PHUNZILO 25
Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?
Baibo imavomeleza kuti “anthu amakhala na moyo waufupi komanso wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Kodi ici ndiye cinali cifunilo ca Mulungu kwa ife? Yankho ni lakuti iyayi. Koma kodi colinga cake kwa ife n’ciyani? Kodi colingaco cidzakwanilitsikadi? Onani mayankho olimbikitsa a m’Baibo.
1. Kodi Yehova amatifunila moyo wotani?
Yehova amatifunila moyo wabwino kopambana. Pamene Yehova analenga anthu oyamba, Adamu na Hava, anawaika m’malo okongola a paradaiso, ochedwa Munda wa Edeni. Ndiyeno “Mulungu anawadalitsa ndi kuwauza kuti: ‘mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi ndipo muliyang’anile.’” (Genesis 1:28) Yehova anafuna kuti iwo akhale na ŵana, kuti apange dziko lapansi kukhala paradaiso, komanso kuti azisamalila zinyama. Colinga cake cinali cakuti anthu onse akhale na thanzi langwilo na moyo wamuyaya.
Ngakhale kuti zinthu sizinacitike mwa njila imeneyo, a colinga ca Mulungu sicinasinthe ayi. (Yesaya 46:10, 11) Iye akufunabe kuti anthu omvela akakhale na moyo wangwilo wopanda mavuto alionse.—Ŵelengani Chivumbulutso 21:3, 4.
2. Kodi tingakhale bwanji na moyo waphindu pali pano?
Yehova anatilenga na ‘zosowa zauzimu,’ kutanthauza cikumbumtima cofuna kumulambila. (Ŵelengani Mateyu 5:3-6.) Amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wa thi-thi-thi, kuti ‘tiziyenda m’njila zake zonse, kuti tizim’konda,’ komanso kuti tizim’tumikila na “mtima . . . wonse.” (Deuteronomo 10:12; Salimo 25:14) Tikamacita zimenezi, tidzapeza cimwemwe ceniceni ngakhale timakumana na mavuto. Kulambila Yehova kumatipatsa moyo waphindu wocita cifunilo ca Mulungu.
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani za cikondi cacikulu cimene Yehova anaonetsa potikonzela dziko lapansi, komanso colinga cake cabwino cimene amatiphuzitsa m’Mawu ake.
3. Yehova ali na colinga cabwino kwambili pa anthu
Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
-
Kodi Mulungu anali na colinga cotani polenga dziko lapansi lokongola?
Ŵelengani Mlaliki 3:11, kenako kambilanani funso ili:
-
Kodi zimenezi zikuuzani ciyani za Yehova?
4. Colinga ca Yehova sicinasinthe
Ŵelengani Salimo 37:11, 29, komanso Yesaya 55:11, kenako kambilanani funso ili:
-
Kodi timadziŵa bwanji kuti colinga ca Yehova pa ife sicinasinthe?
5. Kulambila Yehova kumapangitsa moyo wathu kukhala waphindu
Kudziŵa colinga ca moyo kumatipatsa cimwemwe. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
-
Kodi Terumi anapindula motani atadziŵa colinga ca moyo?
Ŵelengani Mlaliki 12:13, na kukambilana funso ili:
-
Poona zambili zimene Yehova waticitila, kodi ifenso tiyenela kucita ciyani poonetsa kuyamikila kwathu?
MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi Mulungu anatilengelanji pamene anali kudziŵa kuti tidzafa?”
-
Inu mungayankhe bwanji?
CIDULE CAKE
Yehova amafuna kuti tikapeze moyo wosatha wopanda mavuto pano padziko lapansi. Ngati timulambila na mtima wathu wonse, umoyo wathu udzakhala waphindu ngakhale pali pano.
Mafunso Obweleza
-
Kodi poyamba, colinga ca Yehova kwa Adamu na Hava cinali ciyani?
-
Kodi timadziŵa bwanji kuti colinga ca Mulungu kwa anthu sicinasinthe?
-
Kodi moyo weniweni waphindu tingaupeze bwanji?
FUFUZANI
Onani umboni woonetsa kuti munda wa Eden unalikodi.
“Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?” (Nsanja ya Mlonda, January 1, 2011)
Dziŵani cifukwa cake tiyenela kutsimikiza kuti dziko lapansi lidzakhalapobe kwamuyaya.
Dziŵani mmene Baibo ingakuthandizileni kupeza moyo waphindu.
Onani mmene munthu amene anali kuganiza kuti zonse anazipeza pa umoyo anazindikilila cimene anali kusoŵeka.
a M’phunzilo lotsatila, mudzamva kuti cinalakwika n’ciyani.