Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 11

Cikhulupililo Ciyesedwa

Cikhulupililo Ciyesedwa

Abulahamu anaphunzitsa mwana wake Isaki kukonda Yehova na kukhulupilila malonjezo onse a Yehova. Koma Isaki atafika zaka pafupi-fupi 25, Yehova anauza Abulahamu kucita cinthu covuta kwambili. Kodi anamuuza kucita ciani?

Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupeleke nsembe pa phili ku Moriya.’ Abulahamu sanadziŵe cifukwa cake Yehova anamuuza kuti acite zimenezo. Koma anamvelelabe Yehova.

M’mamaŵa tsiku lotsatila, Abulahamu anatenga Isaki na atumiki ake aŵili kuloŵela ku phili la Moriya. Atayenda kwa masiku atatu, anayamba kuona mapili capatali. Abulahamu anauza atumiki ake kuti ayembekeze, pamene iye na Isaki apita kukapeleka nsembe. Abulahamu anapatsa Isaki nkhuni kuti anyamule, ndipo iye anatenga mpeni. Isaki anafunsa atate ake kuti: ‘Nanga nyama yokapeleka nsembe ili kuti?’ Abulahamu anayankha kuti: ‘Mwana wanga, Yehova adzatipatsa.’

Atafika ku phililo, anamanga guwa la nsembe. Ndiyeno, Abulahamu anamanga Isaki kumanja na kumendo, na kum’goneka pa guwa la nsembelo.

Kenako Abulahamu anatenga mpeni. Pa nthawiyo, mngelo wa Yehova anaitana kucokela kumwamba kuti: ‘Abulahamu! Usamuphe mwanayo! Lomba nadziŵa kuti uli na cikhulupililo mwa Mulungu, cifukwa sunakane kupeleka mwana wako nsembe.’ Ndiyeno Abulahamu anaona nkhosa itakodwa na nyanga zake mu ziyango-yango. Mwamsanga anamasula Isaki, na kupeleka nkhosa nsembe m’malo mwa mwana wake.

Kucokela tsiku limenelo, Yehova anacha Abulahamu kuti ni bwenzi lake. Udziŵa cifukwa cake? Abulahamu anali kucita zonse zimene Yehova anamuuza, ngakhale pamene sanamvetsetse cifukwa cake Yehova anamuuza kucita zinthuzo.

Yehova anabwelezela lonjezo lake kwa Abulahamu kuti: ‘Nidzakudalitsa ndi kuculukitsa mbewu yako, kapena kuti ana ako.’ Yehova analonjezanso kudalitsa anthu onse abwino kupitila m’badwa ya Abulahamu.

“Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16