PHUNZILO 3
Coonadi ca m’Baibo Cipezekanso!
Baibo inakambilatu kuti pambuyo pa imfa ya Kristu, padzakhala aphunzitsi abodza pakati pa Akristu oyambilila ndipo adzapotoza coonadi ca m’Baibo. (Machitidwe 20:29, 30) Patapita nthawi, zimenezi zinacitikadi. Iwo anasakaniza ziphunzitso za Yesu ndi ziphunzitso zacikunja, ndipo Cikristu cabodza cinayamba. (2 Timoteyo 4:3, 4) Nanga tingadziŵe bwanji kuti zimene timakhulupilila masiku ano ndi zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni?
Nthawi inafika yakuti Yehova avumbule coonadi. Iye anakambilatu kuti m’nthawi ya mapeto, cidziŵitso coona cidzaculuka. (Danieli 12:4) Mu 1870, kagulu ka anthu ofuna coonadi kanazindikila kuti ziphunzitso za machalichi ambili sizinali za m’Malemba. Conco, io anayamba kufuna-funa coonadi ca m’Baibo kuti apeze ziphunzitso zake zeni-zeni, ndipo Yehova anawadalitsa ndi cidziŵitso pa zinthu zauzimu.
Amuna odzipeleka anaphunzila Baibo mosamala. Ophunzila Baibo akhama amenewo, amene analipo ife tisanabadwe, anapeza njila yophunzilila Baibo imene timagwilitsila nchito mpaka lelo. Iwo anali kutenga nkhani imodzi-imodzi m’Baibo ndi kukambitsilana. Akapeza lemba lovuta kumva, anali kuona malemba ena ofotokoza lemba limenelo. Akapeza mfundo imene igwilizana ndi Malemba onse, anali kuilemba. Mwa kulola Baibo kuti ifotokoze yokha, io anapeza coonadi cokhudza dzina la Mulungu ndi Ufumu wake, colinga cake pa anthu ndi dziko lapansi, mkhalidwe wa akufa, ndi ciyembekezo ca ciukililo. Zimene anapeza zinawamasula ku zikhulupililo ndi miyambo yambili yabodza.—Yohane 8:31, 32.
Pofika mu 1879, Ophunzila Baibo anazindikila kuti inali nthawi yakuti afalitse coonadi. Conco, caka cimeneco anayamba kufalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova, imene timafalitsa mpaka lelo. Masiku ano, timauza anthu coonadi ca m’Baibo m’maiko 240 ndi m’zinenelo zopitilila 750. Kuyambila kale, sizinacitikepo kukhala ndi cidziŵitso coona coculuka conco!
-
Pambuyo pa imfa ya Kristu, n’ciani cinacitika ndi coonadi ca m’Baibo?
-
Kodi n’ciani catithandiza kupezanso coonadi ca m’Mau a Mulungu?