AHEBERI 7-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”
7:1-3, 17
Kodi Melekizedeki anaimila Yesu m’njila ziti?
-
7:1—Anali Mfumu komanso Wansembe
-
7:3, 22-25—Palibe paliponse m’Baibo pamene paonetsa kuti iye anacita kuloŵa m’malo munthu wina, kapena pamene paonetsa kuti anali na womuloŵa m’malo
-
7:5, 6, 14-17—Anacita kusankhidwa na Yehova kukhala wansembe, osati kucita kuutengela kwa makolo ake
Kodi unsembe wa Khristu ni wapadela kuposa wa Aroni m’njila yotani? (it-1 1113 ¶4-5)