Yesu Analemekeza Atate Wake
Mu zokamba na zocita zake zonse, Yesu analemekeza Atate wake wakumwamba. Anali kufuna kuti anthu adziŵe kuti uthenga wake unali wocokela kwa Mulungu. Conco, Malemba ndiwo anali maziko a ziphunzitso zake, ndipo kaŵili-kaŵili anali kugwila mau Malemba. Akatamandidwa, Yesu anali kupeleka citamandoco kwa Yehova. Cacikulu kwa iye cinali kukwanilitsa nchito imene Yehova anam’patsa.—Yoh. 17:4.
Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu . . .
-
potsogoza phunzilo la Baibo kapena pophunzitsa pa pulatifomu?
-
pamene anthu ena atitamanda?
-
poganizila mmene tingaseŵenzetsele nthawi yathu?