Nkhani 73
Mfumu Yabwino Yotsilizila Ya Isiraeli
YOSIYA ali ndi zaka 8 cabe pamene akhala mfumu ya mafuko aŵili a kum’mwela a Isiraeli. Zaka zimenezi n’zocepa kwambili kuti munthu akhale mfumu. Conco, paciyambi anthu acikulile amuthandiza kulamulila.
Pamene Yosiya alamulila kwa zaka 7, ayamba kufuna-funa Yehova. Atsatila citsanzo ca mafumu abwino monga Davide, Yehosafati ndi Hezekiya. Ndiyeno pamene akali cabe mnyamata, acita cinthu cimene cionetsa kuti ni wolimba mtima.
Kwanthawi itali, Aisiraeli ambili anali anthu oipa kwambili. Anali kulambila milungu yonama ndi kugwadila mafano. Conco Yosiya pamodzi ndi anchito ake ayamba kucotsa kulambila konama mu dzikolo. Nchito imeneyi ni yaikulu kwambili cifukwa anthu amene alambila milungu yonama ni ambili. Kodi wamuona pacithunzi-thunzi apa Yosiya ndi anchito ake pamene aphwanya mafano?
Pambuyo pake, Yosiya aika amuna atatu kuti aziyang’anila nchito yokonza kacisi wa Yehova. Anthu asonkha ndalama ndipo zipatsidwa kwa amuna amenewa kuti aziseŵenzetse pa nchito imeneyi. Pamene aseŵenza, mkulu wa ansembe Hilikiya apeza cinthu cofunika kwambili pa kacisi. Limeneli ni buku la cilamulo limene Yehova anauza Mose kulemba kale-kale kwambili. Linali linasoŵa kwa zaka zambili.
Buku limeneli lipelekedwa kwa Yosiya, ndipo apempha kuti liŵelengedwe kwa iye. Pamene amvetsela kuŵelengedwa kwa bukuli, Yosiya aona kuti anthu sanali kutsatila cilamulo ca Yehova. Iye akumva cisoni kwambili cifukwa ca zimenezi, conco ang’amba malaya ake, monga mmene uonela pacinthunzi-thunzi apa. Ndiyeno akamba kuti: ‘Yehova watikwiila cifukwa makolo athu sanatsatile malamulo olembedwa m’bukuli.’
Yosiya alamula mkulu wa ansembe Hilikiya kuti akafunse cimene Yehova adzacita kwa io. Hilikiya apita kwa Hulida mneneli wacikazi kuti akafunse. Mneneliyu amuuza uthenga wocokela kwa Yehova wakuti akauze Yosiya. Iye akuti: ‘Mzinda wa Yerusalemu ndi anthu ake onse adzalangidwa cifukwa analambila milungu yonama, ndipo dziko ladzala ndi zoipa. Koma cifukwa cakuti iwe Yosiya ucita zoyenela, sinidzapeleka cilango ici mpaka pambuyo pakuti iwe wamwalila.’
2 Mbiri 34:1-28.