Nkhani 40
Mose Amenya Cimwala Ndi Ndodo
ZAKA zakhala zikupita—zaka 10, zaka 20, zaka 30, mpaka zaka 39! Koma Aisiraeli akali mu cipululu. Ndipo pazaka zonse izi Yehova asamalila anthu ake. Wakhala akuwadyetsa mana. Usana awatsogolela ndi mtambo wooneka monga cipilala, ndipo usiku awatsogolela ndi moto wooneka monga cipilala. Pazaka zonse izi zovala zao sizisila ndipo mapazi ao sacita vilonda.
Apa ndi mwezi woyamba wa caka ca 40 kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo. Iwo amanganso misasa yao ku Kadesi. Malo amenewa m’pamene Aisiraeli anali zaka 40 zapitazo, pamene anatuma azondi 12 kuti akaone dziko la Kanani. Mlongosi wa Mose, Miriamu, afela pamalo amenewa pa Kadesi. Ndipo monga poyamba paja, mavuto ayambanso.
Anthu alibiletu madzi. Conco ayamba kukangana ndi Mose kuti: ‘Cikanakhala bwino tikanafa. Munaticotselanji m’dziko la Iguputo kutibweletsa kumalo kumene sikumela ciliconse? Kulibe mbeu, nkhuyu, mpesa; kulibenso mitengo ya makangaza. Ngakhale madzi akumwa kulibe.’
Pamene Mose ndi Aroni apita kukapemphela kucihema, Yehova auza Mose kuti: ‘Sonkhanitsa anthu. Uuze cimwala pamaso pao kuti citulutse madzi. Mudzatuluka madzi okwanila kuti anthu onse ndi nyama amwe.’
Conco, Mose asonkhanitsa anthu, ndipo awauza kuti: ‘Mvelani anthu opanda cikhulupililo inu! Kodi Aroni ndi ine ticite kukutulutsilani madzi mu cimwala?’ Pamenepo Mose amenya cimwala kaŵili ndi ndodo, basi madzi ambili ayamba kucoka mu cimwala cija. Ndipo anthu ndi nyama akhala ndi madzi ambili akumwa.
Koma Yehova wakalipa kwambili cifukwa ca Mose ndi Aroni. Kodi udziŵa cifukwa cake? N’cifukwa cakuti Mose ndi Aroni anakamba kuti iwo adzatulutsa madzi mu cimwala. Koma Yehova ni amene watulutsa madzi. Cifukwa cakuti Mose ndi Aroni sanakambe zoona, Yehova anati adzawalanga. Anawauza kuti: ‘Simudzatsogolela anthu anga kudziko la Kanani.’
Posapita nthawi, Aisiraeli acoka ku Kadesi. Patapita nthawi pang’ono, afika ku phili la Hora. Kumeneku Aroni afela pamwamba pa phili limeneli. Iye wafa ali ndi zaka 123. Aisiraeli ali ndi cisoni cacikulu, cakuti amulila Aroni kwa masiku 30. Eleazara mwana wake akhala mkulu wa ansembe wa mtundu wa Aisiraeli.
Numeri 20:1-13, 22-29; Deuteronomo 29:5.