UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Amene Safuna Kutuluka m’Nyumba
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Kupita patsongolo kwa sayansi ndiponso kuwonjezeka kwa upandu kwapangitsa kuti makamela akauni-uni komaso ma intakomu akhale ofala m’manyumba. Tingacite mantha pofuna kulalikila munthu amene akutiona koma ife sitikumuona. Malangizo otsatilawa adzatithandiza kuti tisamacite mantha kulalikila pa kamela kapena pa intakomu.
MMENE TINGACITILE:
-
Khalani na maganizo oyenela. Anthu ambili amene ali na makamela kapena ma intakomu m’nyumba zawo amakhala na cifuno cokamba nafe.
-
Kumbukilani kuti makamela akauni-uni ene amayanba kujambula masanalize belo n’komwe pageti, ndipo mwininyumba angakhale kuti wakuonani kale komanso kukumvetselani pamene mwafika pamalopo.
-
Pamene mwininyumba wakuyankani, kambani naye pa intakomu kapena pa kamela monga mmene mungakambilane naye mwacindunji. Muzimwetulila na kucita magesica mwacibadwa. Kambani zimene munakonzekela kummuza mukanaonana naye mwacindunji. Ngati pali kamela, musamaiyandikile pafupi kwambili. Ngati mwininyumba sakuyankha, musasiye uthenga.
-
Pambuyo pakuti makambilano atha, kumbukilani kuti mwininyumbayo angapitilizebe kukuyang’anani na kukumvetselani.