Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 18

Citsamba Coyaka Moto

Citsamba Coyaka Moto

Mose anakhala ku Midiyani kwa zaka 40. Anakwatila na kukhala ndi ana. Tsiku lina, pamene anali kulishila mbelele, kapena kuti nkhosa, pafupi na Phili la Sinai, anaona zodabwitsa kwambili. Citsamba cinali kuyaka moto, koma osapsa! Pamene anafika pafupi kuti aone, anamvela mawu kucokela m’citsamba muja akuti: ‘Mose! Usafike pafupi. Vula nsapato zako, cifukwa malo amene waimapo ni oyela.’ Yehova ndiye anali kukamba kupitila mwa mngelo.

Mose anacita mantha, ndipo anabisa nkhope yake. Mawuwo anati: ‘Naona kuvutika kwa Aisiraeli. Nidzawapulumutsa m’manja mwa Aiguputo, na kuwaloŵetsa m’dziko labwino. Iwe ndiwe udzatulutsa anthu anga mu Iguputo.’ Izi zinam’dabwitsa kwambili Mose, siconco?

Koma Mose anafunsa kuti: ‘Nidzawayankha ciani anthu akakanifunsa kuti n’ndani wakutuma?’ Mulungu anayankha kuti: ‘Ukawauze kuti Yehova, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo ndiye wanituma.’ Ndiyeno Mose anati: ‘Bwanji ngati anthu sadzamvela mawu anga?’ Yehova anapatsa Mose umboni woonetsa kuti adzamuthandiza. Anauza Mose kuti aponye ndodo yake pansi. Ataiponya pansi, inasanduka njoka! Pamene Mose anaigwila kum’cila, inasandukanso ndodo. Yehova anati: ‘Ukakaonetsa cizindikilo ici, cidzapeleka umboni wakuti ndine n’nakutuma.’

Koma Mose anati: ‘Sinikutha kukamba bwino.’ Yehova anam’lonjeza kuti: ‘Nidzakuuza zimene ukakambe, ndipo nidzatuma Aroni m’bale wako kuti akakuthandize.’ Podziŵa kuti Yehova anali naye, Mose anatenga mkazi wake komanso ana ake, na kubwelela ku Iguputo.

“Musade nkhawa za mmene mukalankhulile kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.”—Mateyu 10:19