Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 33

Zimene Ufumu wa Mulungu Udzacita

Zimene Ufumu wa Mulungu Udzacita

Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulila. Ndipo posacedwa udzapanga masinthidwe aakulu padziko lapansi. Tiyeni tsopano, tione zina mwa zinthu zabwino zimene tikuyembekezela pansi pa ulamulilo wa Ufumuwo.

1. Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwezeletsa bwanji mtendele na cilungamo padziko lapansi?

Yesu, Mfumu yoikidwa na Mulungu kumwamba, adzawononga anthu oipa na maboma awo pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi imeneyo, lonjezo la m’Baibo lidzakwanilitsidwa kwathunthu limene limati: “Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso.” (Salimo 37:10) Pogwilitsa nchito Ufumu wa Mulungu, Yesu adzaonetsetsa kuti mtendele na cilungamo zili paliponse padziko lapansi.—Ŵelengani Yesaya 11:4.

2. Cifunilo ca Mulungu cikadzacitika padziko lapansi, kodi tidzakhala na umoyo wotani?

Pansi pa ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu, “olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Tangoganizani kukhala m’dziko limene munthu aliyense ni wolungama, ndipo aliyense amakonda Yehova na anthu anzake! Sipadzapezeka wodwala, ndipo anthu onse adzakhala na moyo kwamuyaya.

3. Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciyani anthu oipa akadzawonongedwa?

Anthu oipa akadzacotsedwapo, Yesu adzalamulila monga Mfumu kwa zaka 1,000. Pa nthawiyo, iye komanso olamulila anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu padziko lapansi kukhala angwilo, kapena kuti opanda ucimo. Zaka 1,000 zimenezo zikadzatha, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso wokongola. Anthu onse m’dzikolo adzakhala acimwemwe cifukwa comvela malamulo a Yehova. Ndiyeno, Yesu adzabwezela ulamulilowo kwa Yehova, Atate wake. Kuposa n’kale lonse, ‘dzina [la Yehova] lidzayeletsedwa.’ (Mateyu 6:9, 10) Pa nthawiyo, zidzakhala zitatsimikizika kuti Yehova ndiye Wolamulila wabwino, amene amasamala anthu ake. Kenako, Yehova adzawononga kothelatu Satana na ziŵanda zake, komanso anthu onse opandukila ulamulilo Wake. (Chivumbulutso 20:7-10) Zabwino zonse zimene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa zidzakhalapo kwamuyaya.

KUMBANI MOZAMILAPO

Pezani cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Mulungu adzagwilitsa nchito Ufumu wake kukwanilitsa malonjezo onse a m’Baibo akutsogolo.

4. Ufumu wa Mulungu udzacotsapo maboma onse a anthu

“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.” (Mlaliki 8:9) Yehova adzagwilitsa nchito Ufumu wake kucotsapo zopanda cilungamo.

Ŵelengani Danieli 2:44, komanso 2 Atesalonika 1:6-8, kenako kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yehova na Mwana wake Yesu, adzacita nawo ciyani maboma a anthu komanso amene ali ku mbali yawo?

  • Kodi zimene mwaphunzila zokhudza Yehova na Yesu, zakuthandizani bwanji kukhulupilila kuti zimene iwo adzacite zidzakhala zoyenela komanso zacilungamo?

5. Yesu ndiye Mfumu yabwino kopambana

Monga Mfumu yoikidwa na Mulungu, Yesu adzacita zambili kuti adzapindulitse anthu padziko lapansi. Tambani VIDIYO kuti muone mmene Yesu anaonetsela kale kuti ni wofunitsitsa kuthandiza anthu, komanso kuti ali na mphamvu zocokela kwa Mulungu zocita zimenezo.

Pamene anali padziko lapansi, Yesu anapeleka citsanzo ca zimene Ufumu wa Mulungu udzacita. Pa madalitso ondandalikidwa aya, ni ati amene mukuyembekezela mwacidwi kudzaona? Ŵelengani Malemba ake ofotokoza madalitso amenewa.

ALI PADZIKO LAPANSI, YESU . . .

KUCOKELA KUMWAMBA, YESU . . .

  • adzakonza zonse zacilengedwe zowonongeka padziko lapansi.—Yesaya 35:1, 2.

  • adzacotsa njala padziko lapansi—Salimo 72:16.

  • adzaonetsetsa kuti anthu onse akhala na thanzi langwilo.—Yesaya 33:24.

  • adzaukitsa amene anafa na kucotsapo imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.

6. Ufumu wa Mulungu udzabweletsa tsogolo labwino kwambili

Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa colinga ca Yehova capoyamba kwa anthu. Ndipo anthuwo adzakhala kwamuyaya m’paradaiso padziko lapansi Tambani VIDIYO kuti muone mmene Yehova, kupitila mwa Mwana wake Yesu, akukwanilitsila colinga Cake.

Ŵelengani Salimo 145:16, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji kudziŵa kuti Yehova adzakhutilitsa “zokhumba za camoyo ciliconse”?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ngati tingavotele Boma la olamulila acilungamo, lingacotsepo mavuto onse a anthu.”

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzacotsapo mavuto ati amene maboma a anthu sangathe kuwathetsa?

CIDULE CAKE

Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa colinga cake. Udzasintha dziko lonse lapansi kukhala paradaiso wodzaza anthu abwino amene adzalambile Yehova kwamuyaya.

Mafunso Obweleza

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzayeletsa bwanji dzina la Yehova?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa malonjezo a m’Baibo?

  • Pa zimene Ufumuwo udzacita, n’ciyani cimene mukuyembekezela mwacidwi?

Colinga

FUFUZANI

Ŵelengani zimene zidzacitike mkati mwa ulamulilo wa Yesu wa zaka 1,000, komanso kumapeto kwake.

“Kodi pa Tsiku la Ciweluzo Padzacitika Zotani?” (Nsanja ya Mlonda, September 1, 2012)

Onani mmene mabanja angayelekezele capamodzi kuti ali m’Paradaiso.

Muziyelekeza Kuti Muli m’Paradaiso (1:50)

Mu nkhani yakuti “N’nali na Mafunso Ambili Omwe Anali Kunisowetsa Mtendele,” onani mmene wandale wopandukila boma anapezela mayankho okhutilitsa.

“Baibo Imasintha Anthu” (Nsanja ya Mlonda, January 1, 2012)