Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 99

Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi

Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi

Ku Filipi, kunali mtsikana wina wanchito amene anali na ciŵanda. Ciŵandaco cinali kum’pangitsa kulosela zakutsogolo. Mwanjila imeneyo, anali kupangila mabwana ake ndalama zambili. Paulo na Sila atafika ku Filipi, mtsikana uja anawalondola kulikonse kwa masiku ambili. Ndipo ciŵandaco cinam’pangitsa kumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba!” Paulo atalema nazo, anauza ciŵandaco kuti: ‘M’dzina la Yesu, tuluka mwa mtsikanayu!’ Pamenepo, ciŵanda cija cinacoka mwa mtsikanayo.

Mabwana a mtsikanayo ataona kuti Paulo wacotsapo njila yawo yopangila ndalama kupitila mwa mtsikana uja, anakalipa kwambili. Anagwila Paulo na Sila na kuŵapeleka kwa oweluza milandu. Atafika kumeneko iwo anati: ‘Anthu awa akuphwanya malamulo, ndipo akusokoneza mzinda wonse!’ Oweluzawo analamula kuti am’kwapule Paulo na Sila, na kuwaponya m’ndende. Woyang’anila ndende anawaika m’cipinda ca mkati-kati ca ndende, kumene kunali mdima wa ndiwe yani, na kuwamanga m’matangadza.

Ali m’ndendemo, Paulo na Sila anali kuimbila Yehova zitamando, ndipo akaidi ena anali kumvetsela. Ndiyeno pakati pa usiku, mwadzidzidzi panacitika civomezi camphamvu cimene cinagwedeza ndende yonseyo. Zitseko za ndendeyo zinatseguka, ndipo unyolo na matangadza anamasuka. Pamenepo woyang’anila ndendeyo anathamanga kuloŵa mkati-kati mwa ndendeyo. Anangoona kuti zitseko zonse n’zotseguka. Poganiza kuti akaidi onse athaŵa, iye anasolola lupanga kuti adziphe.

Koma Paulo anafuula kuti: ‘Usadzivulaze! Tonse tilimo!’ Woyang’anila ndendeyo anathamanga kukagwada pamaso pa Paulo na Sila. Iye anaŵafunsa kuti: “Ndicite ciyani kuti ndipulumuke?” Iwo anamuyankha kuti: ‘Iweyo, komanso onse a m’banja mwako mufunika kukhulupilila mwa Yesu.’ Kenako Paulo na Sila anaŵaphunzitsa mawu a Yehova, ndipo woyang’anila ndendeyo na onse a m’banja lake anabatizika.

“Anthu adzakugwilani ndi kukuzunzani, adzakupelekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakutengelani kwa mafumu ndi abwanamkubwa cifukwa ca dzina langa. Umenewu udzakhala mpata wanu wocitila umboni.”—Luka 21:12, 13