Maina awo anali Hofeni na Pinihasi. Iwo sanali kumvela malamulo a Yehova, ndipo anali kucitila anthu zinthu zoipa kwambili. Amati Aisiraeli akabweletsa nsembe kwa Yehova, Hofeni na Pinihasi anali kutengapo nyama yabwino kwambili kuti akadye. Eli anamvela zimene ana ake anali kucita, koma sanacitepo kanthu. Kodi Yehova analekelela zimenezi?
Olo kuti Samueli anali wamng’ono kwambili poyelekezela na Hofeni na Pinihasi, iye sanatengele khalidwe lawo. Yehova anali kum’konda Samueli. Tsiku lina atagona usiku, Samueli anamvela mawu oitana dzina lake. Anauka, n’kuthamangila kwa Eli, na kuyankha kuti: ‘Nili pano!’ Koma Eli anamuuza kuti: ‘Sin’nakuitane. Yenda ukagone.’ Samueli anapita kukagona. Koma anamvelanso kuitana. Pamene Samueli anamvela kuitana kacitatu, Eli anazindikila kuti Yehova ndiye anali kuitana Samueli. Conco, anauza Samueli kuti ngati adzamvelanso mawu omuitana, ayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova, ine mtumiki wanu nikumvetsela.’
Samueli anayendanso kukagona. Koma anamvelanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Pamenepo anayankha kuti: ‘Lankhulani, ine
mtumiki wanu nikumvetsela.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Umuuze Eli kuti nidzamulanga pamodzi na banja lake. Iye adziŵa kuti ana ake akucita zinthu zoipa kwambili pa cihema canga. Koma sacitapo kanthu.’ M’mawa mwake, Samueli anatsegula zitseko za cihema, monga anali kucitila nthawi zonse. Iye anacita mantha kuti auze mkulu wa ansembe zimene Yehova anamuuza. Koma Eli anamuitana na kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova anakuuza ciani? Niuze zonse.’ Conco Samueli anafotokozela Eli zonse.Pamene Samueli anali kukula, Yehova anapitiliza kukhala naye. Aisiraeli onse anali kudziŵa kuti Yehova anasankha Samueli kukhala mneneli ndi woweluza.
“Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”—Mlaliki 12:1