PHUNZILO 86
Yesu Aukitsa Lazaro
Yesu anali na anzake a pa mtima atatu, amene anali kukhala ku Betaniya. Anzakewo anali Lazaro, na azilongosi ake aŵili, Mariya na Marita. Tsiku lina, Yesu ali ku tauni ya Pereya, Mariya na Marita anatumiza uthenga wa matenda a kaya-kaya kwa Yesu. Iwo anati: ‘Lazaro ni wodwala kwambili. Conde bwelani mwamsanga!’ Koma Yesu sanapite nthawi imeneyo. Patapita masiku aŵili, m’pamene anauza ophunzila ake kuti: ‘Tiyeni ku Betaniya. Lazaro ali m’tulo akugona, tikafika nidzamuutsa.’ Atumwiwo anati: ‘Ngati Lazaro ali m’tulo, kugonako kudzam’thandiza kuti acile.’ Conco Yesu anawauza mochulilatu kuti: ‘Lazaro wamwalila.’
Yesu pofika ku Betaniya, n’kuti Lazaro atagona m’manda kwa masiku anayi. Anthu ambili anali kumeneko kudzatonthoza Marita na Mariya. Marita atamvela kuti Yesu wabwela, anathamanga kukakumana naye. Ndiyeno Marita anati: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongosi wanga sakanamwalila.” Yesu anamuuza kuti: ‘Mlongosi wako adzakhalanso na moyo. Kodi ukhulupilila zimenezi Marita?’ Poyankha Marita anati: ‘Nikhulupilila kuti adzauka pa kuuka kwa akufa.’ Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka na moyo.”
Kenako Marita anapita kukauza Mariya kuti: ‘Yesu wabwela.’ Mariya anathamanga kupita kwa Yesu, ndipo khamu la anthu linam’londola. Atafika anagwada pansi pa mapazi a Yesu, akulila kuti: ‘Ambuye, mukanakhala kuno, sembe mlongo wathu ali moyo!’ Yesu anaona mmene Mariya anavutikila mu mtima. Basi nayenso anayamba kulila. Anthu ataona kuti Yesu akugwetsa misozi, anati: ‘Onani, Yesu anali kum’kondadi Lazaro.’ Koma ena anafunsa kuti: ‘Nanga n’cifukwa ciani sanabwele kudzam’cilitsa mnzake?’ Kodi Yesu anacita ciani?
Yesu anapita ku manda kumene anaika Lazaro. Pa mandapo anavalapo na cimwala cacikulu. Iye analamula kuti: ‘Cotsani cimwala ici.’ Pamenepo Marita anati: ‘Koma pofika lelo akwana masiku anayi! Ayenela kuti thupi lake linayamba kununkha.’ Koma anthuwo anacotsabe cimwala cija. Ndiyeno Yesu anapemphela kuti:
‘Atate, zikomo kuti mwanimvela. Nidziŵa kuti nthawi zonse mumanimvela. Koma nipemphela mokweza mawu kuti anthu awa adziŵe kuti ndinu munanituma.’ Kenako anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Panacitika zodabwitsa: Anthu anangoona Lazaro uyo watuluka, thupi lake likali cikulungile m’nsalu za kumanda. Yesu anati: “M’masuleni, mlekeni apite.”Poona izi, ambili anakhulupilila mwa Yesu. Koma ena anapita kukauza Afarisi. Kucokela pa nthawiyo, Afarisi anayamba kufuna-funa mpata wakuti aphe onse aŵili, Lazaro na Yesu. M’pamene mmodzi wa atumwi 12, Yudasi Isikariyoti, anapita kwa Afarisi n’kukafunsa kuti: ‘Mudzanipatsa zingati kuti nikuthandizeni kugwila Yesu?’ Iwo analonjeza kum’patsa ndalama 30 zasiliva. Basi Yudasi anayamba kufuna-funa mpata wakuti apeleke Yesu kwa Afarisi.
“Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa. Ndipo njila zopulumukila ku imfa ndi za Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”—Salimo 68:20