Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 17

Kodi Yesu ni Munthu Wotani?

Kodi Yesu ni Munthu Wotani?

Pamene tiphunzila zimene Yesu anakamba na kucita ali padziko lapansi, timadziŵanso za makhalidwe ake abwino amene amatikokela kwa iye, komanso kwa Atate wake, Yehova. Kodi ena mwa makhalidwe abwino amenewo ni ati? Ndipo tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pa umoyo wathu?

1. Kodi Yesu ni wofanana na Atate ake m’njila ziti?

Kumwambako, Yesu wakhala akuona Atate wake wacikondiyo, na kuphunzila zinthu zoculuka kwa zaka mabiliyoni ambili-mbili. Mwa ici, iye amaganiza, kukhudzidwa mu mtima, komanso kucita zinthu, ndendende monga atate wake. (Ŵelengani Yohane 5:19.) Yesu amaonetsa bwino lomwe makhalidwe a Atate wake. N’cifukwa cake ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Pamene mukuphunzila za makhalidwe a Yesu, Yehovanso mudzafika pom’dziŵa bwino. Mwacitsanzo, poona mmene Yesu anamvela anthu cifundo, mudzadziŵa kuti Yehova amasamala za inu.

2. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti amakonda Yehova?

Yesu anati: “Kuti dziko lidziŵe kuti ndimakonda Atate, ndikucita izi kutsatila lamulo limene Atatewo anandipatsa.” (Yohane 14:31) Ali padziko lapansi, Yesu anaonetsa cikondi cacikulu kwa Atate wake pokhala womvela kwa iye, ngakhale pamene kunali kovuta kutelo. Iye anali kukondanso kukamba za Atate wake, komanso kuthandiza anthu kuti akhale paubwenzi na Atate wake.—Yohane 14:23.

3. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti amakonda anthu?

Baibo imakamba kuti Yesu amawakonda kwambili anthu. (Miyambo 8:31) Cikondi cimeneci anacionetsa polimbikitsa anthu na kuwathandiza mofunitsitsa. Anacita zozizwitsa poonetsa mphamvu zimene ali nazo na cifundo cake. (Maliko 1:40-42) Anthu anali kucita nawo mokoma mtima komanso mosayang’ana nkhope. Kwa anthu omvetsela moona mtima, mawu a Yesu anali opatsa citonthozo na ciyembekezo. Iye anali wokonzeka kuvutika ngakhale kufa kumene, cifukwa cokonda anthu. Koma kwenikweni, amakonda kwambili anthu otsatila zimene iye amaphunzitsa.—Ŵelengani Yohane 15:13, 14.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phunzilani zowonjezela za umunthu wa Yesu. Onaninso mmene mungatengele citsanzo cake pa kuonetsa cikondi na kuwolowa manja.

4. Yesu amawakonda Atate wake

Citsanzo ca Yesu cimatiphunzitsa mmene tingaonetsele cikondi kwa Mulungu. Ŵelengani Luka 6:12 komanso Yohane 15:10, 17:26. Mukaŵelenga iliyonse ya malemba aya, kambilanani funso ili:

  • Potengela citsanzo ca Yesu, tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yehova?

Yesu anali kuwakonda kwambili Atate wake wakumwamba, cakuti anali kupemphela kwa iye kaŵili-kaŵili

5. Yesu amaganizila anthu ofunikila thandizo

Yesu anaika zosoŵa za anthu ena patsogolo pa za iye mwini. Ngakhale pamene anali wotopa, anaseŵenzetsa nthawi komanso nyonga zake kuti athandize anthu. Ŵelengani Maliko 6:30-44, na kukambilana mafunso aya:

  • Pa lemba ili, kodi Yesu anaonetsa m’njila ziti kuti amaganizila ena?—Onani mavesi 31, 3441, komanso 42.

  • N’ciyani cinalimbikitsa Yesu kuthandiza anthu?—Onani vesi 34.

  • Popeza Yesu amaonetsa makhalidwe a Yehova, kodi zitiuzanji za Yehova?

  • Kodi tingatengele motani citsanzo ca Yesu coganizila anthu ena?

6. Yesu ni wowolowa manja

Ngakhale kuti Yesu anali na zinthu zocepa zakuthupi, anali wowolowa manja, ndipo amalimbikitsanso ife kukhala owolowa manja. Ŵelengani Machitidwe 20:35, na kukambilana funso ili:

  • Malinga n’kunena kwa Yesu, kodi n’ciyani cingamatipatse cimwemwe?

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso ili.

  • Ngakhale titakhala tilibe zambili zakuthupi, kodi tingakhalebe wopatsa m’njila zina ziti?

Kodi mudziŵa?

Baibo imatiphunzitsa kuti tizipemphela kwa Yehova m’dzina la Yesu. (Ŵelengani Yohane 16:23, 24.) Tikamapemphela m’njila imeneyi, timaonetsa kuti tikuyamikila zimene Yesu anacita potithandiza kukhala mabwenzi a Yehova.

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mavuto amene amagwela anthu, Mulungu anacita kulembelatu.”

  • Popeza Yesu amaonetsa makhalidwe a Atate wake, kodi zocita zake zimatitsimikizila bwanji kuti mavuto amene timakumana nawo sikuti Yehova ndiye anakonzelatu?

CIDULE CAKE

Yesu amakonda Yehova, ndipo amakondanso anthu. Popeza Yesu ni wofanana na Atate wake, tikafika pomudziŵa bwino Yesu, Yehova naye tidzamudziŵa bwino kwambili.

Mafunso Obweleza

  • Potengela citsanzo ca Yesu, tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yehova?

  • Potengela citsanzo ca Yesu, tingaonetse bwanji kuti timakonda anthu?

  • Ni khalidwe liti la Yesu limene mumalikonda kwambili?

Colinga

FUFUZANI

Kodi Baibo imakambapo ciliconse za mmene Yesu anali kuonekela?

“Kodi Yesu Anali Kuoneka Bwanji?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Mmene Yesu anali kucitila zinthu na akazi, kodi tingaphunzilepo ciyani?

“Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa” (Nsanja ya Mlonda, September 1, 2012)