Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 55

Thandizani Mpingo Wanu

Thandizani Mpingo Wanu

Zungulile dziko lapansi, anthu mamiliyoni akusangalala polambila Yehova m’mipingo masauzande ambili-mbili. Iwo amayamikila cilangizo na citsogozo cimene amalandila. Ndipo amathandiza mipingo yawo mofunitsitsa m’njila zambili. Kodi inunso mumayamikila ndipo ndinu wokondwa kukhala mu mpingo wanu? Ndipo kodi ndinu wofunitsitsa kuuthandiza?

1. Kodi ni njila ziti zimene mungagwilitse nchito nthawi yanu na mphamvu zanu kuthandiza mpingo?

Aliyense wa ife akhoza kucitapo kanthu kuti azithandiza mpingo wawo. Mwacitsanzo, kodi mu mpingo wanu alimo okalamba kapena odwala? Kodi mungawathandize kupita ku misonkhano kapena kuwathandiza pa zinthu zina, monga kukagula zinthu kapena nchito zapakhomo? (Ŵelengani Yakobo 1:27.) Kuwonjezela apo, tingadzipeleke kuthandiza pa nchito yoyeletsa Nyumba yathu ya Ufumu kapena kukonza zowonongeka. Palibe amene amatikakamiza kucita zinthu zimenezi. Cikondi cathu pa Mulungu komanso abale athu ndico cimatikolezela kuti ‘tidzipeleke mofunitsitsa.’Salimo 110:3.

Palinso njila zina zimene a Mboni obatizika angathandizile mpingo wawo. Abale ofikapo kuuzimu angayenelele kukhala atumiki othandiza, ndipo m’kupita kwa nthawi angakhale akulu. Komanso, abale ngakhale alongo angathandize mpingo pokhala apainiya kuti apititse patsogolo nchito yolalikila. A Mboni ena angathandize mwa kumanga nawo malo olambililapo, kapena kusamukila kudela kumene mpingo wina ukufunikila thandizo m’njila zina.

2. Kodi tingaseŵezetse bwanji zinthu zathu pothandiza mpingo?

Tikhoza ‘kulemekeza Yehova na zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miyambo 3:9.) Umakhaladi mwayi wathu kucita copeleka ca ndalama na zinthu zina kuti tithandize mpingo wathu, komanso kuti tipititse patsogolo nchito yolalikila padziko lonse. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:7.) Zopeleka zathu zimathandizanso pakagwa zocitika zadzidzidzi. Ambili a ife nthawi na nthawi ‘timaika kenakake pambali’ ka copeleka. (Ŵelengani 1 Akorinto 16:2.) Zopeleka zathu tingaziponye mu tumabokosi pamalo athu olambilila, kapena tingazitumize pa Intaneti pa donate.jw.org. Yehova amatipatsa mwayi wakuti tionetse cikondi cathu pa iye pogwilitsa nchito ndalama komanso zinthu zathu kuthandiza mpingo.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani njila zimene mungathandizile mpingo wanu.

3. Tingathandize pogwilitsa nchito zinthu zathu

Yehova amakonda anthu opatsa mokondwela. Yesu naye n’cimodzi-modzi. Mwacitsanzo, Yesu anacita cidwi na mkazi wamasiye wosauka, amene anali wofunitsitsa kucita copeleka. Ŵelengani Luka 21:1-4, na kukambilana mafunso aya:

  • Kuti tikondweletse Yehova, kodi tiyenela kucita copeleka ca ndalama zambili?

  • Kodi Yehova na Yesu amamva bwanji tikamapeleka na mtima wonse?

Kuti mudziŵe mmene zopeleka zathu zimagwilila nchito, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi zopeleka zimagwila nchito zanji pothandiza mipingo padziko lonse?

4. Tiyeni tidzipeleke kuti tithandize

Mu nthawi zamakedzana, alambili a Yehova anali kugwila nchito mokangalika kuti malo awo olambilila azikhala osamalika. Zimenezi zinali kutheka osati cabe mwa zopeleka za ndalama ayi. Ŵelengani 2 Mbiri 34:9-11, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Mwisiraeli aliyense anali kuthandiza bwanji kusamalila nyumba ya Yehova, kapena kuti malo olambilila?

Kuti muone mmene Mboni za Yehova zimatengela citsanzo ca atumiki amakedzana amenewo, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani mafunso otsatila.

  • N’cifukwa ciyani kuli kofunika kusunga Nyumba yathu ya Ufumu ili yaukhondo komanso yosamalika?

  • Nanga inu mungathandize mu njila ziti?

5. Abale ayenela kulimbikila kuti ayenelele maudindo

Malemba amalimbikitsa amuna acikhristu kucita zonse zotheka kuti athandize mpingo. Kuti muone citsanzo, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi Ryan analimbikila motani kuti athandize mpingo?

Baibo imafotokoza ziyenelezo zimene abale ayenela kuzikwanilitsa kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu. Ŵelengani 1 Timoteyo 3:1-13, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi abale amene amalimbikila kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu, ayenela kukhala anthu otani?

  • Nanga mabanja awo ayenela kukhala otani?—Onani vesi 4 na 11.

  • Abale akalimbikila kukwanilitsa ziyenelezo zimenezi, kodi aliyense mu mpingo amapindula motani?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi a Mboni za Yehova amazipeza kuti ndalama zoyendetsela nchito yawo?”

  • Kodi inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Yehova amayamikila kwambili pamene tiyesetsa kuthandiza mpingo na nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso zinthu zathu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi tingagwilitse nchito bwanji nthawi yathu na mphamvu zathu kuthandiza mpingo?

  • Nanga tingaseŵenzetse bwanji zinthu zathu kuthandiza mpingo?

  • Kodi inu pacanu mungafune kuthandiza mpingo mu njila ziti?

Colinga

FUFUZANI

Onani cifukwa cake Mulungu sakulamulanso kuti olambila ake azipeleka cakhumi.

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopereka Chakhumi?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani kuti “kukalamila,” kapena kuti kulimbikila, kuti muyenelele udindo mu mpingo kutanthauza ciyani.

“Kodi Mukukalamila Udindo?” (Nsanja ya Mlonda, September 15, 2014)

Onani a Mboni ena olimba mtima amene amadzipeleka na mtima wonse kuti apeleke zofalitsa kwa olambila anzawo.

Mmene Zofalitsa Zathu Zimawafikila Anthu mu Congo (4:25)

Dziŵani mmene timapezela ndalama zoyendetsela nchito yathu mosiyana kwambili na zipembedzo zina.

“Kodi Ndalama Zoyendetsela Nchito ya Mboni za Yehova Zimacokela Kuti?” (Nkhani ya pawebusaiti)