Nkhani 29
Cimene Mose Anathaŵila
YANG’ANA pacithunzi-thunzi apa. Wamuona Mose athaŵa kucoka ku Iguputo. Kodi waŵaona amuna amene amuthamangitsa? Kodi udziŵa cifukwa cake afuna kumupha? Tiye tione ngati tingapeze cifukwa cimene acitila zimenezi.
Mose anakulila mu nyumba ya Farao, mfumu ya ku Iguputo. Iye anakhala munthu wanzelu ndi wolemekezeka kwambili. Anali kudziŵa kuti sanali Mwiguputo, koma kuti makolo ake eni-eni anali akapolo aciisiraeli.
Tsiku lina, pamene Mose anali ndi zaka 40, anaganiza zopita kukaona mmene umoyo wa anthu akwao unalili. Anali kuwacitila nkhanza kwambili. Mose anaona Mwiguputo akumenya kapolo waciisiraeli. Pamene anayang’ana uku ndi uku, n’kuona kuti kunalibe amene anali kumuona, anamenya Mwiguputo uja, ndipo anafelatu. Ndiyeno Mose anafocela thupi la munthu uja mumcenga.
Tsiku lotsatila Mose anapitanso kukaona anthu akwao. Iye anaganiza kuti angawathandize kuleka kukhala akapolo. Pamenepo anaona amuna aŵili aciisiraeli akumenyana. Ndiyeno Mose anauza amene anali wolakwa kuti: ‘N’cifukwa ciani umenya m’bale wako?
Iye poyankha anati: ‘Anakuika iwe kukhala kalonga ndi woweluza wathu ndani? Kodi ufuna kundipha mmene unaphela Mwiguputo uja?’
Pamenepo Mose anacita mantha. Anaona kuti anthu adziŵa zimene anacita kwa Mwiguputo uja. Ngakhale Farao anamva zimenezi, ndipo anatuma amuna kuti akamuphe Mose. Ndiye cifukwa cake Mose anathaŵa kucoka ku Iguputo.
Pamene Mose anacoka ku Iguputo, anayenda kudziko la kutali la Midiyani. Ali kumeneko, anakumana ndi banja la Yetero, ndipo anakwatila mmodzi wa ana ake akazi, dzina lake Zipora. Mose anakhala mbusa ndipo anali kulisha nkhosa za Yetero. Anakhala mu dziko la Midiyani kwa zaka 40. Tsopano Mose anali ndi zaka 80. Ndiyeno tsiku lina, pamene anali kulisha nkhosa za Yetero, cinthu codabwitsa cinacitika cimene cinasintha umoyo wake wonse. Tsegula peji yotsatila, tione kuti cinthu codabwitsa cimeneco cinali ciani.
Ekisodo 2:11-25; Machitidwe 7:22-29.