GAWO 6
Mmene Ana Amasinthila Banja
“Ana ndi colowa cocokela kwa Yehova.”—Salimo 127:3
Kubadwa kwa mwana kungakhale kokondweletsa komanso kolemetsa kwa anthu okwatilana. Monga makolo atsopano, mungadabwe kuti mukuthela nthawi yaitali ndiponso mphamvu zanu pa kusamalila mwana wanu wakhanda. Kusagona mokwanila ndi kusintha kwa maganizo kungapangitse kuti cikwati canu cisaziyenda bwino. Inu nonse aŵili mudzafunika kusintha zinthu zina kuti musamalile mwana wanu ndiponso kusunga cikwati canu. Kodi uphungu wa m’Baibulo ungakuthandizeni bwanji kulimbana ndi mavuto amenewa?
1 M’POFUNIKA KUMVETSA MMENE MWANA AMASINTHILA UMOYO WANU
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Komanso cikondi “sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya.” (1 Akorinto 13:4, 5) Popeza kuti tsopano mwakhala ndi mwana, mwacibadwa mumaika maganizo anu pa kusamalila mwana wanu. Komabe, mwamuna wanu angayambe kuona kuti simukumusamala, conco musaiŵale kuti nayenso akufunika cisamalilo canu. Moleza mtima ndiponso mokoma mtima, mungamuthandize kuona kuti mumamuganizila ndi kuti iyenso ayenela kuthandizako posamalila mwana wanuyo.
“Inunso amuna pitilizani kukhala ndi akazi anu mowadziŵa bwino.” (1 Petulo 3:7) Mufunika kumvetsa kuti tsopano mkazi wanu adzayamba kuthela mphamvu zake zambili kusamalila mwana wanu. Iye tsopano wakhala ndi maudindo ena amene mwina angamucititse kukhala ndi nkhawa, kukhala wolema komanso kukhala wosakondwela. Nthawi zina akhoza kumakukwiyilani, koma yesetsani kuugwila mtima cifukwa “munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.” (Miyambo 16:32) Khalani wozindikila ndipo muthandizeni pa zimene akufunikila.—Miyambo 14:29.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Atate: Thandizani mkazi wanu kusamalila mwana ngakhale usiku. Mucepetseko nthawi imene mumathela pocita zinthu zina n’colinga cakuti mupeze nthawi yambili yokhala ndi mkazi wanu ndiponso mwana wanu
-
Amai: Mwamuna wanu akafuna kukuthandizani kusamalila mwana musazikana. Ngati sacita bwino nchito imeneyi, muyamikileni ndipo mokoma mtima muonetseni mmene mumacitila
2 LIMBITSANI CIKWATI CANU
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Ngakhale kuti m’banja lanu mwabwela wina watsopano, kumbukilani kuti inu ndi mnzanu wa m’cikwati mukali “thupi limodzi.” Yesetsani kulimbitsa cikwati canu.
Akazi, muziyamikila thandizo limene mwamuna wanu amapeleka. Mau anu oyamikila angakhale ‘ocilitsa.’ (Miyambo 12:18) Amuna, muuzeni mkazi wanu kuti ndi wofunika kwambili ndipo mumamukonda. Muyamikileni cifukwa ca mmene amasamalila banja.—Miyambo 31:10, 28.
“Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Nthawi zonse muzimucitila zabwino mnzanu wa m’cikwati. Monga okwatilana, khalani ndi nthawi yokambitsilana, kumvetselana ndi kuyamikilana. Ikafika nthawi ya kugonana musamanane. Ganizilani zofuna za mnzanu wa m’cikwati. Baibulo limati: “Musamanane kupatulapo ngati mwagwilizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziŵika.” (1 Akorinto 7:3-5) Conco muli aŵili muyenela kukambilana nkhaniyi moona mtima. Kumvetsetsa kwanu ndi kuleza mtima kudzalimbitsa cikwati canu.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Musaiŵale kupeza nthawi yoceza ndi mnzanu wa m’cikwati
-
Muzicita tunthu tung’onotung’ono tumene tungapangitse mnzanu wa m’cikwati kumva kuti akukondedwa. Mukhoza kumubweletsela kamphatso kakang’ono kapena kumutumilako kamesegi.
3 KUPHUNZITSA MWANA WANU
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke.” (2 Timoteyo 3:15) Onani zimene mungacite kuti muphunzitse mwana wanu. Mwana akhoza kuphunzila zambili, ngakhale asanabadwe. Mwana wanu akali m’mimba, amadziŵa mau anu ndipo angakhudzidwe ndi mmene inuyo mukumvela. Akali wakhanda muzimuŵelengela. Ngakhale kuti sangamvetse zimene mukuŵelengazo, akadzakula zidzamuthandiza kuti adzakonde kuŵelenga.
Ngakhale ndi wamng’ono kwambili, mwana wanu angakumvetseleni mukamakamba za Mulungu. Muloleni kuti azikumvetselani mukamapemphela kwa Yehova. (Deuteronomo 11:19) Pamene museŵela naye muzikamba za zinthu zimene Mulungu anapanga. (Salimo 78:3, 4) Pamene mwana wanu akula, adzazindikila kuti mumakonda Yehova ndipo iyenso adzaphunzila kukonda Yehova.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Pemphani nzelu kwa Mulungu zakuti muphunzitse bwino mwana wanu
-
Kuti mwana wanu aphunzile zinthu mwamsanga, muzibweleza mau amene ali ndi mfundo zikuluzikulu