Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 103

Aloŵa M’cipinda Cokhoma

Aloŵa M’cipinda Cokhoma

PAMENE Petulo ndi Yohane acoka kumanda kumene kunali thupi la Yesu, Mariya atsala yekha kumeneko. Iye ayamba kulila. Ndiyeno aŵelama ndi kuyang’ana m’manda monga taonela pacithunzi-thunzi capita. Mmenemo aonamo angelo aŵili! Iwo amufunsa kuti: ‘Ulila ciani?’

Mariya ayankha kuti: ‘Atenga Mbuye wanga, ndipo sinidziŵa kumene amuika.’ Mariya aceuka ndipo aona munthu. Ndiyeno munthuyo amufunsa kuti: ‘Kodi ufuna ndani?’

Mariya aganiza kuti munthuyo ni wosamalila munda, ndi kuti mwina ndiye watenga thupi la Yesu. Conco akuti kwa iye: ‘Ngati mwamucotsa ndinu, ndiuzeni conde kumene mwamuika.’ Munthu ameneyu kweni-kweni ni Yesu. Avala thupi limene Mariya sanalidziŵe. Koma pamene munthuyo amuchula dzina, Mariya adziŵa kuti ni Yesu. Iye athamanga ndi kukauza ophunzila kuti: ‘Ndawaona Ambuye!’

Nthawi ina patsiku limenelo, pamene ophunzila aŵili ali paulendo wopita ku mudzi wa Emau, munthu wina afika ndi kuyamba kuyenda nao pamodzi. Ophunzila ali ndi cisoni kwambili cifukwa Yesu waphedwa. Koma pamene apitiliza ulendowo pamodzi, munthuyo afotokoza zinthu zambili zocokela m’Baibo zimene ziwatonthoza mtima. Ndiyeno, pamene aima kuti adye cakudya, ophunzilawo azindikila kuti munthuyo ni Yesu. Pamenepo Yesu asoŵa, ndipo ophunzila aŵiliwa mwamsanga abwelela ku Yerusalemu kuti akauze atumwi za iye.

Pamene zimenezi zicitika, Yesu aonekelanso kwa Petulo. Ophunzila ena akondwela kwambili pamene amvela zimenezo. Ndiyeno ophunzila aŵili aja ayenda ku Yerusalemu ndipo apeza atumwi. Iwo afotokoza mmene Yesu anaonekelanso kwa io pamene anali paulendo. Koma pamene afotokoza zimenezi, udziŵa cokondweletsa cimene cicitika?

Yang’ana pacithunzi-thunzi apa. Yesu aonekela m’cipinda cimene io alimo ngakhale kuti citseko ni cokhoma. Ophunzila akondwela kwambili! Ndithudi limeneli ndi tsiku lacisangalalo! Kodi ungaŵelenge nthawi zimene Yesu waonekela kwa otsatila ake? Kodi waŵelenga nthawi zisanu?

Pamene Yesu aonekela kwa io, mtumwi Tomasi sanali nao. Conco ophunzila amuuza kuti: ‘Tawaona Ambuye!’ Koma Tomasi akamba kuti sadzakhulupilila mpaka amuone yakha. Ndiyeno patapita masiku 8, ophunzila asonkhananso pamodzi m’cipinda cokhoma, ndipo panthawiyi Tomasi ali nao pamodzi. Mwadzidzidzi, Yesu aonekela kwa io m’cipindamo. Tomasi tsopano akhulupilila.