Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 102

Yesu Ali Moyo

Yesu Ali Moyo

KODI wamudziŵa mkazi uyu ndi amuna aŵili amene ali pacithunzi-thunzi apa? Mkaziyu ni Mariya Mmagadala, mnzake wa Yesu. Ndipo amuna amene avala zoyela ni angelo. Ndipo kacipinda aka mmene Mariya ayang’ana ni mmene thupi la Yesu linaikidwa pamene anamwalila. Kacipinda kameneka ni manda. Koma tsopano mtembo mulibe! Kodi ndani amene wautengamo? Tiye tione.

Pamene Yesu amwalila, ansembe auza Pilato kuti: ‘Pamene Yesu anali moyo anakamba kuti adzaukitsidwa pakapita masiku atatu. Conco uzani asilikali kuti azilonda pamanda. Pamenepo ophunzila ake sadzaba thupi lake ndi kunama kuti wauka!’ Pilato auza ansembe kutumiza asilikali kuti azilonda pamanda.

Koma m’mawa kwambili patsiku lacitatu kucokela pamene Yesu anamwalila, mngelo wa Yehova aonekela mwadzidzidzi. Iye acotsa cimwala pamanda. Asilikali acita mantha kwambili cakuti angoima osacita ciliconse. Koma pamene io ayang’ana m’manda, apeza kuti mtembo mulibe! Ndiyeno asilikali ena apita mumzinda ndi kukauza ansembe zimene zacitika. Koma kodi udziŵa zimene ansembe oipa amenewa acita? Apatsa asilikali ndalama kuti akambe zabodza. Ansembe auza asilikali kuti: ‘Muzikamba kuti ophunzila ake abwela usiku ndi kuba thupi lake pamene ife tinali gone.’

Panthawi imeneyi, akazi amene anali anzake a Yesu abwela ku manda. Iwo adabwa kwambili kupeza kuti m’manda mulibe ciliconse! Mwadzidzidzi angelo aŵili amene avala zovala zonyezimila aonekela. Iwo afunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani mufuna Yesu kuno? Iye wauka. Yendani mwamsanga ndipo mukauze ophunzila ake.’ Akazi amenewo athamanga mwamsanga! Koma pamene ali m’njila mwamuna wina awaimitsa. Kodi wamudziŵa mwamuna amene awaimitsa? Ameneyu ni Yesu! Iye akuti, ‘Yendani mukauze ophunzila anga.’

Pamene akazi auza ophunzila kuti Yesu ali moyo ndipo amuona, ophunzilawo ziŵavuta kukhulupilila. Petulo ndi Yohane athamangila kumanda kuti akadzionele okha, koma apeza kuti m’manda mulibe thupi la Yesu! Pamene Petulo ndi Yohane acoka, Mariya Mmagadala atsala kumeneko. Ndiyeno pamene ayang’ana mkati, aonamo angelo aŵili.

Kodi udziŵa cimene cinacitikila thupi la Yesu? Mulungu anacititsa kuti lisaoneke. Sanaukitse Yesu ndi thupi limene anali nalo pamene anafa. Iye anapatsa Yesu thupi lauzimu latsopano, monga matupi amene angelo kumwamba ali nao. Koma kuti aonetse ophunzila ake kuti ali moyo, Yesu akhala ndi thupi limene anthu angaone, monga mmene tidzaphunzilila.