Nkhani 86
Nyenyezi Itsogolela Amuna A Kum’mawa
KODI waiona nyenyezi yowala kwambili imene mwamuna uyu asontha? Nyenyezi imeneyi inaoneka pamene amuna amenewa ananyamuka kucoka ku Yerusalemu. Amuna amenewa ni a kum’mawa ndipo amakhulupilila za nyenyezi. Akhulupilila kuti nyenyezi yatsopano imeneyi iwatsogolela kwa munthu wina wofunika kwambili.
Pamene amuna amenewa anafika ku Yerusalemu, anafunsa kuti: ‘Kodi mwana amene adzakhala mfumu ya Ayuda ali kuti? “Ayuda” ni dzina lina la Aisiraeli. Ndipo amuna amenewo anati: ‘Tinaona nyenyezi yake coyamba pamene tinali kum’mawa, ndipo tabwela kuti timulambile.’
Pamene Herode, mfumu ya ku Yerusalemu, anamva zimenezi anakalipa kwambili. Iye sanali kufuna mfumu ina kutenga malo ake. Conco Herode anaitana ansembe akulu ndipo anawafunsa kuti: ‘Kodi mfumu yolonjezedwa idzabadwila kuti?’ Iwo anayankha kuti: ‘Baibo imati ku Betelehemu.’
Conco Herode anaitana amuna a kum’mawa, ndipo anati: ‘Pitani mukamufune-fune mwanayo mosamala, ndipo ngati mwamupeza mudzandidziŵitse, kuti inenso n’kamugwadile.’ Koma M’ceni-ceni, Herode anali kufuna kupeza mwana ameneyu kuti amuphe!
Ndiyeno nyenyezi ipitilila amuna amenewo ndi kupita ku Betelehemu, ndipo iima pamalo amene mwana ameneyu ali. Pamene amuna amenewa aloŵa m’nyumba, apeza Mariya ali ndi mwana wake, Yesu. Iwo atulutsa mphatso ndi kupatsa Yesu. Koma panthawi ina Yehova acenjeza amuna amenewa kumaloto kuti asabwelele kwa Herode. Conco apitila njila ina pobwelela ku dziko la kwao.
Pamene Herode anamva kuti amuna a kum’mawa anapitilila pobwelela kwao, anakalipa kwambili. Conco apeleka lamulo lakuti ana onse amuna mu Betelehemu azaka ziŵili kubwela pansi aphedwe. Koma Yehova acenjezelatu Yosefe kumaloto, ndipo Yosefe acoka ku Iguputo ndi banja lake. M’kupita kwa nthawi, pamene Yosefe amvela kuti Herode anamwalila, anatenga Mariya ndi Yesu ndi kubwelela ku Nazareti. Uku n’kumene Yesu anakulila.
Kodi uganiza kuti ndani anacititsa nyenyezi yatsopano kuwala? Kumbukila kuti pamene amuna anaona nyenyezi, coyamba anapita ku Yerusalemu. Satana Mdyelekezi anafuna kupha Mwana wa Mulungu, ndipo anadziŵa kuti Mfumu Herode ya ku Yerusalemu idzafuna kumupha. Conco Satana ayenela kuti ni amene anacititsa nyenyezi ija kuwala.
Mateyu 2:1-23; Mika 5:2.