Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 3

Kodi Muyenela Kuikhulupilila Baibo?

Kodi Muyenela Kuikhulupilila Baibo?

Baibo imatilonjeza zinthu zambili, komanso imatipatsa upangili wabwino, na uphungu wothandiza. N’kutheka kuti mumafuna kudziŵa zimene imaphunzitsa, komanso mumafuna kusamala. Kodi muyeneladi kukhulupilila malonjezo na upangili wopezeka m’buku lakale-kale limeneli? Kodi zimene Baibo imakamba n’zothandizadi masiku ano? Ndipo kodi n’zothekadi kuti tingakhale na umoyo wa cimwemwe masiku ano komanso m’tsogolo? Alipo anthu ambili amene amakhulupililadi zimenezi. Tiyeni tione ngati inunso mungakhulupilile.

1. Kodi Baibo imakamba zoona kapena ni buku la nthano cabe?

Baibo imakamba kuti ili na “mawu olondola a coonadi.” (Mlaliki 12:10) Imasimba zocitika zenizeni zokhudza anthu amene anakhalakodi. (Ŵelengani Luka 1:3; 3:1, 2.) Olemba mbili yakale, komanso akatswili ofukula zinthu zakale, apeza kuti madeti, anthu, malo, komanso zocitika zochulidwa m’Baibo n’zoona.

2. Olo kuti Baibo ni buku lakale-kale, n’cifukwa ciyani siinathe nchito?

Baibo inakambilatu zinthu zambili zosadziŵika panthawiyo. Mwacitsanzo, inakambako nkhani zokhudza sayansi. Ndipo zambili zimene inakambazo anthu sanali kuzikhulupilila panthawiyo. Koma sayansi yamakono yatsimikizila kuti zimene Baibo inakambazo ni zoona. Baibo idzakhalabe yodalilika “mpaka muyaya, ndithu mpaka kalekale.”Salimo 111:8.

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhulupilila zimene Baibo imakamba za kutsogolo?

M’Baibo muli maulosi a okambilatu zinthu zimene zikalibe kucitika. (Yesaya 46:10) Baibo inakambilatu zocitika zambili kukali nthawi yaitali, ndipo zinthuzo zinakwanilitsidwa ndendende. Inakambilatunso momveka bwino zimene zikucitika padziko lapansi masiku athu ano. M’phunzilo lino, tidzakambilana ena mwa maulosi a m’Baibo. Ndipo kulondola kwake, n’kocititsa cidwi kwambili!

KUMBANI MOZAMILAPO

Yesani kupeza mbali zimene sayansi yamakono imavomelezana na Baibo, komanso pezankoni maulosi a m’Baibo angapo ocititsa cidwi.

4. Sayansi imavomelezana na Baibo

M’nthawi zamakedzana, anthu ambili anali kukhulupilila kuti dziko lapansi linakhazikitsidwa pa cinthu cina cake. Tambani VIDIYO.

Onani zimene zinalembedwa m’buku la Yobu zaka ngati 3,500 zapitazo. Ŵelengani Yobu 26:7, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani mfundo yakuti dziko lapansi n’lolenjeka “m’malele” ni yocititsa cidwi?

M’zaka za m’ma 1800 m’pamene anthu anamvetsa zungulile-zungulile wa madzi. Koma onani zimene Baibo inakamba zaka masauzande kale-kalelo. Ŵelengani Yobu 36:27, 28, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani mafotokozedwe amenewa a zungulile-zungulile wa madzi ni ocititsa cidwi?

  • Kodi malemba amene mwaŵelenga amalimbitsa bwanji cikhulupililo canu pa Baibo?

5. Baibo inakambilatu zocitika zapadela

Ŵelengani Yesaya 44:27–45:2, na kukambilana funso ili:

  • Zaka 200 pasadakhale, kodi Baibo inakambilatu ciyani za kugwa kwa Babulo?

Mbili yakale imaikila umboni wakuti Mfumu Koresi ya Perisiya, pamodzi na asilikali ake, anagonjetsa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E. b Iwo anapatutsa mtsinje umene unali citetezo ca mzindawo. Ataloŵa mu mzindawo, zipata zili citsegukile, anaugonjetsa popanda kumenya nkhondo. Kufika pano, papita zaka 2,500, ndipo Babulo akali matongwe okha-okha. Onani zimene Baibo inakambilatu.

Ŵelengani Yesaya 13:19, 20, na kukambilana funso ili:

  • Kodi zimene zinacitikila Babulo zinakwanilitsa bwanji ulosi umenewu?

Matongwe a Babulo masiku ano ku Iraq

6. Baibo inakambilatu zinthu zimene timaona masiku ano

Baibo imati tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’ (2 Timoteyo 3:1) Onani zimene Baibo inakambilatu za masiku otsiliza:

Ŵelengani Mateyu 24:6, 7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi n’zocitika zapadela ziti zimene Baibo inakambilatu kuti zidzacitika m’masiku otsiliza?

Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Baibo inati m’masiku otsiliza anthu adzakhala na makhalidwe abwanji?

  • Kodi ni makhalidwe ati amene mwadzionela mwekha?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Baibo ni buku la nthano na zikhulupililo za anthu cabe.”

  • Kodi n’ciyani cimakukhutilitsani kuti Baibo imakamba zoona?

CIDULE CAKE

Mbili yakale, sayansi, komanso maulosi, zonsezi zimatsimikizila kuti Baibo ni buku lodalilika.

Mafunso Obweleza

  • Kodi nkhani za m’Baibo ni zoona kapena n’zongopeka?

  • Nanga ni nkhani ziti zimene sayansi imavomelezana na Baibo?

  • Kodi zimene Baibo imakambilatu za kutsogolo n’zoona? Inde kapena ayi, fotokozani.

Colinga

FUFUZANI

Kodi Baibo imakamba zolakwika pa nkhani za sayansi?

“Kodi Sayansi Imagwilizana na Baibo?” (Nkhani ya pa webusaiti)

Kodi zoona zake n’zotani pa nkhani ya “masiku otsiliza”?

“Maulosi 6 a m’Baibo Amene Akukwanilitsidwa Masiku Ano” (Nsanja ya Mlonda, May 1, 2011)

Phunzilani mmene maulosi a m’Baibo onena za Ufumu wa Girisi anakwanilitsidwila.

‘Mau Aulosi’ Amatilimbikitsa (5:22)

Onani mmene maulosi a m’Baibo anasinthila maganizo a munthu wina pa Baibo.

“N’nali Kukhulupilila Kuti Kulibe Mulungu” (Nsanja ya Mlonda Na. 5, 2017)

a Maulosi ni mauthenga ocokela kwa Mulungu amene amakamba za kutsogolo.

b B.C.E. itanthauza “Yesu asanabwele,” ndipo C.E. itanthauza “Yesu atabwela.”