Gao 8
Zimene Baibo Imakamba Zimacitika
Baibo imakamba nkhani zeni-zeni zimene zinacitika kale, ndiponso imatiuza zinthu zimene zidzacitika mtsogolo. Anthu sangakambe za mtsogolo. Pacifukwa cimeneci, timadziŵa kuti Baibo inacokela kwa Mulungu. Kodi Baibo imakamba ciani za mtsogolo?
Imatiuza za nkhondo yaikulu ya Mulungu. Pankhondo imeneyi Mulungu adzayeletsa dziko lapansi mwa kucotsapo zoipa zonse ndi anthu oipa, koma adzachinjiliza anthu amene amamutumikila. Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, idzaonetsetsa kuti atumiki a Mulungu ali pamtendele ndipo ali acimwemwe, ndiponso sadzadwalanso kapena kufa.
Tiyenela kuyamikila kuti Mulungu adzasandutsa dziko lapansi kukhala paladaiso, si conco? Koma tiyenela kucitapo kanthu kuti tikakhalemo mu paladaiso. Mu nkhani yotsilizila ya buku lino tidzaphunzila zimene tiyenela kucita kuti tikapeze zinthu zabwino zimene Mulungu adzacitila anthu amene amamutumikila. Conco uyenela kuŵelenga GAO 8 kuti udziŵe zimene Baibo imakamba za mtsogolo.