PHUNZILO 14
Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?
Kwa zaka zambili, maphunzilo aumulungu akhala mbali yofunika kwambili kwa Mboni za Yehova. Anthu amene amadzipeleka kuti azilalikila za Ufumu nthawi zonse, amalandila maphunzilo apadela kuti ‘akwanilitse mbali zonse za utumiki wawo.’—2 Timoteyo 4:5.
Sukulu ya Apainiya. Mpainiya wa nthawi zonse akakwanitsa caka cimodzi mu utumiki wake, amaloŵa sukulu ya masiku 6 imene ingacitikile pa Nyumba ya Ufumu ya kufupi ndi kwawo. Colinga ca sukulu imeneyi ni kuthandiza apainiya kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova, kunola maluso awo m’mbali zonse za utumiki, komanso kuti apitilize kutumikila mokhulupilika.
Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Sukulu imeneyi ya miyezi iŵili, anakonzela apainiya aciyambakale amene ni okonzeka kucoka kwawo ndi kukatumikila kumene alaliki ni ocepa. Amakhala ngati akukamba kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” Amacita izi potengela citsanzo ca Mlaliki wopambana onse amene anakhalapo padziko lapansi, Yesu Khristu. (Yesaya 6:8; Yohane 7:29) Kusamukila kumalo akutali kungafune kuti munthu ajaile kukhala na umoyo wosalila zambili. Cikhalidwe, nyengo, ndi cakudya zikhoza kukhala zosiyana kwambili na zimene anazoloŵela kwawo. Angafunikenso kuphunzila citundu catsopano. Sukulu imeneyi imathandiza abale ndi alongo amene sali pabanja, ndi amene ali pabanja, a zaka zoyambila 23 mpaka 65, kukulitsa makhalidwe auzimu ofunikila pa utumiki wawo. Imawathandizanso kuphunzila maluso amene adzacititsa kuti Yehova na gulu lake liwagwilitsile nchito kwambili.
Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo. M’ciheberi, liu lakuti “Giliyadi” limatanthauza “Mulu wa Umboni.” Kucokela pamene sukulu ya Giliyadi inayamba mu 1943, anthu otsiliza maphunzilo opitilila 8,000 atumizidwa monga amishonali kuti akacitile umboni “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi,” ndipo pakhala zotulukapo zabwino. (Machitidwe 13:47) Mwacitsanzo, pamene otsiliza maphunzilo a Giliyadi anafika m’dziko la Peru koyamba, m’dzikomo munalibe mpingo olo umodzi. Koma lomba muli mipingo yopitilila 1,000. Amishonali athu atayamba kutumukila m’dziko la Japan, munali Mboni zosakwana 10. Koma lomba kuli Mboni zopitilila 200,000. Ku Sukulu ya Giliyadi imeneyi ya miyezi isanu, amaphunzila Mau a Mulungu mozamilapo. Aja amene akumikila monga apainiya apadela, amishonali, m’maofesi a nthambi, kapena oyang’anila madela, amaitanidwa kuti akaloŵe sukuluyi. Amalandila maphunzilo akuya kuti alimbikitse na kupititsa patsogolo nchito ya padziko lonse.
-
Kodi colinga ca Sukulu ya Apainiya n’ciani?
-
Kodi Sukulu ya Alengezi a Ufumu anakonzela ndani?