Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 32

Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!

Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!

Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila kumwamba mu 1914. M’pamenenso anayamba masiku otsiliza a ulamulilo wa anthu. Tidziŵa bwanji zimenezi? Tidzakambilana maulosi a m’Baibo, zocitika za padziko, komanso makhalidwe a ŵanthu kucokela mu 1914.

1. Kodi maulosi a m’Baibo anakambilatu ciyani?

M’Baibo, buku la Danieli linaonetselatu kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila kumapeto kwa nyengo yochedwa “nthawi zokwanila 7.” (Danieli 4:16, 17) Patapita zaka mahandiledi, nyengo imodzi-modziyo Yesu anaichula kuti “nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu.” Ndipo iye anaphunzitsa kuti nyengo imeneyo inali isanathe. (Luka 21:24) Monga mmene tionele, nthawi zokwanila 7 zimenezo zinatha m’caka ca 1914.

2. Kucokela mu 1914, kodi padziko pakhala pakucitika zinthu zotani, ndipo anthu akuonetsa makhalidwe otani?

Ophunzila a Yesu anamufunsa kuti: “Kodi . . . cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciyani?” (Mateyu 24:3) Powayankha, Yesu ananenelatu zinthu zambili zodzacitika pambuyo pakuti iye wayamba kulamulila kumwamba mu Ufumu wa Mulungu. Zina mwa zocitikazo zikuphatikizapo nkhondo, njala, na zivomezi. (Ŵelengani Mateyu 24:7.) Baibo inakambilatunso kuti mu “masiku otsiliza” anthu adzakhala na makhalidwe opangitsa umoyo kukhala wovuta. (2 Timoteyo 3:1-5) Zocitika zimenezi, komanso makhalidwe a anthu amenewa, zaonekela kwambili maka-maka kuyambila mu 1914.

3. N’cifukwa ciyani zinthu zaipa kwambili conco padzikoli kucokela pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila?

Yesu atangoikidwa kukhala Mfumu, kumwamba kunabuka nkhondo pakati pa iye na Satana pamodzi na ziŵanda zake. Pa nkhondoyo Satana anagonjetsedwa. Baibo imakamba kuti “iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ni wokwiya kwambili cifukwa akudziŵa kuti adzawonongedwa. Conco, iye amacititsa mavuto ambili komanso zopweteka padziko lapansi. Ndiye cifukwa cake zinthu zafika poipa kwambili padziko! Koma Ufumu wa Mulungu udzacotsapo mavuto onsewa.

KUMBANI MOZAMILAPO

Pezani mmene timadziŵila kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914, na zimene tiyenela kucita.

4. Kuŵelengetsela zaka kwa m’Baibo kumaloza ku 1914

Mulungu anapangitsa Mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara, kulota maloto olosela zakutsogolo. Kumasulila kwa malotowo kumene Danieli anafotokoza kuonetsa kuti malotowo anali kulosela za Ulamulilo wa Nebukadinezara, komanso wa Ufumu wa Mulungu.—Ŵelengani Danieli 4:17. a

Ŵelengani Danieli 4:20-26, na kuseŵenzetsa chati pa tsamba lotsatila kuti muyankhe mafunso aya:

  • (A) Kodi Nebukadinezara anaona ciyani m’maloto ake?—Onani mavesi 20 na 21.

  • (B) Kodi n’ciyani cinali kudzacitikila mtengowo?—Onani vesi 23.

  • (C) Nanga n’ciyani cinali kudzacitika kumapeto kwa “nthawi zokwanila 7”?—Onani vesi 26.

Mmene Maloto a Mtengowo Akukhudzila Ufumu wa Mulungu

ULOSI UMENEWO (Danieli 4:20-36)

Ulamulilo

(A) Mtengo waukulu kwambili

Kudukizidwa kwa Ulamulilowo

(B) “Gwetsani mtengowo . . . kufikila patadutsa nthawi zokwanila 7”

Ulamulilowo ubwezeletsedwa

(C) “Inu mudzayambilanso kulamulila mu ufumu wanu”

Pa kukwanilitsidwa koyamba kwa ulosi umenewu . . .

  • (D) Kodi mtengowo unaimilako ndani?—Onani vesi 22.

  • (E) Kodi ulamulilo wake unadukizidwa motani?—Ŵelengani Danieli 4:29-33.

  • (F) Nanga n’ciyani cinacitika kwa Nebukadinezara kumapeto kwa “nthawi zokwanila 7”?—Ŵelengani Danieli 4:34-36.

KUKWANILITSIDWA KOYAMBA

Ulamulilo

(D) Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo

Kudukizidwa kwa Ulamulilowo

(E) Pambuyo pa 606 B.C.E., Nebukadinezara acita misala, ndipo sakutha kulamulila kwa zaka 7

Ulamulilowo ubwezeletsedwa

(F) Nebukadinezara wacila misala yake, ndipo wayambanso kulamulila

Pa kukwanilitsidwa kwaciŵili kwa ulosi uwu . . .

  • (G) Kodi mtengowo unaimilako ndani?—Ŵelengani 1 Mbiri 29:23.

  • (H) Kodi ulamulilo wawo unadukizidwa motani? Nanga timadziŵa bwanji kuti unali wodukizidwabe pamene Yesu anali padziko lapansi? —Ŵelengani Luka 21:24.

  • (I) Kodi ulamulilo umenewu unabwezeletsedwa liti, ndiponso kuti?

KUKWANILITSIDWA KWACIŴILI

Ulamulilo

(G) Mafumu aciisiraeli oimilako ulamulilo wa Mulungu

Kudukizidwa kwa Ulamulilowo

(H) Yerusalemu awonongedwa, ndipo mzele wa mafumu aciisiraeli udukizidwa kwa zaka 2,520

Ulamulilowo ubwezeletsedwa

(I) Yesu ayamba kulamulila kumwamba mu Ufumu wa Mulungu

Kodi nthawi zokwanila 7 ni nyengo yaitali motani?

Malemba ena a m’Baibo amatithandiza kumvetsa bwino malemba enanso. Mwacitsanzo, buku la m’Baibo la Chivumbulutso limafotokoza kuti nthawi zitatu na hafu ni masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Nthawi imeneyi kuiculukitsa kaŵili itipatsa nthawi zokwanila 7, kapena kuti masiku 2,520. Nthawi zina m’Baibo, liwu lakuti tsiku limatanthauza caka. (Ezekieli 4:6) Ni mmenenso zilili na nthawi 7 zochulidwa m’buku la Danieli, zimaimilako zaka 2,520.

5. Dziko linasintha kucokela mu 1914

Yesu ananenelatu zimene zidzacitika padziko lapansi, zoonetsa kuti iye wakhala Mfumu. Ŵelengani Luka 21:9-11, na kukambilana funso ili:

  • Mwa zocitika zimenezi, kodi ni ziti zimene mwaonapo kapena kumvako?

Mtumwi Paulo anafotokoza mmene anthu adzakhalila m’masiku otsiliza a ulamulilo wa anthu. Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5, na kukambilana funso ili:

  • Mwa makhalidwe amenewa, ni ati amene mukuona mwa anthu masiku ano?

6. Kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila kuyenela kutilimbikitsa kucitapo kanthu

Ŵelengani Mateyu 24:3, 14, na kukambilana mafunso aya:

  • Ni nchito iti yofunika imene ikuonetsa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila pali pano?

  • Kodi mungacite ciyani kuti mutengeko mbali pa nchito imeneyi?

Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulila, ndipo posacedwa udzayamba kuyendetsa zinthu zonse padziko lapansi. Ŵelengani Aheberi 10:24, 25, na kukambilana funso ili:

  • Kodi aliyense wa ife ayenela kucita ciyani pamene ‘tikuona kuti tsikulo likuyandikila’?

Ngati mudziŵa zinthu zimene zingathandize anthu ena na kuwapulumutsa, kodi mungacite ciyani?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’cifukwa ciyani a Mboni za Yehova amakamba kuti caka ca 1914 n’capadela?”

  • Kodi inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Maulosi a m’Baibo, kuŵelengetsela zaka, komanso zocitika za m’dziko zionetsa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulila. Timaonetsa kuti timakhulupilila zimenezi pamene tilalikila za Ufumuwo na kupezeka pa misonkhano ya mpingo.

Mafunso Obweleza

  • N’ciyani cinacitika pa mapeto a nthawi zokwanila 7 zoculidwa m’Baibo, m’buku la Danieli?

  • N’ciyani cimakukhutilitsani kuti Ufumu wa Mulungu unayambadi kulamulila mu 1914?

  • Mungaonetse bwanji kuti mumakhulupilila zakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila pali pano?

Colinga

FUFUZANI

Onani zimene olemba mbili yakale komanso ena ananena pa kusintha kwa zocitika m’dziko kuyambila mu 1914.

“Nthawi Imene Makhalidwe Analowa Pansi Kwambili” (Galamuka!, April 2007)

Ŵelengani mmene ulosi wopezeka pa Mateyu 24:14 unakhudzila umoyo wa munthu wina.

“N’nali Kukonda Baseball Kuposa Cina Ciliconse!” (Nsanja ya Mlonda No. 3 2017)

 Kodi tikudziŵa bwanji kuti ulosi wa mu Danieli caputala 4 umanenanso za Ufumu wa Mulungu?

“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila? (Mbali 1)” (Nsanja ya Mlonda, October 1, 2014)

N’ciyani cimaonetsa kuti “nthawi zokwanila 7” zochulidwa mu Danieli caputala 4 zinatha mu 1914?

“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2014)

a Onani  nkhani ziŵili zomaliza pa mbali yakuti Fufuzani m’phunzilo lino.