FUNSO 15
Mungacipeze bwanji cimwemwe?
“Ndi bwino kudya zamasamba koma pali cikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali cidani.”
Miyambo 15:17
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.”
Yesaya 48:17
“Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu, cifukwa ufumu wakumwamba ndi wao.”
“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”
“Zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inuyo muwacitile zomwezo.”
“Odala ndi amene akumva mau a Mulungu ndi kuwasunga!”
“Munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.”
“Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.”
1 Timoteyo 6:8
“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”
Machitidwe 20:35