Gao 1
Kucokela pa Cilengedwe Kufika pa Cigumula
Kodi ndani amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi? Nanga dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zina zambili zili padziko lapansi zinakhalako bwanji? Baibo imatiuza yankho la zoona kuti amene anazilenga ni Mulungu. Conco buku lathu lino liyamba ndi nkhani za mu Baibo zokamba zacilengedwe.
Timaphunzila kuti, poyambilila Mulungu analenga anthu amzimu monga iye. Anthu amenewo ni angelo. Koma Mulungu analenga dziko lapansi kuti pakhale anthu monga ife. Conco, Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi ndi kuwacha kuti Adamu ndi Hava. Ndiyeno anawaika mu munda wokongola. Koma cifukwa cakuti sanamvele Mulungu, anataya mwai wokhala ndi moyo wamuyaya.
Kucokela pa cilengedwe kukafika pa Cigumula cacikulu, panapita zaka 1,656. Mkati mwa nthawi imeneyi, padziko lapansi panakhalako anthu oipa ambili. Kumwamba kunali anthu amzimu osaoneka, Satana ndi angelo ake oipa. Koma padziko lapansi panakhalako Kaini ndi anthu ena oipa, kuphatikizapo viŵanthu vina vamphamvu kwambili. Komanso panakhalako anthu ena abwino, monga Abele, Inoki ndi Nowa. Mu Gao 1 la buku lino tidzaŵelenga za anthu onse amenewa ndi zocitika za mu nthawi yao.